umodzi womwe khristu anaupemphereranamikangobibleschool.org/uploads/pdfs/umodzi.pdf · umodzi...
TRANSCRIPT
Umodzi 11/29/12
Umodzi Womwe Khristu Anaupempherera
Mawu oyamba: Titha kumadziwa malembo, titha kumabatiza anthu ambiri ndi kukhazikitsa malo a mpingo ochuruka, koma popanda umodzi, ntchito yonseyo sidzapindula kanthu. M’Moyo wathu wathupi wauchimo,
kumakhala kosabvuta kupatukana. Koma mwa Mzimu Woyera wokha ndimo tingathe kusunga umodzi.
Mulungu amafuna mpingo utakhala wolimba ndi wangwiro ndikuti ukafikire ndi kuthandiza mizimu yambiri
yotayika ndi kuibweretsa kwa Yesu.
Cholinga chathu chenicheni mu maphunzirowa ndikufuna kuphunzira za ubwino ndi kufunika kwa umodzi,
kumvetsa zomwe Baibulo limaphunzitsa za umodzi ndinso kuphunzira momwe tingathetsere zolimbana ndi
makangano pakati pathu ndi kukhala amodzi mwa Khristu.
Mutu 1: Umodzi ndi Wofunika Koposa
1. Sanafe, Yesu anapempherera umodzi wa omtsatira ake, kuphatikizirapo ifenso lero lino – Yohane
17:11,20,21. Kodi Yesu amamva bwanji akamaona ife tikugawanika? Nanga muganiza amamva bwanji
akamaona ife tikuonetsa umodzi?
A. Imfa ya Yesu inali pafupi kwambiri. Iye anali ndi kanthawi kochepa kwambiri asanamwalire koti
apemphere. Choncho anayenera kupempherera zinthu zokhazo zomwe zinali zofunikira kwambiri
m’moyo wake. Umodzi chinali chinthu chofunikira kwambiri pa pemphero lake. Yesu anasiya malo
ake aulemu kumwamba ndi cholinga chofuna kupulumutsa dziko lapansi. Iye anagwira ntchito
molimbika pa nthawi ya utumiki wake. Anali atatsala pang’ono kukapereka moyo wake pamtanda.
Yesu sanafune kuti ntchito yake ndi imfa yake kuti ingopita pachabe. Iye anafuna uthenga wake wa
chipulumutso ukhale wopambana padziko lonse.
B. Zikanakhala bwanji ngati ophunzira a Yesu akadapanda kulemekeza pemphero limeneli? Zikadakhala
bwanji ngati wophunzira aliyense akadayambitsa mpingo wake wake wa payekha ndi kupatuka pa
anzake ena onse. Kodi anthu akadakhulupirira uthenga womwe ophunzirawa akadamalalikira? Kodi
muganiza kuti uthenga umenewu bwenzi tikumaumva monga tichitira leromu?
C. Yesu anapemphera “kuti dziko likhulupirire.” Kupatukana kwathu kumatchinjiriza anthu kuti
asakhulupirire uthenga wabwino. Tiyenera kuonetsa mwa kuchita chikondi ndi mtendere womwe
tiulalikira. Kodi muganiza ndi anthu angati omwe akadalandira chipulumutso ngati Akhristu
akadapanda kugawikana?
D. Yesu anati nyumba kapena ufumu uliwonse womwe ugawikana wokha sungaime ayi – Mateyu 12:25.
2. Paulo anafuna kuti Afilipi akhalirane mwa mtendere ndi umodzi kuti awalire dziko lapansi monga kuunika
– Afilipi 2:14-16. Ngati Afilipi aja sakadasunga umodzi, ndiye kuti utumiki wa Paulo pa uthenga wabwino
ukadakhala wopanda phindu. Ngati palibe chikondi ndi mtendere pakati pa Akhristu pamenepo palibenso kuunika.
3. Baibulo limatilamula ife kuti tisunge umodzi pakati pathu – 1 Akorinto 1:10; Aefeso 4:1-6.
A. Umodzi ndi ganizo limene timalipanga. Ndi chinthu chimene timasankha.
B. Umodzi wa Chikhristu sutanthauza kuti tonse tikhale ndi ganizo lofanana pa zinthu zazing’ono
m’Baibulomo. Koma utanthauza kugwirizana mu zikhulupiriro ndi zolinga zazikulu mwa chikondi pa
wina ndi mnzake ndiponso pa otaika.
C. Umodzi wa thupi la Khristu ndi chimodzi mwa zinthu zisanu ndi ziwiri za ziphunzitso zazikulu za
chikhulupiriro cha Chikhristu – Aefeso 4:4-6.
D. Pamene tigawanikana mosasamalira bwino, ndiye kuti sitimvera malamulo a Khristu ndi Atumwi aja.
Umodzi 2
4. Umodzi ndi wofunika kwambiri chifukwa Mulungu amakonda mpingo wake ndi kudana komanso
kuweruza omwe amayambitsa mipatuko – Miyambo 6:16-19; Tito 3:10,11; Aroma 16:17,18.
Sindikondwera pamene wina abvutitsa ndi kupweteka thupi langa. Ndimakwiya pamene wina asokoneza
banja langa ndi kuyambitsa mabvuto. Kugawikana kumaononga ndi kubvulaza thupi la Khristu.
Kumasokoneza ndi kugawanitsa banja la Mulungu. Kugawikana kumapunthwitsa anthu otayika ndipo
kumawalepheretsa kukhulupirira mwa Khristu. Mulungu amawakonda otayikawo. Mulungutu amalikonda banja lake. Choncho chiweruzo chake chimakhala chokhwima kwa omwe amabweretsa kapena kuyambitsa
malekano. Tamvetserani momwe Mulungu amaweruzira nkhani za malekano:
A. Pamene kulimbana ndikugawanikana kubwera mu mpingo, Akhristu ambiri amapwetekedwa mumtima
kapena kusowa mtendere wa mtima ndipo kenako amasiya kutsatira Yesu. Yesutu anatichenjeza kuti
tisachite zinthu zomwe zingachimwitse anthu ndi kuwapangitsa kusiya kumvera Khristu.
Ngati wina apangitsa mmodzi wa aang’ono awa omwe amakhulupirira ine kuti achimwe, kukanakhala
bwino kuti woteroyo akolekedwe mkhosi mwake ndi mwala wamphero waukulu ndiumizidwa m'nyanja
yakuya kwambiri. Tsoka dziko lapansi chifukwa cha zinthu zomwe zichimwitsa anthu! Ngati dzanja
lako kapena phazi lako likuchimwitsa ndi bwino kulidula ndi kulitaya. Pakuti kuli bwino kulowa
m’moyo wopunduka kapena wopanda dzanja kapena phazi koposa kuponyedwa m'moto wa nthawi
zonse uli ndi manja kapena mapazi awiri. Ndipo ngati diso lako likuchimwitsa, likolowole ndi kulitaya.
Kuli bwino kwa iwe kulowa m'moyo ndi diso limodzi koposa kukhala ndi maso awiri ndi kuponyedwa
m’gehena wa moto – Mateyu 18:6-9.
B. Mulungu adzaononga iwo omwe adzaononge kachisi wake. Paulo analemba za anthu omwe anaononga
mpingo, kachisi wa Mulungu, poyambitsa mipatuko.
Kodi simudziwa kuti inu ndinu kachisi wa Mulungu ndikuti Mzimu wa Mulungu akhala mwa inu? Ngati
wina aliyense awononga kachisi wa Mulungu, Mulungunso adzamuononga popeza kachisi wa Mulungu
ndiwopatulika ndipo inu ndinu kachisiyo – 1 Akorinto 3:16,17.
Ngati tilimbana ndi kumagawanikana moona osapembedza ndiye kuti tikukana uthenga wabwino womwe
tiulalika. Ngati timakondana, ndiye kuti anthu onse adzadziwa kuti ndifedi ophunzira a Khristu. Palibe chinthu
chomwe chimaphwanya ndikuononga ntchito ya uthenga wabwino koposa malekano athu. Kodi muganiza
dziko lathuli likadakhala lotani lero ngati Akhristu onse pamodzi akadakhala amodzi ndi ogwirizana ndi
kumalalikira uthenga wabwino ndi mphamvu zonse?
Mafunso okambirana: � Nchifukwa chiyani timangolimbikira pa ziphunzitso zina koposa momwe tichitira pa chiphunzitso cha
umodzi?
� Tafotokozani momwe kugawanikana kwalepheretsa ndi kutchinjirizira uthenga wabwino m’dera lanu.
� Tafotokozani momwe umodzi wolimbikitsira ulaliki wa uthenga wabwino m'chigawo kapena dera lanu.
Mutu 2 - Zomwe Baibulo Linena pa za Chiphunzitso cha Umodzi.
Mawu oyamba: Baibulo lonse limaphunzitsa za umodzi. Mulungu adalenga mwamuna ndi mkazi ndipo anati
iwo akhale thupi limodzi (Genesis 2). Ndipo Yesu adati, ”Chomwe Mulungu wa chimanga, munthu
asachilekanitse” – Mateyu (. Abrahamu anati kwa Loti “Pasakhale kukangana pakati pa iwe ndi ine, pakuti tiri
abale” – Genesis 13. Pamene Kora, Datani ndi Abrahamu anayeserera kugawa Israyeli pogalukira Mose ndi
Aroni, Mulungu anang’amba nthaka ndipo onse ogalukirawo anamezedwa pomwepo. Davide analemba kuti
“Zimakhala zosangalatsa kwambiri pamene abale akhala pamodzi mwa umodzi!” – Masalmo 133. Umodzi wa
thupi la Yesu ndi chiphunzitso chofunikira kwambiri cha m’Chipangano Chatsopano. Tiyenera kumvera
chiphunzitso chimenechi. Ngati timakhulupirira ndi kuphunzitsa ziphunzitso zinanso za m’Chipangano
Chatsopano, tiyeneranso kukhulupirira ndi kuphunzitsa chiphunzitso cha umodzi.
1. M’Chipangano Chatsopano, umodzi uli ndi maziko awiri, maziko a uzimu ndi maziko a chiphunzitso.
Umodzi 3
A. Pa Aefeso 4:1-3 timawerenga za umodzi wokhazikika pamaziko auzimu.
Monga wamndende wa Ambuye, ndi kudandaulirani ine tsopano, kuti muyende molingana ndi
moyenera maitanidwe omwe unaitanidwa n awo, ndipo onetsetsani kuti mukudzichepetsa
ndiponso muli ofatsa; khalani opirira; ololerana wina ndi mnzake mwachikondi. Samalirani
kwambiri poonetsetsa kuti mukusunga umodzi wa mzimu podzimangirira pa mtendere nthawi zonse.
Umodzitu ndi wa Mzimu. Kudzichepetsa monga Khristu ndiko kumachititsa kuti umodzi utheke.
Chilengedwe chathu chathupi cholakwa chimakonda moyo wopatukana. Tawerengani mndandanda wa
“ntchito za thupi” mu Agalatiya 5:19-21. Mukuona kuti madano, ndeu, kaduka, zopsa mtima,
kukhumba zonyansa, zotetana, magawano, mipatuko ndi njiru zaikidwa mu gulu limodzi ndi chigololo,
kuledzera ndi nyanga. Theka la machimo omwe atchulidwa mu mndandanda umenewu amapezeka
pafupifupi m'malekano a mumpingo uliwonse, ndi mukulekana kwa banja liri lonse. Koma tawerengani
mndandanda wa “chipatso cha mzimu mu Agalatiya 5:22,23. Umodzi umakhala wosavuta ngati anthu
akhala otere.
Popanda chipatso cha Mzimu Woyera, chimene chimagonjetsa khalidwe lakale ndi kusintha ife kuti
tifanane Khristu, sitingathe kusunga umodzi. Ngakhale tigwirizane ndi ziphunzitso zonse, koma
khalidwe lathu la kudzikonda lidzapezabe njira ya kutilekanitsa ngati tikuyenda m’thupi. Makolo a
gulu la chibwezero, limene Mpingo wa Khristu mmene tiri kukhalamo lero, anayetsetsa kugwirizanitsa
okhulupirira malembo. Anatisonyeza ife mmene tingagwirizanirane mwa ziphunzitso zenizeni za
Baibulo. Koma sanaphunzitse zambiri za malekano ochitidwa mwa uzimu. Koma tiyenera kuphunzira.
B. Mu Aefeso 4:4-6 Paulo ali kutipatsa ife madziko a chiphunzitso cha umodzi. Watchula ziphunzitso
zazikulu zisanu ndi ziwiri zimene tiyenera kuzikhulupirira m’malo mwakuti tikhale amodzi.
Pali thupi limodzi ndi Mzimu mmodzi—monga momwe munaitanidwa ku chiyembekezo
chimodzi pamene munaitanidwa—Ambuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi;
Mulungu mmodzi ndi Atate wa onse, amene ali pamwamba pa onse ndi mwa onse ndi mkati
mwa zonse.
Tafanizirani 1 Akorinto 15:1-8 pamene Paulo waika mndandanda wa zinthu zofunika kwambiri mu
uthengamo.
Pakuti chimene ndinalandira ndinapereka kwa inu monga chofunika choyambirira: kuti
Khristu anafera zoipa zathu monga mwa malembo, ndikuti anaikidwa, ndikuti anauka pa tsiku lachitatu monga mwa malembo, ndi kuti anaonekera kwa Petro, ndi kwa khumi ndi awiriwa.
Izi ndi zoonadi zolimba zimene zitipanga ife kukhala monga momwe tiri. Chotsani ngakhale chimodzi
mwa izo ndipo sitingakhalenso mpingo wa Ambuye. Tiyenera kulandira zonsezo m’malo mwakuti
tikhale amodzi ndi kulandirana wina ndi mnzake. Tiribe ufulu wakugwirizana ndi wina aliyense
wokana ngakhale chimodzi mwa zoonadi zimenezi. Sitingathenso kusiya chimodzi mwa zoonadi
zimenezi m’malo mwakuti tisunge umodzi.
Malembonso akuphunzitsa kuti sitingakhale amodzi ndi Akhristu amene achita mitundu ya uchimo
yoipa ndipo sakulapa – 1 Akorinto 5; Mateyu 16:15-20; Aroma 16:17,18.
2. Umodzi wakhazikika pa chisomo. Tiri amodzi ndi Mulungu pachifukwa cha chikhululukiro cha chisomo
chake. Tiri amodzi ndi Iye osati chifukwa ife tiri olungama koma chifukwa zochimwa zathu zakutidwa ndi
mwazi wa Khristu. M’njira yomweyo, tiri amodzi wina ndi mnzake kupyolera m’chisomo ndi
chikhululukiro.
Mulandirane wina ndi mnzake, monga momwe Khristu anakulandirani inu, m’malo mwakuti tichitire
Mulungu ulemu. – Aroma 15:7.
Mulungu anatilandira ife monga anthu osakonzeka, ndipo momwemonso ife tilandirane wina ndi mnzake
monganso anthu osakonzeka.
Umodzi 4
Monga momwe ndakukonderani inu, inunso mukondane wina ndi mnzake – Yohane 13:34.
Yesu anatikonda ngakhale tinali wochimwa koteronso tikondane wina ndi mnzake. Umodzitu umadalira
chisomo. Mulungu watipatsa ife malamulo ena ndipo tiyenera kuwalemekeza. Komatu nkhani ya
Chikhristu simalamulo ayi. Koma ndi nkhani ya chikondi, ubale wokhulupirika ndi Mulungu. Kulekana
kwakukulu pakati pa Chikhristu ndi zipembedzo zina zonse kuli pa chisomo. Mulungu adzatiweruza popanda chifundo ngati tiribe chifundo pa ubale wathu ndi anzathu. – Yakobo 2:13.
A. Taonani kuti pali ziphunzitso zina zofunika kwambiri zomwe tonse tiyenera kudzikhulupirira ndipo
ngati tipanda kutero sikungatheke kuti tikhale amodzi – Aefeso 4:4-6; 1 Akorinto 15:3-8; 5:1-13.
Tiyenera kupatuka pa wina aliyense yemwe akana ziphunzitso zofunikirazi.
B. Komanso Baibulo limafotokozera ndi kuzindikiritsa kuti alipo magawo ena ndi nkhani zina
zazing’ono zomwe Akhristu okhulupirika ndi oona angathe kumva mosiyana ndikutsatira mosiyana
komabe nakhala amodzi mu mtendere ndi Mulungu, wina ndi mnzake – Aroma 14. Ichitu ndi
chiphunzitso chofunikira koposa chomwe Baibulo liphunzitsa za umodzi.
1) Yesu amati pali malamulo ena omwe amakhala ofunikira kuposanso ena – Mateyu 23:23; 22:35-
40; 40:19. Tiyenera kumasamalira malamulo ena onse koma ena ndi ofunika kuwasamalira
kwambiri chifukwa ali ndi maziko osiyana ndi ena.
2) Ziphunzitso zina zomamveka bwino ndimalemba ake koma zina zimakhala zovuta kumvetsa
kwake – 2 Petro 3:16. Ziphunzitso zomwe zimakhudza chipulumutso chathu zimakhala zomveka
mosavuta. Nkhani zomwe ziri zovuta kutanthauzira kwake kapena kumvetsa, nkhani zomwe
zimadalira kwambiri pa umunthu wathu wolephera ndi nzeru zathu za umunthu sizingakhale
nkhani za chipulumutso kapena zifukwa zoti tilekane.
3) Malamulo ena a m’malembo amangokhala ndi cholinga chofuna kufotokozera tanthauzo lokhala
Mkhristu ndi mwana wa Mulungu. Malamulo ena amangokhudzidwa ndi nkhani zazing’ono ndi
zosakhala zakuya kwenikweni. Ziphunzitso za chikondi, ndi chikhulupiriro ndi kukhulupirika ndi
zomwe ziri zotumikira koposa ziphunzitso zofotokozera za dongosolo la chipembedzo.
Kulakwitsa moona pa zakutalika kwa tsitsi lamkazi sikuli kuopsa kwambiri monga zingaopsere
ngati munthu sakhulupirira za “kuuka”. Afarisi anali otanganidwa ndi okhudzidwa kwambiri ndi
zinthu zooneka kunja kwa thupi ndi mtima monga za miyambo yosiyanasiyana ndi kusamba
munthawi zokonzedwa. Yesu anawasonyeza malemba oti, “ndifuna chifundo, osati nsembe ayi –
Mateyu 12:1-7; 9:10-13.
4) Mulungu amadziwa kuti popeza tiri nako kufooka kwathu kwa umunthu, ndiponso chifukwa
choti tonse sitiri okhwima m’chikhulupiriro, sitingathe kuona bwinobwino, ndimvetsa bwino
mawu ake. Munkhani zoterozo, iye amangotipatsa mwa chisomo chake ndipo amatilamula ife
kuti tiwachitirenso anzathu zomwezo – Aroma 14:1-15; 7. Izi zimakhudzanso nkhani zomwe
timakhulupirira ndi kuzolowera kuchita m’mipingo mwathu. Pamene tidzapita kumwamba
tidzatulukira kuti tonse tidalakwitsa m'zinthu zina zazing’ono zing’ono zomwe tidazikhulupirira.
Palibe ndi mmodzi yemwe amamvetsa bwino ndi kumvera malembo onse mwachindunji. Nkhani
ndi yoti tiri opulumutsidwa mwa chisomo.
Nkhani zambiri zomwe timalimbana nazo ndi kumakanganira mpaka kumagawanikana nazo
mumpingo sinkhani za chipulumutso konse. Koma umodzi ndi nkhani ya chipulumutso. Ichi ndi
chiphunzitso chofunikira zedi. Komabe palinso choonadi chomwe Baibulo limafotokoza pa za
umodzi chomwe anthu ambiri satha kuchimvetsa. Zitsanzo:
(a) Sitiri oyenera ngakhale kulandira mbale wofooka, womangiririka zinthu zazing’ono
zoti tingathe kuchita nazo kapena osachita nazo.
(b) Akhristu omwe ali a maganizo awiri osiyana pa nkhani zimenezi, angathe kukhala nafe
pamodzibe ngakhale mmodzi wa iwo ali wolakwa. Ichi chitanthauza kuti mu nkhani
Umodzi 5
zomwe mpata umakhalapo pakati pa abale okhulupirika kuti akhale ndi maganizo
olekana pa nkhani zina, sizingakhale nkhani za chipulumutso ayi.
(c) Pamene mbale asiyana ndi ine pa momwe titanthauzira malembo, sichitanthauza kuti
iyeyo saopa Mulungu kapena akuyesetsa kusamvera
Mulungu mwa muyezo uliwonse.
(d) Lamulo la Paulo mu Aroma 14 loti tilorerane limakhudza zambiri zoposa khalidwe
lakelake la munthu. Kukhulupirira masiku oyera ndi opatulika kunakhudzanso
misonkhano ya mipingo zochitika chitika pa nthawi ya chipembedzo.
(e) Mbale amene ali womangiridwa ku chikumbumtima chake yemwe amaweruza mbale
wake “pochita zoipa” akubweretsa magawano chimodzimodzi monga momwe mbale
yemwe achita zomwe zikhumudwitsa ubale wake womangiririka ku chikumbumtima
chake uja. M’mbuyomo takhala tikutsutsa yemwe amayambitsa zinthu zatsopano
monga woyambitsa mipatuko. Uku kunali kulakwa. Mu Aroma 14 sitiphunzira motero.
5) Pamene tiwerenga bwino ndi kumvetsa bwino Aroma 14,15 timaloledwa kukhalabe amodzi
ngakhale pali nkhani zina zazing’ono zomwe tikulephera kumva mofanana. Choncho ndi
malembo amenewa titha kuona ndi kumvetsa bwino nkhani imeneyi kuti:
a.) Mulungu amatilamulira kuti tipitirirebe kugwira ntchito pamodzi chifukwa cha nkhani
zofunikira kwambiri zomwe timazimva mofanana ndi kusiya zina zazing’onozing’ono
zomwe tingathe kuchita popanda izozo kuti Mulungu ndiye aweruze.
b.) Ndingathe kugwiri ntchito ndi abale ena mumpingo ngakhale pali zina zomwe
sitizimva mofanana pa mfundo zina zomwe iwo achita ndi kukhulupirira.
c.) Nkhani itha kukhala ndi magawo abwino ndi oipa ngakhale ndiikulupirira koposa.
Ngati pafika poti kumasulira kwa umunthu wathu wooka kugwiritsidwa ntchito
nkutheka kuti nditha kukhala wolakwa m’chikhulupiriro changa.
C. Makolo athu akale pa nthawi yawo yobwezeretsa anasonkhanitsa chiphunzitso cha m'Chipangano
Chatsopano cha umodzi m’mawu oti, “M’chikhulupiriro, umodzi; malingaliro, ufulu; m'zonse,
chikondi."
D. Ngakhale kulekana kwina ndi kofunika chifukwa kumakhudza za ziphunzitso zofunikira, nthawi zambiri kulekana kumakhalapo chifukwa sitimvetsa zomwe Baibulo limaphunzitsa za chisomo.
1) Chisomo ndi choonadi siziri zinthu zotsutsana china ndi chinzake ayi. Zonsezi zimagwirizana
ntchito yofotokozera za khalidwe ndi moyo wa Yesu – Yohane 1:14. Yesu anasakaniza chisomo
chopusa ndi kuleza, pamodzi kukhudzidwa koposa kwa choonadi.
2) Paulo anawauza Akhristu kuti “simuli pansi pa lamulo koma pansi pa chisomo.” – Aroma 6:14.
Anthu powerenga mawu amenewa amaganiza kuti chisomocho chimatanthauza kuti azichita ziri
zonse zomwe zingawakomere koma Paulo akukanitsitsa zimenezi. Sitiyenera kumaopa momwe
chisomo chingakhudzire kumvera kwa pachoonadi. Chisomo nthawi zonse chimapereka kumvera
kwakukulu kuposa chilamulo chomwe chimangotsamira pa zowerengeka za malamulo akunja kwa
thupi ndi mtima. Chisomotu chimasintha mitima yathu ndipo chimatipangitsa kukhala omafuna
kukondweretsa Mulungu.
3) Pamene tiwalandira iwo amene tisiyana nawo maganizo pa nkhani zina zazing’ono sikutanthauza
kuti tikugwirizana ndi zomwe tikuona ngati iwo akulakwitsa ayi. Sizitanthauza kuti tasiya kumvera
lemba la m’Baibulo ndi limodzi lomwe. Tiyenera kumakhala osamalira kwambiri potsatira
maganizo athu m’makhalidwe athu ndi kumaphunzitsa ena zomwe tikukhulupirira kuti ndi zomwe
malemba akutanthauza.
Umodzi 6
Koma ngati sakumvetsabe chomwe tikutanthauza pa nkhani yomwe tikuwauzayo ngati iri
yaing’ono, tiyeni tipitirezebe kuwakonda ndi kugwira nawo ntchito pamodzi. Mu Aroma 14
timamva kuti tiyenera kusiyira Mulungu kuti aweruze nkhani zina zomwe ife talephera.
Kusunga umodzi pakati pathu ndi omwe tisiyana nawo maganizo ndi lamulonso pa lokha, ndi
chinthu choyenera kuchikhulupirira, ndi gawo la chiphunzitso cha Chipangano Chatsopano.
Baibulo limatiphunzitsa kuti anthu onse, kuphatikizapo akulu ampingo angathe ndipo ayenera kumagwira ntchito pamodzi, ndipo sikuti zingatheke kuti azikhala ofanana m’maganizo pa mfundo
zonse angakumana nazo. Mpingo ungathe kukula koposa anthu zana limodzi (100) popanda
kulekana maganizo. Koma kuti izi zitheke, pamafunika kuti tikhale ndi luso lozindikira msanga
nkhani zoti titha kulolerana popeza ndi zazing’ono.
Mutu 3: Zoyambitsa Kulekana.
Nthawi zina m’mudzi mumagwa mliri. Anthu amavutika ndipo ena amafa. Madotolo ndi akatswiri ena
amabwera kuti afufuze choyambitsa kapena chomwe chikufalitsa matendawo. Pamene atulukira ndi kumvetsa
bwino gwero la matendawo, ndi pomwe angathe kuthetsa matendawo ndi kuwatchinjirizanso. Momwemonso
ngati timvetsa bwino chomwe chimayambitsa kapena komwe kumachokera moyo wolekana, ndi pomwe
tingathe kuchiza ndi kutchinjiriza bvuto limeneli. Malingana ndi malemba, zoyambitsa kulekana zina ndi:-
1. Kukana kukhulupirira zinthu zofunikira kwambiri ndi malamulo a m’Baibulo.
A. Yohane analemba kuti Akhristu asamalandire m’nyumba zawo aphunzitsi omwe ankati Yesu
sanabwera monga munthu wathupi – 1 Yohane 2:22,23; 4:1-3; 2 Yohane 7-11; tawerengani ndipo
mufanizire 1 Akorinto 13:3; Aefeso 4:4-6; 1 Akorinto 15:3,4; 5:1-13.
B. Mulungu satitsutsa ife ngati tidzilekanitsa kwa aphunzitsi onyenga oterewa. Tiri oyenera kupatuka pa
amenewa.
2. Moyo wathu wauchimo “thupi” – Agalatiya 5:19-21; 3 Yohane 9,10. Timanena kuti kupatukana kwathu
sikuli koyipa chifukwa tichita zomwe malembo anena, koma zoona ndi zoti nthawi zambiri nkhani
imakhala yokanganira ukulu ndi mphamvu, kapena nthawi zina kuwawirana mtima ndi kusakhululukirana
chabe.
3. Kukonda kuchititsana makani pa zinthu zopanda pake ndi zosamveka – 1 Timoteo 1:3-7; 4:7; 6:3-5,20,21;
2 Timoteo 2:15-17,23-26; 4:3,4; Tito 1:10-15; 3:9-11.
4. Kusamvetsa bwino zomwe Baibulo liphunzitsa za umodzi – kapena za umodzi weniweni womwe Baibulo
limafotokoza – Aefeso 4:16; Aroma 14:1-15; 7
5. Kukulitsa ndi kulemekeza zinthu zina koposa Khristu ndi mtanda – 1 Akorinto 1:10 – 4:1. Anthu a ku
Korinto anagawanikana chifukwa anakhulupirira ndikutsatira kwambiri alaliki koposa Yesu Khristu. Ife
mwina tikhoza kumakhulupirira kwambiri ndi kutamanda koposa mlaliki wodziwa kuyankhula bwino,
mphunzitsi mwanzeru, dzina, nyumba, chiphunzitso, kapena mwambo. Zonse ndi zomwe zimalekanitsa
Akhristu, (Paulo adati Akorinto anayenera kukhala nalo gulu lomwe ankadziwika nalo kuti aonetse ndi uti
anali wobvomerezeka kwa Mulungu – 1 Akorinto 11:9). Chirichonse (ngakhale chiphunzitso) chomwe
chimalowetsedwa m’malo mwa Khristu monga nkhani yaikulu, chimakhala fano
6. Kukhulupirira malamulo, kukhulupirira kuti timalandira chipulumutso mwa zintchito zabwino zomwe
tichita koposa chisomo cha mtanda.
Moyo wathu wauchimo wathupi, nthawi zonse umafuna kutenga dongosolo la uthenga wa chisomo ndi
kuusandutsa kuti ukhale monga lamulo chabe, dongosolo lomwe anthu amalandira chipulumutso chifukwa
chotsatira malamulo chabe. Izitu zinawachitikira ena aja a mumpingo woyamba uja. Taonani Machitidwe
15 ndinso kalata ya kwa Agalatiya. Ndipo zakhala zikuchitikanso mumpingo mu mazana mazana a zaka
kuyambira munthawi ya atumwi. Anthu omwe amalimbana ati pofuna kuteteza dongosolo la malamulo,
nthawi zambiri amalakwitsa poganiza kuti, malinga ndi chikhulupiriro chawo, iwo amachita zimenezi
pofuna kuvutikira uthenga wabwino ndi chikhulupiriro cha Chikhristu, komanso ati amachita zimenezi
polimbikitsa uthenga wabwino ndi Chikhristu.
Umodzi 7
A. Chipangano Chatsopano chimaphunzitsa kuti palibe yemwe angalandire chipulumutso chifukwa
chosunga lamulo,, chifukwa palibe ndi mmodzi yemwe, amene amasunga malamulo mwachindunji ndi
mosamala. Tonse tinachimwa ndipo taperewera mu ulemerero wa Mulungu, komabe timawerengedwa
olungama chifukwa Yesu analipira machimo athu ndi mwazi wake pa mtanda – Aroma 3:20-28.
B. Kufananiza pakati pa kuweruzidwa mwa lamulo ndi kuweruzidwa mwa chisomo
Kuyeretsedwa mwa Lamulo Kuyeretsedwa mwa Chisomo
Zochita zathu za ife eni Zochitidwa ndi Mulungu
Kudalira pa ntchito zabwino - Kudalira ntchito yomwe Yesu anachita
Agalatiya 3:10; Yakobo 2:10.
Kuchita bwino kwa ife eni. Kuchita bwino kochokera kwa Mulungu.
Kutukumuka chifukwa chochita bwino Kukweza ndi kulemekeza Mulungu
Kulandira chipulumutso “chomwe- Chipulumutso mphatso yomwe Mulungu ayenera
kutipatsa” sitinali oyenera kuilandira.
Ukapolo Ufulu
Kukhudza zolembedwa zokhazo basi Kukhudza mzimu ndi maganizo amkati.
Mwa zintchito, zochitika Mwa chikhulupiriro
Kuchita bwino chifukwa cholamulidwa- Kuchita bwino chifukwa moyo wathu watsopano
ufuna kutero.
Kungochita ndikutsata zingapo zoti- Kuchita zonse zabwino zomwe tingathe
zomwe tifuna.
Onse analephera Onse angalandire.
C. Komabe anthu ena amaganizirabe kuti adzalandira chipulumutso posunga bwino malamulo a Mulungu.
Mwa chilengedwe chathu, mipatuko imabadwa chifukwa chotsamira pa malamulo. Taonani zina za
zinthu zomwe munthu wotsamira pa malamulo amachita:
1) Amasankha ena a malamulo a milungu yomwe ndi yodziwika ndi yokondedwa ndi iyeyo kapena
ziphunzitso zina za malembo ndi kuzigwiritsa ntchito monga muyezo woonera chikhulupiriro
koma panthawi yomweyo akutaya ndi kuiwala malamulo ambiri a Mulungu ndi ziphunzitso
zomwe (makamaka zamkati mwa mtima ndi za uzimu).
2) Amawatenga onse omwe amasamala bwino malamulo omwe iye anawasankhawa monga
olungama ndi okhulupirika kwa Mulungu ndipo ena onse omwe sasunga zimenezi monga
“olakwa” Ichi chitanthauza kuti iwowa amene ali “olungama ndi okhulupirikawa”, sali olakwa.
Alibe tchimo. Izi zimaonetsa kulakwitsa posasamala mfundo yoti tonse timalephera kumvera
Mulungu m'zinthu zambiri chifukwa cha kusadziwa kapena kufooka, ndipo onse ayenera kudalira
chisomo.
3) Amalimbikira pa malamulo oyang’ana zakunja kwa thupi ndi kumvera kwake kopanda ungwiro
koposa malamulo amkati mwa mtima ndi kumvera kwa mkatikati kwa Mulungu.
4) Amakhazikitsa maganizo ambirimbiri a anthu ndi miyambo ya anthu monga malamulo ena
owonjezedwa pa malamulo a Mulungu – Taonani Mateyu 15:1-20. Ngati munthu ali wotetezeka
ndi kusunga malamulo kwake koposa chisomo, pamenepa, iye amaona kuti zingamuyendere
bwino ngati aonjezerabe malamulo ena awiri atatu monga linga lomuteteza, m’malo mongotsata
Umodzi 8
ndi kuchita zinthu momveka bwino monga momwe malemba afotokozera. Miyambo ina
imaonjezeredwa ndi cholinga choti zioneke zoonadi. Ichitu ndi chifukwa chake mipingo ina
ipezeka kuti nthawi zonse ikulekana pa mfundo zina zatsopano.
5) Amalimbikira za mgwirizano wathu ndi malamulo koposa mgwirizano wathu ndi Mulungu
yemwe anapereka malamulowo. Akhristu otsamira kwambiri pa malamulo nthawi zambiri amakhala ofooka pa momwe iwo eni ayendera ndi Mulungu.
D. Nchifukwa chiyani moyo wathu wauchimo umakonda kutsatira ndi kusamala malamulo koposa
chisomo?
1) Titha kukhala ndi chipembedzo cholamulidwa ndi ife eni, chokhala ndi dongosolo
lomangoyang’ana ndi kutsamira pa mndandanda wa malamulo osankhika ndi ziphunzitso
zokonzedwa. (Pamene munthu ali pa ubale iye ndi Mulungu, zinthu sizikhala pansi pa
ulamuliro wake ayi; Mulungu amatitengerabe ife nthawi zoti zomayeserera ndi kuchita
chifuniro chake ku miyoyo yathu.
2) Kudalira pa malamulo kumatipatsa moyo wodzitcha apamwamba. Ife tiri okhulupirika ndi
omvera ndipo enawo ali olakwa – tafanizirani ndi mawu opezeka pa Luka 18:9-14.
3) Zimatipangitsa kuti tidzinyenge tokha poganiza kuti tiri otetezeka. Popeza tikungoyang'ana pa
zofunikira za Mulungu zowerengeka chabe osati pa zofuna zake zonse, timaona ngati tikuchita
bwino pa kumvera.
4) Timangolimbikira kuchita zinthu zingapo zoonekera kunja mokhoza (kapena kungosunga
ziphunzitso zingapo chabe zolondola), osati kusinthika kwa mitima yathu (ntchito ya pamoyo
wathu wonse yotheka chifukwa cha thandizo la chisomo cha Mulungu chokha basi).
5) Pamene tiri pansi pa ulamuliro wa chilamulo timakhala ndi lamulo lochitira chiri chonse ndipo
sitisowanso kuvutika ndi kuganiza. Pamene kwa munthu yemwe ali pansi pa chisomo ayenera
kugwiritsa ntchito mfundo zauzimu pofuna kuyankha Mafunso ambiri omwe malembo
sanafotokozere mwatchutchutchu, ndipo izi zimafunika kuti ife tikhale olimba ndi oganiza
mozama kwambiri.
6) Ndi kosabvuta kusamalira dongosolo la malamulo koposa kusamalira Mulungu amoyo ndi
woopsa.
E. Zoopsya Zapadera Zodalira Malamulo
1) Zimatamanda kuchita bwino kwa ife eni ndi kumvetsa kwathu ndi kuchotsa chitamandochi
kwa mwini wake Yesu ndi mtanda – taonani 1 Akorinto 1:31; 2:2.
2) Zimatipangitsa kukhala otukumuka ndi onyada m’malo mokhala odzichepetsa. Timakhala
okonzekera kuweruza ndikutsutsa anzathu enanso.
3) Zimabereka kugawikana kosiyanasiyana m’thupi la Khristu, kusokoneza pemphero la Ambuye
wathu lija la Umodzi. Umodzi pakati pa anthu operewera pa ufumu wa Mulungu umatheka
mwa chisomo.
4) Zimalinganitsa maganizo athu aumunthu ndi chikhalidwe chathu malamulo a Mulungu ndipo
potero zmatipangitsa kuti kupembedza kwathu kwa Mulungu kusakhale kobvomerezeka –
Mateyu 15:1-20.
5) Zimatipatsa nthawi yoti tidzinyengeka poganiza kuti ndifedi omvera Mulungu, potsamira
kwambiri pa malamulo pang’ono osankhidwa mosaganizira bwino. (Kodi ndi chiyani chomwe
chimapangitsa kuti malamulo ochepa amenewa akhale ofunika kuposa ena onsewo? Kodi ndi
Umodzi 9
chiyani chimapangitsa kuti nkhani zina za ziphunzitso zikhale ndi mphamvu koposa malamulo
ake amkatikati mwake?)
6) Zimanyalanyaza malamulo a Mulungu pa za mtima ndi mzimu, ndipo amakhala wokhutitsidwa
ndi kungomvera lamulo Lolembedwa popanda kuganizira mzimu ndi cholinga cha lamulolo.
7) Timangodzidalira tokha m’malo modalira Mulungu.
8) Timalowetsa ubale wathu ku malamulo angapo omwe timawasankha m’malo molimbikitsa
ubale ndi Mulungu. Timadziwa zambiri za malamulo koposa Mulungu yemwe anapereka
malamulowo.
9) Pali malamulo ena omwe timawakonda ndi kuwazolowera ndi maganizo ena, ngakhale akhale
abwino powagwiritsa ntchito monga mwa cholinga cha Mulungu. Amasanduka mafano kwa ife
chifukwa amalowa m’malo mwa Ambuye ndi mtanda wa Khristu pa ziphunzitso zathu. Palibe
lamulo kapena chiphunzitso chomwe chingakhale ndi tanthauzo ngati chiri chongodziimira
pachokha pambali pa Umbuye wa Khristu.
10) Kudalira ndi kutsamira pa malamulo kumabvala kumvera koperewera kwa Mulungu chifukwa
kumanyalanyazitsa malamulo ambiri a Mulungu ndipo amangotsala ochepa okha, chifukwa
kumanyalanyazitsa nkhani za mkatikati za kumvera ndi kulemekeza zakunja zooneka ndi
maso. Mwa chisomo, wokhulupirira amakhala wotengeka pomvera Mulungu chifukwa iye
amachita ichi pobvomereza chikondi cha mtanda, ubale wake wa iye ndi Ambuye wake.
11) Zikapitirira, kutsamira pa malamulo kumadzapherezera potilekanitsa ife ndi chisomo cha
Mulungu. “Inu amene muyetsedwa olungama ndi lamulo, mulibe kanthu popeza
munasiyanitsidwa ndi Khristu; Mudagwa posiyana nacho chisomo” – Agalatiya 5:4.
Simungathe kukhulupirira ntchito zonse za Khristu ngati mukhulupirira kwambiri pa kuchita
bwino kwanu kwa inu eni kapena kulungama kwanu. Ntchito ya kukhululukira ndi kuombola
inachitika chifukwa cha ochimwa, osati chifukwa cha iwo ali angwiro.
Komatu zonsezi sizitanthauza kuti Mulungu alibe nafe ntchito kapena kuti kumvera kwathu kuli
kosafunika. Cholinga chenicheni cha chisomo ndicho chofuna kukhazikitsa mwa ife moyo wodzadza
ndi kumvera koposaposa. Monga momwe mkulu wina ananenera, “Mulungu amakukondani monga
momwe muliri komatu amakukondani koposa kotero kuti sangathe kukusiyani pomwe muliripo.”
Mutu 4: Umodzi Pakati pa Ogwira Ntchito
Gawo loyamba: Kusunga Ubale Wabwino.
Mawu oyamba: Satana amafuna kugawanitsa ndi kudanitsa anthu. Amafetsa kuwawirana mtima ndi udani.
Khristu amafuna kuyanjanitsa ndi kugwirizanitsa anthu. Iye amafetsa mtendere ndi chikondi. Anthu nthawi
zonse adzakhala ndi maganizo olekana ndi makangano. Ngati zimenezi tingozilekerera osaziperera njira
yokonza, zimakwaniritsa zolinga za Satana. Maganizo a Yesu angathe kuthetsa kulekana kwa maganizo pakati
pa anthu ndi kugwetsa malinga olekanitsa mabanja, mipingo, achinansi, kuntchito kapena maubale ena
osiyanasiyana. Yesu watipatsa mfundo zomwe zingathe kuchiza ndi kubwezeretsa ubale woonongeka. Tiyeni
tione komwe makangano amachokera ndi chomwe tingachite pa nkhani imeneyi.
1. Muzu weniweni wa kulimbana ndi kulakwirana pakati pa anthu ndi kunyada ndi kudzikonda – Mateyu
18:1-5.
A. Bvuto: Tonse timafuna kudziwa kuti “Kodi wamkulu ndani?” (wopambana, mpondamatiki, wokhoza,
wodzisamala, wosiririka, wokondedwa, wa ulamuliro woposa ndi zina zotero). Ngati nthawi zonse
ndi mangoganizira za ine ndekha, ndiye kuti kulimbana ndi enawo kuyenera kuyambika nthawi ina
iriyonse.
B. Kuthetsa kwake: Kukhala wakufa kuthupi” – Agalatiya 2:20.
Umodzi 10
1) Mateyu 18:3,4 – Mudzione ngati kamwana kakang’ono podzifanizira ndi ena.
2) Afilipi 2:5-8 – Kutaya ulemu ndi ufulu wanu mwakufuna kwanu.
3) Aefeso 5:21 – Kumverana chifukwa choopa ndi kulemekeza Khristu.
4) Afilipi 2:3,4 – Muwatenge ena onse monga ofunikira koposa inu.
5) Yohane 13:3-17 – Sambitsanani mapazi anu.
2. Sitingathe kubwezeretsa ubale womwe taononga – Mateyu 18:6.
A. Malipiro kwa olakwayo:
1) “Kuli bwino amizidwe m’nyanja yakuya.”
2) Mulungu sadzamva pemphero lake – Mateyu 5:23,24; Ahebri 12:14.
B. Mtengo kwa ena onse okhudzidwa.
1) Abale apabanja – kuwawidwa
2) Mpingo – kupatukana
3) Osakhulupirira - kukanidwa – Yohane 17:20,21; Afilipi 2:14-16.
C. Musalole kukhala woyambitsa udani kapena kukana kuthetsa zolimbana – Aroma 12:18.
1) Konzani msanga tolakwika ting’ono-ting’ono pa ubale wanu madzi asanafike mkhosi.
2) Pezani njira zothandiza kuti mukonze ubale molumikizana.
3) Limbikirani kuonetsa chikondi. Bwezerani chabwino ku choipa – Aroma 12:17,21.
4) Musaumirire pa ufulu wanu – mungadzaupezenso.
5) Mudzadalitsidwa – Mateyu 5:9.
3. Muyenera kuganizira ndi kuthana ndi zonse zoyambitsa maudani ndi kukhumudwitsa – Mateyu 18:7-14.
A. Kuganizira gwero la zolakwirana: Kodi inu muli ndi gawo lanji pa kulimbanako? Mateyu 7:1-5.
1) Ndi milandu yochepa yomwe wolakwa amakhala mmodzi.
2) Yang’anani bwino mopanda kukondera chomwe chakhumudwitsa mnzanu, mwana, kholo,
mbale, ndi mlongo wanu.
3) Kodi zochita zanga pankhaniyi zimaonjeza bwanji moto wa nkhani?
a. Mwina zolakwa zamnzangayo sizachilendo kwenikweni, koma momwe ndazitengera
ndi momwe muli moonjezera mafuta pa moto.
b. Mwina ndimaganizira kwambiri za ufulu wanga.
c. Ena sadzasiya kuchimwa. Kuthetsa kwake kuyenera kukhala malingana ndi momwe
ndiitengera nkhaniyo.
Umodzi 11
d. Ichi ndicho chinsinsi cha ufulu ndi mtendere.
B. Kuchotsa zoyambitsa kulakwirana:
1) Kuyankhula (dula dzanja lako, kolowola diso) kumasonyeza changu chochotsera zoyambitsa
uchimo ndi kulakwirana. Mizimu ikutayika.
2) Kudzitamandira ndi kudzikonda kwanga sikuli koyenera.
3) Chikondi ndicho chidzalipira mtengo wa mtendere ndi kuyanjananso.
a. Yesu analipira msonkho womwe sanayenera – Mateyu 17:24-27.
b. “Bwanji osangololera kuti inu mukhale onyengedwayo” – 1 Akorinto 6:1-8.
c. Abrahamu anangompatsa Loti mwayi woti iye asankhe malo okhalako poyambirira
popewa kulimbana – Genesis 13:8-11.
4) Muthane nazo zolakwiranazo tsopano – musalorele kuti kudzitamandira kwanu ndi
kudzikonda kwanu kuononge mwana wa Mulungu – Aroma 14:13,15,19,21.
4. Tsatirani ndondomeko ya Mulungu yothetsera zolakwirana – Mateyu 18:15-20; 5:23-26.
A. Pitani kwa yemwe wakulakwiraniyo ndi kumuuza iyeyo osati ena ayi.
1) Timangofuna kuuza wina aliyense chifukwa cha mkwiyo wathu.
2) Anthu ambiri amathamangira kuuza akulu a mpingo asanaonane ndi wowalakwirayo.
B. Pitani modzichepetsa ndi modekha – Agalatiya 6:1. Mkwiyo umapangitsa kuti munthu winayo
ayambe kudziteteza ndipo amayamba kudzikonzera njira zodzitchinjiriza nazo.
C. Chitani zimenezi mwachangu, mkanganowo usanakule, usanakhudze ena, ndipo mitima isanafike
polimba.
1) Timalandira chilango chowawa pokana nzeru ya malemba.
2) Kulimbana kumakhala zaka zambiri mwinanso mpaka moyo wawo wonse chifukwa cha
kunyada.
3) Koma ngati pali chikondi chokwanira ndi kukhudzidwa pa moyo wabwino wa pa banja pake,
mpingo, kuntchito, anthu atha kupeza njira.
5. Khululukani monganso Mulungu anakukhululukirani. – Mateyu 18:21-35.
A. Kukhululuka kulibenso china chofaniziridwa nacho, ngati tifuna kupulumutsidwa – Mateyu
6:12,14,15.
1) Kusakhululuka ndilo “tchimo losakhululukidwa” lomwe tingalichite.
2) Nchifukwa chiyani tidzayembekezera kuti Mulungu atichitire ife zomwe sitingachitire enawo?
3) Kubwezera kuli kwa Mulungu – Aroma 12:19.
B. Kukhululuka ndi “mchitidwe wokhala ndi cholinga” osati wongomverera m’thupi ayi.
1) Monganso chikondi, ndi lamulo lachikhalire.
Umodzi 12
2) Titha kuganizira zosankha kuchita mchitidwe wokhululuka. Kenako tidzayamba kumva m’thupi.
C. Kusakhululuka kumangolekerera ubale ukumangosweka.
1) Kuwawirana mtima pakati pa mwamuna ndi mkazi komwe kumangokhala osapezeredwa njira
yothetsedwa kumasakaza banja. (Ngakhale kuwawirana mtima kwa kholo, mbale, mlongo ngakhale wina aliyense).
2) Mkwiyo ndi kuwawirana mtima kwathu kumapatsa Satana mwayi m’miyoyo yathu – Yakobo
1:20; Aefeso 4:26,27.
D. Kukhululukirana kumabwezeretsa ndi kuchiza maubale owonongeka.
1) Ngati wina apempha chikhululukiro, tiyenera kutero nthawi yomweyo kuchokera pansi pa
mtima, popeza nafenso ndi ochimwa.
2) Mzimu wokhululukira umakhala wofunikira munthu winayo asanalape.
a. Khristu anapempherera iwo omupachika – Luka 23:34.
b. Mzimu wokhululukira sufulumiza kuchita choipa – 1 Petro 4:8; 1 Akorinto 13:6,7.
c. Pamene munthu mmodzi ali nawo mzimu wokhululukira ndipo abwera poyera,
zimapangitsa kuti winayonso abwere poyera.
Mawu otsiriza: Pamene tikuchita ndi zolakwirana, tikupemphedwa kuti “tithetse zoipa ndi zabwino.” – Aroma
12:20,21. Chabwino chomwe muchita chidzasungunula mtima wa yemwe munali kulimbana nayeyo – 1
Samueli 24:26.
Umodzi Pakati pa Ogwira Ntchito Gawo Lachiwiri: Pamene Ogwira Ntchito Mumpingo Alekana Maganizo.
Kodi bvuto lalikulu mumpingo ndiliti? Pa za utumiki? Akulu ambiri amaganiza kuti bvuto lalikulu ndi la
maubale a pakati pa atsogoleri. Mipingo yambiri yaonongeka chifukwa chakulimbana pakati pa akulu ampingo
koposa mabvuto ena monga ankhuli yachiwerewere kapena zanyanga ndi ufiti.
1. Ogwira ntchito mumpingo ayenera kuphunzira kusamalira ubwino wa ntchito ya Khristu asanaganizire za
zofuna zawo, ndiponso ayenera kudziwa ndi kuphunzira bwino magwero a zolimbana ndi kuthana nazo
zisanafike powasokoneza mwa uzimu, kusokoneza ntchito yawo, kukhumudwitsa ntchito ya mpingo
kumudzi ndi kumayiko akutali, ndi kulepheretsa kupulumutsidwa kwa miyoyo.
Sitingathe kulipira mtengo wa kulakwitsa komwe kungabwere kwa ife ngati tilephera kuchita zimenezi –
Luka 17:1-2; Yakobo 3:1.
2. Akulu ampingo ayenera kuzindikira gawo la moyo wodzikonda poyambitsa zolimbana. Akulu ampingo
nawonso ali nalo bvuto limeneli monganso wina aliyense. Amishonale kapena ogwira ntchito ampingo
nthawi zonse ayenera kumagwira ntchito m'magulu. Tingathe kumanena kuti tikulimbana chifukwa
“chofuna kutsata mfundo zokhazikika,” “zotumikira za mudongosolo”, kapena “nkhani zauzimu,”
pamene nkhani yeniyeni iri, “kodi wamkulu ndani?” “kodi akulamulira ndani?” pakadakhala palibe
kudzitukumula, nkhani zinazo bwenzi zitathetsedwa.
Mukaika atambala awiri mukhola lankhuku ndiye kuti mukhala nkhondo yafumbi mpaka adziwike mwini
weniweni wolamulira kholalo. Ndi kuganiza kuti palibe kusiyana pankhani ya nkhukuyi. Ku thupi ifenso
ogwira ntchito mumpingo tiri chomwecho pachilengedwe. Koma izi zisakhale chomwecho kuuzimu. Ndi
mfundo za Khristui ndi kukhwima mu uzimu kwa Mkhristu kokha komwe kungathe kuthetsa mabvuto a
ubale wa ogwira ntchito mumpingo. Ine kusagwirizana kudzakhalapobe koma zisafike poti mpaka
kuononga kapena kufooketsa ntchito ya Mulungu.
Umodzi 13
3. Ngakhalenso ophunzira anali kukumana ndi nthawi zina zomwe panali mabvuto osiyana maganizo pakati
pawo. Paulo ndi Barnaba anafika poti aliyense amayenda m'njira yake yake, komabe anapitirira kusunga
ndi kusamala ubale wawo monga abale – Machitidwe 15:36-40 (sikukadakhala
kotheka kuti athe kufalitsa uthenga wabwino modalilika ngati akadalephera kuyanjana wina ndi
mnzake). Pamene Petro analakwitsa, Paulo analimbana naye kwambiri – Agalatiya 2:11-14. Koma anthu awiriwa anaconda ndi kulemekezana kwambiri – 2 Petro 3:15.
4. Anthu odzikhulupirira okha ndi kudzitukumula, omva za iwo okha, omwe amati akakumana ndi
maganizo olekana ndi awo, nkumaona ngati ali pa chiopsezo, asamasankhidwe pa udindo uliwonse mu
mpingo.
Malembo amati “woyang’anira asakhale womva za iye yekha.” (Tito 1:7). Koma akhala “wodzadzidwa
ndi Mzimu Woyera.” (Machitidwe 6:3) mphunzitsi sangathe kutumikira ena ngati iye alibe chipatso cha
Mzimu Woyera. Umodzi “ndi wa Mzimu” – Aefeso 4:1-3. Posankha a mishonale kapena akulu ampingo,
sikokwanira kwa munthu kukhala wodziwa kuyankhula bwino, kukonza zinthu mwadongosolo,
utsogoleri, ndi kukhala wodalira kwambiri pa ziphunzitso kokha ayi. Zinthu zonsezi zimakhala
zosafunikira ngati wosankhidwayo alibe mzimu wa Khristu – 1 Akorinto 13; Aroma 8:9. Pamene
mukuganizira za munthu woti akutsogolereni, tadzifunsani nokha kuti “kodi munthu ameneyi amachita
bwanji ndi anthu ena pa nkhani za ntchito za kumpingo? Nanga ku banja kwake?
5. Pakati pa Akhristu ndi pakati pa atsogoleri, Yesu watiphunzitsa momwe tingathetsere kusiyana kwathu
kwa maganizo. Ogwira ntchito ampingo ndi atsogoleri ayenera kumazindikira zakuopsa komwe
kumakhalapo chifukwa chakusagwirizana pakati pawo popeza kumakhudza ntchito ya uthenga wabwino.
Kuopsa kochotsedwa, kutaika kwa nthawi ndi mphamvu, kulephereka kwa mapemphero (Mateyu
5:23,24; Ahebri 12:14); Kupunthwitsa omwe akadakhala Akhristu ndinso Akhristu aang’ono ndi ofooka
– Yohane 17:21; Afilipi 2:14,15; Luka17:1,2.
6. Ogwira ntchito ampingo ayenera kumanga mfundo yoti sadzalola kusiyana maganizo kwawo kuti
kuononge ntchito ya Mulungu.
7. Atsogoleri ndi antchito ampingo ayenera kumatsata mfundo za malemba pokonza maubale osweka.
Konzani ubale womwe wangoyamba kuonetsa zizindikiro zoonongeka zisanafike woipitsitsa. - Mateyu
18:15-17; Agalatiya 6:1; Mateyu 5:21-26; Aefeso 4:26-27; Yakobo 1:19,20; Mateyu 7:2-5.
8. Pewani chirichonse chomwe chimakulakwitsani ndi kuyambitsa zolimbana – Aroma 14:13,19,19,21;
Mateyu 18:8,9.
9. Pewani kudzitukumula – Aroma 12:16; Afilipi 2:3..
10. Musakakamire pa ufulu wanu, Yesu sanachite choncho ayi – Afilipi 2:5-11; 1 Petro 2:21-25; Aroma
15:1-3. Paulonso sanatero ayi – 1 Akorinto 4:10-13; 9:19-23; 2 Akorinto 12:15. Tonse timatha
kumverana wina ndi mnzake ndipo timaphunzitsidwa kutero – Aefeso 5:21.
11. Pewani “kuyerekeza zinthu moipa” – kuyerekeza mongoganizira mopanda umboni weniweni – 1
Timoteo 6:4; Yohane 7:24.
12. Chikondi chimakwirira machimo ochuruka ndi zolakwika za unyinji – 1 Petro 4:8; 1 Akorinto 13:4-7.
13. Khululukiranani wina ndi mnzake – Aefeso 4;31,32; Mateyu 18:21-35.
14. Sungani chidzalo cha chipatso cha mzimu woyera – Agalatiya 5:22,23; Luka 11:13.
15. Sankhani antchito omwe ndi obvomerezeka mogwirizana ndi maganizo a choonadi ndi mfundo za
mpingo pa ntchito zake. Ngati pali kusamvana mu nkhani zina, kambiranani zimenezi m'kanyumba
komatu popanda abale ena onse.
16. Ngati nkhani zake ziri zazikulu mutha kuitana akulu ena odalirika kuti ayese kukuthandizani kukonza
Umodzi 14
zobvutazo. Nthawi zina mutha musiyitsa njira yanji, koma chofunikira kwambiri ndi choti anthu awiri
olakwiranawo athetse nkhani yawoyo mwa uzimu ndipo akhaliranenso mwa mtendere pakati pawo koma
ngati apitirirabe kusungirana mkwiyo m’mitima mwawo, chisomo cha Mulungu chiyenera kuchotsedwa
kwa iwo pa ntchito yawo ya mtsogolo.
Takambirana za zosautsa, koma paliponse pamene mzimu wa Khristu uli mwa ogwira ntchito, zosautsa zonse zimathetsedwa zisanafike poipitsitsa. Mautumiki ena omwe amagwiridwa mogwirizana amathekanso, monga
anamchitira Paulo ndi anzake ogwira naye ntchito – Afilipi 3:16-17.
Umodzi Pakati pa Ogwira Ntchito Gawo Lachitatu: Kumanga Ubale Wabwino Pakati pa Atsogoleri Ampingo
Mawu oyamba: Mpingo utha kumayenda bwino, koma kenako ntchito imayamba kusokonekera chifukwa cha
kukangana wina ndi mnzake pakati pa atsogoleri. Ntchito zambiri za pa mpingo zimalowa pansi ndi kuzilala
chifukwa cha kukokana komwe kumayambika chifukwa cha ziphunzitso zonyenga. Ife atsogoleri kupyolera mu
kufooka kwathu, chonde, tisaononge kachisi wa Mulungu. 1 Akorinto 3:16,17.
1. Maganizo osiyanasiyana okhudza ubale pakati pa atsogoleri onse a mpingo (woyang’anira ndi
woyang’anira mnzake, woyang’anira ndi mlaliki, woyang’anira ndi mtumiki, ndi ena). Zambiri za
mfundo zimenezi, zimathandizanso pa ubale apakati pa Akhristu onse.
A. Chitani zonse mosakondera kapena kuyang’ana nkhope – 1 Timoteo 5:21. Aliyense ali nawo
anthu omwe amakondwera nawo, komatu izi zisakhudze momwe muchitira ndi anthu enawo.
B. Musamuyankhulire munthu mawu omwe simunayenera kumuyankhulira. Ndipo musayankhule
chirichonse chokhumudwitsa chomwe chiri chosathandiza.
C. Ganizirani ndi kusinkhasinkha zonse zomwe mwakonza ndi mawu omwe mwakonza kuti kodi
enawo akamva siziwapweteka m’maganizo?
D. Musakhale odzitamandira nokha ndi kumva za inu nokha monga opambana – Aroma 12:3,16.
E. Muzindikire zomwe zingautse, komanso zofooka za anthu ena pamodzi ndi zomwe amakonda
maganizo awo onse. Yesetsani kusamalira zimenezi ngati nkotheka.
F. Muzilolera zofooka za anzanu monga momwe mungafunirenso kuloleredwa pa zofooka zanu ndi
anzanu – Mateyu 6:14,15; Aroma 15:7.
G. Zindikirani kufunika kwa mphatso iriyonse ndi luso m’thupi la Khristu – Aroma 12:3-8.
Musayembekezere kuti munthu aliyense azingochita bwino nthawi zonse. Yamikirani mphatso
ya munthu aliyense pa yekha koposa kumukana kapena kumunyoza chifukwa chakulephera
kwake.
H. Nthawi zonse perekani ulemu kwa iwo omwe ayenera kuulandira panthawi yake – Aroma 13:7.
Khalani achangu potulukira zabwino zomwe ziri mwa anthu ena monganso momwe
mungachitire ndi zoipa mwayiwo. Mulibe ufulu wodzudzula zolephera, koma muyambe
mwabweza mangawa oyamikira ndi kulemekeza khalidwe labwino.
I. Phunzirani ndi kuzindikira chifukwa chomwe munaonetsera khalidwe la mtundu umenewo kwa
anzanu, ndipo muchotseretu moyo woipawo ku mbali yanu. Ichi chidzadalitsa moyo wanu wonse
kuchokera pa nthawi yomwe mwa phunzira izi.
J. Pa mkangano uliwonse, poyamba, inde movutikira, taonani ndi kufufuza mokhulupirika mbali
yomwe inu mwachititsa kuti mkanganowu ufike pamenepa, chomwe mumachita, ndipo kenako
yambani mwadzikonza inu eni ake – Mateyu 7:1-5.
K. Fulumirani kukonza ubale ndi kubwezeretsa mgwirizano pamene kusamvana kungoyamba
Umodzi 15
kumene, pamene anthu sanataye mafuno abwino kapena chikhulupiriro mwa wina ndi mnzake.
Kukonza kumeneku kukhala chinthu choyamba kuganiziridwa. Ubale umasokonezeka chifukwa
ife timalolera kuti zitero. Anthu amakhala ogwirizana pamodzi chifukwa amatsimikira kutero
mokondweretsa Yesu. Ayenera kutero.
L. Ngati pali kusaganizirana bwino pakati panu ndi mnzanu pa nkhani ina, musayembekezere kuti
mnzanuyo ayambe kubwera kwa inu kudzapepesa. Yesu akuwauza olakwiridwa onse kuti iwo
apite – Mateyu 18:15-17. Akumuuza wolakwirayo kuti apite – Mateyu 5:23-25. Palibe
“weniweni woti akhale woyamba kupita”. Koma pitani ndi kudzichepetsa konse poopa kuti
mungaonjezere mabvutowo – Agalatiya 6:1. (Atsogoleri nawonso ayenera kudzichepetsa, lamulo
limeneli lodzichepetsa silichotsera atsogoleri ayi). Muyenera kuuza mnzanu kuti “timangoononga
ntchito ya Mulungu ndi Kupunthwitsa ena ngati tipitirira kusungirana udani. Ine ndifuna kuti
tiyambe kukhalirana bwino iwe ndi ine. Kodi titani pamenepa?
M. Khululukirani moonadi iwo omwe akulakwirani – Mateyu 18:21-35. Mulungu
sangakukhululukireni ngati inu simukhululukira. Zindikirani kuti kukhululuka sichinthu
chongomveka m’thupi ndi m’maganizo mwanu chabe koma ndi chinthu chomwe munthu
amachita kusankha kuti achite.
N. Lumikizanani ngakhale mnzanuyo sakutero. Khalani okonzekera kulandira mnzanuyo, siyani
chitseko chikhale chotsekula nthawi zonse.
O. Chitani zabwino ndipo mukhale achifundo ngakhale mnzanuyo akuchitireni zoipa zotani.
Musabwezere choipa ndi choipa chinzake, koma ndi chabwino gonjetsani choipacho – Aroma
12:17-21.
P. Mudzitha kukhala tcheru pofulumira kuona nthawi zomwe ena akumva kuwawa, kaya
kulimbana, ndiponso pamene akukumana ndi nyengo zowawa, ndipo muonetse mtima
wachifundo. Musangokhala omangiririka ku zinthu zanu zokha zokondweretsa inu nokha
mpakana kuchita kuiwala osatha kuona mabvuto a ena.
Q. Ganizirani njira zoonetsera chikondi ndi kuganizira ena. Chikhale cholinga chanu kuti nthawi
zonse mukhale monga wolimbikitsa ndi wochangamutsa munjira yomwe muyankhulira ndi
kuchitira.
R. Muzikhala ndi maphunziro a Baibulo olongosoka ndinso mapemphero pamodzi ndi atsogoleri ena onse. Izi zidzakuikani inu kufupi ndi Mulungu ndiponso pakati pa wina ndi mnzake.
S. Khalani ndi nthawi zapadera zomachezerana, kubindikira pamodzi ndinso kusangalala ndi
atsogoleri ena (monga mwa chitsanzo, mabanja awiri kuyenderana kumapeto a sabata). Izi
zimalimbikitsa ubale.
T. Zindikirani kuti anthu ena ndi obvuta kumvetsa zinthu. Anthu ena samalola kuti chisomo
chiwasinthe kwatunthu mumtima mwawo. Zindikirani kuti muyenera kukhala ndi moyo
wodziletsa ndi wolimba kuti musaonetse kupsa mtima kwanu kwa anthu oterewa ndi cholinga
chofuna kuwaonetsa chitsanzo chanu chabwino ndi kutinso ntchito ya Khristu isasautsike.
Yesetsani kutchinjiriza moyo wanu ndi kuusunga bwino poyambirira pomwe musanapse mtima –
Izi zimakhala zosabvutirapo
U. Ngati mukukaikira, nthawi zonse tsatirani lamulo labwino ndi loyenera kusungidwa iri:
“muzonse, chitirani ena zomwe mungakondwere iwo atakuchitirani.” – Mateyu 7:12;
tawerengani ndi kufaniziranso ndi Mateyu 22:39.
2. Maganizo ena oti mlaliki achite nawo pankhani ya ubale wake ndi oyang’anira/abusa.
A. Alemekezeni abusa ndi mawu ambiri. Ngati mungathe kuwalola kuti akuyang’anireni pa ntchito
Umodzi 16
yomwe mukugwira, teroni. Mutha kuyankhula nawo molimbikira mfundo yanu, koma nthawi
zonse munjira yaulemu. Ngati muli nawo bvuto, yankhula nawoni abusawo kapena mmodzi wa
iwo osati kuyamba kumanena za iwo ndi anthu ena.
B. Musataye nthawi pomachita zionetsa kukondweretsedwa ndi mmodzi kapena ena a iwo. Izi
zingathe kuononga ntchito yanu ndi abusawo. Inde malinga ndi chikhalidwe cha munthu, mutha kuzolowerana ndi abusa ena mosiyana ndi ena, komabe muyenera kupereka ulemu mofanana
kwa onsewo. Onanani ndi abusa osiyanasiyana mu nthawi zosiyanasiyana pa nkhani zomwe
sizisowa abusa onsewo pamodzi.
C. Musanyengere abusawo kapena kuwachititsa kuti akukondeni munjira ya dziko kapena mwa
ndale, koma yesetsani kukhala mbale wachilungamo ndi choonadi kwa onsewo.
D. Musawapeputse abusa ngati inu munaphunzira bwino Baibulo kuposa iwo. Koma mugawane
nawo zinthu zabwino mwa Ambuye pamene mungathe kutero, ndi kuwalimbikitsa kukula mu
uzimu. Zinthu zomwe mungagawane nawo zitha kukhala mabukhu, maganizo, makaseti a mawu
a Mulungu, ma autilaini, madongosolo, anthu ndi zina zotere.
E. Mlaliki asataye nthawi ndi kulimbana ndi abusa chifukwa cha ulamuliro kaya kukondedwa.
Ngati anthu amenewa, abusa ndi mlaliki ali wokhwima mu uzimu wa Khristu, iri silimakhala
bvuto kwa iwo. Mwina ngati bvutoli liripo, aliyense wokhudzidwa achite ndi mzimu wake ku
mbali yake.
F. Ziri kwa abusa kuitana alaliki ku misonkhano yawo kapena ayi. Koma sayenera kuitana mlaliki
ku msonkhano womwe nkhani yake iri kuyang’ana mlalikiyo. Komabe pamene pali ubale
wabwino, abusa ambiri amasangalala poitana mlaliki chifukwa chakumvetsa kwake ndi udindo
wake pa mpingopo. Izi zimakhala zoona pamene abusa ake akuwetadi nkhosa mwa uzimu osati
omangochita misonkhano yongofuna kumanga mfundo wamba. Onsewo ndi ogwira ntchito a
mpingo, ndipo mlaliki monga wodziwa bwino za nkhosa zapampingopo, angathe kukhala
thandizo la mtengo wapatali kwa abusawo popanda kusokoneza dera la udindo wawo.
G. Alaliki omwe angosankhidwa kumene ayenera azibweretsa pang’onopang’ono maganizo awo
akusintha kwa ntchito zina za mpingo. Perekani nthawi yokwanira musanayambe zina, poonetsa
ulemu.
H. Ngati mpingo umapereka chithandizo kwa mlaliki, mlalikiyo ayenera adzigwiradi ntchitoyo.
Popeza nthawi zambiri amagwira popanda woyang’anira, ayenera aziyambitsa yekha ntchito zambiri. Ayenera kumagwira ntchito nthawi yake yonse ngati alandira chithandizo pa zosowa
zake zonse. Mlaliki asamajombe pa ntchito ya mpingo chifukwa cha ntchito zake zathupi kaya
bizinesi yake. Nthawi yomweyonso, abusa ayenera kuzindikira kuti kufunika kwa mlaliki
kumasinthasintha malingana ndi nthawi, choncho sangathe kusunga dongosolo lokhazikika
(ngakhale kuli koyenera kuti azisunga dongosolo labwino). Ngati mlaliki ali wodzipereka nthawi
zonse, abusa asamuimbe mlandu ngati nthawi zina agwira ntchito zapakhomo pake munthawi in
yatsiku lomwe kulibe ntchito zazikulu. Ayenera kukumbukira kuti amagwira ntchito munthawi
zambiri zausiku posawerengera masana ndi zina zotero. Koma izi zisachitike mopitirira.
I. Mlaliki ayenera kuchita dongosolo lomadziwitsa abusa pa kusintha kwa madongosolo a ntchito
zake monga maulendo opita kwina, maulaliki a nyumba ndi nyumba, ndi zina zotero, ngakhale
ngati maulendowo anali obvomerezeka. Izi zimathandiza kupewa kusamvetsetsana.
J. Ayeneranso kupereka dongosolo lokambirana ndi abusa mfundo ziri zonse zazikulu zomwe
afuna kuchita, zomwe ziri zoyenera kukambidwa pakati pawo.
K. Mlaliki ayenera aphunzire kusunga chisomo pamene mfundo zomwe anakonza zakanidwa ndi
abusa. Abusa angathe kumva zinthu mosiyana ndi momwe iye akumvera, komabe munjira
iriyonse, palibe yemwe adzingokhalira kuchita zake zokha nthawi zonse. Mlaliki asakhale
wowinya ngati mfundo zake sizinamveredwe.
Umodzi 17
L. Ngati mbusa mmodzi kapena abusa angapo nthawi zonse angotsutsa kapena kulimbana ndi
mfundo zonse zomwe mlaliki apereka, pamenepa mlaliki angolimbikira pa mfundo zomwe iwo
agwirizana nazozo kuti poteropo ayambe kubwererana pafupi ndi kumvetsana
pang’onopang’ono. Kuganizirana zina ndi zina kungathe kuzima ngati mlaliki atsatira njira
zobweretsa chiyanjano nayesa mwa choonadi kukondweretsa enawo. “Gonjetsani choipa ndi
chabwino” – Aroma 12. Musalole maganizo owawa akhazikike mkati mwanu poganizira mbusa kapena abusa, chifukwa izi zidzalepheretsa kuti mugwire nawo bwino ntchito.
M. Mlaliki ayenera kuyesetsa kumvera zomwe abusa afuna momwe angathere, ndipo ndi mtima
wofunadi. Koma ngati ali ndi bvuto lachikumbumtima ndipo sangathe kuchita zomwe iwo afuna,
ayenera wachifundo koma moona mtima kufotokoza bwino kwa iwo ndi kupempha kuti ayese
kumukomera mtima. Ngati apempha mwa mzimu wabwino, iwonso adzamumvera ndi
kulemekeza pempho lakelo. Chirichonse chingatheke kukonzedwa pokambirana munjira
yabwino popanda kukhumudwitsana.
N. Ngati pali bvuto lalikulu pakati pa mlaliki ndi mpingo kapena abusa loti kusiya ntchito yake
kungakhale ngati njira yabwino, ayenera kukambirana moona ndimosasuka ndi abusa ndipo iwo
onse pamodzi ayesere njira zonse zoti ziwathandize kukonza ndi kuthetsa bvuto lawolo.
Chimodzi modzinso ngati bawo abusa ali ndi bvuto longa lomweli ndi alaliki.
O. Nthawi zina njira yothandiza imakhala yosiya ntchito – Machitidwe 15:36-41. Ngati mlaliki
waona kuti nkwabwino kupuma ntchito, ayenera kutero popanda kuyambitsa maganizo achabe
kapena kugawanitsa mpingo. Pa nthawi yobvuta imeneyi, zambiri zidzadalira momwe iye
asungira lirime lake. Ndipo ngakhale kuti abusa ndi mlaliki agwira ntchito zolekana kuyambira
pamenepa, iwo ayenerabe ngati nkutheka kusunga ubale weniweni. Ayenera kukhazikitsa ubale
ndi Chiyanjano asanalekane.
P. Pamene mlaliki ndi mpingo alekana, pasapezeke m’modzi wonenanena zambiri kwa akunja ndi
onse omwe siziwakhudza mosayenera kapena kusiya mbiri yachabe.
Q. Mlaliki ayenera apereke nthawi yokwanira kuti mpingo uthe kupeza wantchito wina, ndipo
mpingo uyenera kumpatsa mlaliki nthawi yoti akonze madongosolo atsopano.
R. Alaliki ndi abusa ayenera kukhala ndi zolembera za mapangano awo pa zomwe wina
angayembekezere kwa wina pofuna kupewa zosagwirizana zina ndi zina.
3. Maganizo ena oti abusa achite nawo pankhani ya ubale wawo ndi alaliki.
A. Yesetsani kumvetsa ndi kulemekeza maganizo a mlaliki, ngakhale pamene simubvomerezana
nawo nthawi zonse.
1) Nthawi zonse mlaliki amakhala kuti anaphunzitsidwa kuyesetsa kugwiritsa ntchito
malemba mobvomerezeka pofunafuna ndi kukulitsa mizimu yambiri. Nchachidziwikire
kuti abusa sangamvere maganizo onse omwe mlaliki angapereke, koma pomangotsutsa
nthawi zonse ndi kumangonena-nena za maganizowa, abusa amakhumudwitsa ndi
kugwetsa mphwayi antchito achinyamata abwino ndipo nthawi zambiri kupangitsa kuti
asiye ndi kuchoka m’chiyanjano chathu kapena kusiyananso utumiki kwathu. Abusa
ayenera kupewa msampha wodziona ngati atetezi a zochitika kokha. Abusa nawonso ndi
atsogoleri ndipo monga achitira mlaliki ayeneranso kumafunafuna njira zoberekera
zipatso.
2) Abusa ayenera kubvomereza kuti ndi momwe zimakhalira monga mwa chilengedwe kuti
mlaliki amakhala ndi maganizo amphamvu, atsopano. Ena. Ena amakhala abwino, ena
ayi. Abusa ayeneranso kukumbukira kuti kumatheka kuti mbusa akhale ndi maganizo
akale otopa, kukhala wozolowera zomwe zomwezo, kuopa kugwira ntchito mwa
mphamvu, kapena kuwalola kuchepetsa kapena kusiya kumene kulamulira magawo ena
antchito yake. Abusa ayenera kukhala ndi maganizo sinthika pa nkhani zimenezi ndi
Umodzi 18
zizolowezi zimenezi. Atatero ndiye kuti zidzamuthandiza kugwirizana bwino ndi mlaliki
ndipo zidzamthandiza kubvomereza pamene alaliki akana kulandira maganizo ake.
B. Abusa ayenera kulemekeza maphunziro ndi zonse zomwe mlaliki adziwe, mphatso ndi maluso
osiyanasiyana a mlaliki. Ngakhale sangathe kubvomera zonse, ayenera adzikhala ndi chidwi
chomvera moona maganizo akewo. Nati afuna kukonza bwino kapena kukana kumene maganizo amlaliki, ayenera kutero m'njira yoti sikhumudwitsa mlaliki. Kudekha ndi kudzichepetsa ndi
zofunika kwa abusa monga ziriri kwa Akhristu ena onse.
C. Abusa ayenera kuganizira za zosowa za mlaliki pachuma ndi nthawi ndi banja lake. Ayenera
kumlimbikitsa kuti aziwauza za zosowa zake momasuka ndi moona. Utumiki wake
umamutengera nthawi yake yokhala ndi banja lake, ndipo abusa ayenera kumamvetsa pamene
mlaliki asowa kuchitako zina za kubanja kwake. Abusa ayenera kukonza dongosolo la masiku
omwe mlaliki ayenera kupuma ndi nthawi yoti ayendere malo ena monga kupumula.
D. Abusa ayenera kukonza dongosolo loti amve maganizo a mlaliki pa za alaliki ena omwe
angaitanidwe ku misonkhano ndi zokambirana zina. Mlaliki angathe kudziwa zomwe abusa
asoweka kuti adziwe pa za kufunika kwa mlaliki woitanidwayo pa ntchito ya pampingopo.
E. Ngati mlaliki akulakwitsa, abusa ayenera kumuthandiza modekha koma mwa chimvekere kuti
athe kuona zomwe akuchitazo. Ayenera kugwiritsa ntchito njira yomwe ingamulimbikitse, osati
njira yomwe ingamuvulaze m’maganizo.
4. Maganizo ena othandiza abusa pamodzi ndi alaliki.
A. Ayenera kumalowa ndi kuchita maphunziro pamodzi, kupemphera pamodzi ndi kulowa
m’bindikiro pamodzi kuti athe kuphunzira ndi kufunafuna cholinga cha Mulungu kuti athe
kulunzanitsa maganizo ndi mitima yawo ku zolinga ndi njira zofanana.
B. Abusa ndi alaliki ayenera kumazidziwa okha, akhale omvetsa zokhumba zawo zomwe
zingaonetse kudzikonda, ndipo azindikire zonse zomwe zingawafooketse kapena zofooka zawo
zimene, zamkati mwawo zomwe zingawapangitse kuti akhale odzimva mopitirira kapena kufuna
ulamuliro mopitirira. Ayenera moganiza bwino ndi mwachangu kuthana ndi zizolowezi zimenezi
kuti mwina izi zingaononge ntchito ya Yesu ndi kusokoneza mizimu. – 1 Akorinto 3:16,17.
C. Umodzi pakati pa abusa ndi alaliki uyenera ukhale woti mpingo wonse uchitire umboni monga
chitsanzo chabwino. Ngati pabuka kusamvana pankhani zina, chonde, zimenezi zisadziwike ndi ena onse koma zikhale monga chinsinsi pakati pa atsogoleri kufikira njira yothetsera itapezeka.
Abusa ayenera kuthandizira mlaliki monga momwe angathere pamaso pa mpingo monganso
momwe mlaliki naye angachitire.
5. Maganizo ena othandiza pakati pa mlaliki ndi alaliki enawo.
A. Ngati alaliki awiri agwirira ntchito pamodzi, nchachidziwikire kuti zikhala ngati zija za atambala
awiri mkhola limodzi. Amalimbana mpaka mmodzi aoneke wamwamuna. Moyo umenewu
womwe ndi wathupi, wokonda kulimbana, ulibe malo ndi nthawi pakati pa antchito a Yesu ndipo
uyenera kuthetsedweratu mwa kulapa ndi mzimu woyera. – Agalatiya 5:19-26.
B. Mlaliki ayenera kutaya khalidwe lonse la nsanje ndi kaduka pa mlaliki mnzake yemwe ali ndi
nzeru ndi maganizo oposa mnzakeyo. Iye ayenera kukondwera chifukwa mlaliki mnzakeyo
akutha kutumikira Mulungu mwangwiro. Dziwani kuti tonse tiri m’gulu limodzi.
C. Mlaliki asataye nthawi yake pomabvutika mumtima chifukwa mlaliki wina akuthandizidwa
kapena akulemekezedwa bwino, kapena akuchitidwa bwino munjira iriyonse. Mtumiki wa
Mulungu akhale wokhutitsidwa pololera kuti Mulungu akhale wokonza ndi Kulongosola za
ulemu ndi thandizo lomwe iye angalandire, ndi bwino kungoganizira kwambiri za ntchito yake
yotengera chipulumutso cha Yesu kwa anthu. Tiyenera kutaya ufulu ndi ulemu wathu monganso
Umodzi 19
adachitira Yesu – Afilipi 2:5-11; Yohane 3:26-30.
D. Mlaliki yemwe ndi mlendo pa malopo ayenera kutsogoleredwa m’njira iriyonse yofunikira ndi
mlaliki wa pamalopo, iye ndi yemwe angalondolere kwa anthu omwe ayenera kuyenderedwa, ndi
zina zotumikira za uzimu pa mpingopo, ndi zina zotero. Mlaliki wodzachezayo, ngati ali ndi
mzimu wabwino, amabwera kudzatumikira, ndipo adzabvomera maganizo amlaliki wa pamaloyo.
Mawu otsiriza: Nkutheka kuti kudzera mu ubale wapakati pa anthu kuposa m’njira iri yonse, atsogoleri ndiwo
ali ndi mwayi woonetsa dziko zoonadi ndi kukoma kwake kwenikweni kwa ziphunzitso za Ambuye wathu
Yesu Khristu.
Umodzi Pakati pa Ogwira Ntchito Gawo Lachinayi: Zomwe Tingachite ndi Zolimbana.
Yesu nthawi zonse ankachenjeza ophunzira ake za mabvuto, zotsutsa ndi za mayesero omwe atumiki ake anali
kudzakomana nawo. Sanayesere ndi pang’ono pomwe kungowaika m'masamba kuti iwo aganize kuti iwo
adzakhala akupambana mosabvuta ndi mwa chisangalalo – Mateyu 10:16-42; Luka 9:57-62. Koma iye
anawalonjeza za chisomo ndi thandizo loti adzathe kuchita bwino, ndipo anawaonetsa kuti adziwe kuti
ntchitoyo pamodzi ndi mphoto yakeyo ndi zoyenera kubvutikiridwa. Nkhondo ya uzimu ifanana ndi nkhondo
zina zonse. Pamakhala kulimbana, zobvuta ndi zoopsa zomwe. Komabe iyenera kukhalapo basi ndipo
koyenera. Msirikali aliyense amakhala ndi zolinga ziwiri pa nkhondo yake, choyamba chimakhala chofuna
kugonjetsa mdani, ndipo chachiwiri kudziteteza kuti asagonjetsedwe.
1. Momwe tingachitire ndi zotsutsana.
A. Tiyenera kukonzekera kukomana ndi zolimbana – 2 Timoteo 3:12; Luka 6:22-26; Mateyu
10:16,34-36; Machitidwe 20:23; 1 Akorinto 16:8,9; Marko 10:29,30; Aefeso 6:10-12; 2 Timoteo
2:3; Yohane 3:19; Yohane 15:20.
B. Kutsutsana kulipo kwa mitundu ndi mphamvu zosiyanasiyana.
1) Kwina ndi komwe mumachita ku kuyamba nokha chifukwa cha kupusa kwanu, kufooka
kwanu kapena kuchimwa kwanu.
2) Kwina ndi komwe kumachokera kwa abale ofooka komabe olimbikira omangiririka ku
ziphunztso ndi zizolowezi za anthu, kusakhwima kapena kukhala ndi mtima wokhulupirira
kwambiri zinthu zadziko. Tawerengani Mateyu 16:21-23; ndipo mufanizire.
3) Kwina ndi komwe kumayamba pamene muputa anthu omwe ndi omangiririka ku
zolimbana, zofuna zawo ndi osakasaka chisangalalo ndi ulemerero.
4) Kwina ndi komwe kumayambitsidwa ndi choipa chomwe chimakhazikika kwa anthu koma
ndi kumaoneka ngati ndi chauzimu.
C. Dongosolo lothandiza pochita ndi kugonjetsera zotsutsana pa utumiki wanu wa Yesu.
1) Nthawi zonse muyambe ndi kupempha nzeru kwa Mulungu, ndi kukhulupirira Iye
adzaperekadi – Yakobo 1:5-8 (kutsutsa kumatithandiza potipangitsa kuti tidalire Mulungu).
2) Yeretsani moyo wanu ndi mtima wanu kuti mukhale okhulupiriradi za Chiyanjano chanu
ndi Yesu ndinso chithandizo chake. “musasiye malo ena alionse, ngakhale kufooka kwina
kuli konse kwa mzimu.” – Aefeso 6:10-18; Yohane 14:30.
3) Chotsani mwa inu chirichonse cholakwika chomwe chingathe kumayambitsa kapena
kuthandizira pa zotsutsana – Machitidwe 24:16; 1 Akorinto 10:31-33; 11:1.
Umodzi 20
a. Mwapemphero, moona, fufuzani moyo wanu ndi womwe mumafikira enawo – 2
Akorinto 13:5; Mateyu 7:5. Kodi mumangochita zinthu potsatira zomwe thupi ndi
maganizo anu afuna mosalingalira bwino, kodi mumachita zinthu mopupuluma, kodi
mukusowa moyo wa chisomo pa makhalidwe anu, kodi mukusowa kudzichepetsa
ndi kuupeza mtima, kusagwirizana ndi zina, kukondera, kukhulupirira ndi kumva
zanu zokha? Kutsutsidwa kumatithandiza kuti tikhale ndi mwayi wokonzanso moyo ndi khalidwe lathu.
b. Ngakhale pamene mnzathuyo watilakwira, tiyeni tidzifulumiza kupeza njira
yothetsera bvutolo ife tokha. Kumakhala kobvuta kuti tiwasinthe ena mwa msanga
nthawi zonse, koma mungathe kudzisintha nokha, kusintha momwe muchitira ndi
ena akakulakwirani ndinso machitidwe anu pa nthawi yotsutsidwa.
4) Khalani msirikali wodalira nkhondo – Aefeso 6:18; Akolose 4:12. Pemphero la
wolungama lingathe kuchotsa mapiri a zolimbana – Marko 11:20-25. Pamene muli ndi
bvuto lalikulu, chitani nalo mwa kusala kudya ndi pemphero (komatu mukhale oupeza
mtima ndi okhazikika m’maganizo pa kusala kwanuko – chifukwa njirayi iribe tsenga liri
lonse.) Mulungu amakonda mapemphero a iwo amene amakonda mpingo ndi mizimu ya
otayika ndi ofooka.
5) “Pita kwa mbale wako” – Mateyu 18:15-17; 5:25; Aefeso 4:26-27. Musanene kwa ena
zambiri za yemwe akukutsutsaniyo – yankhula nayeni. Konzani zolimbana zanu
mwachangu zisanafike poopsa, makamaka pamene mwangoyamba kumene kudabwa,
musanayambe kukayikirana koti zinthu zifike pobereka uchimo waukulu. Konzani msanga
ming’alu ya ubale wanu isanasanduke mipata yaikulu ndi kugwetsa khoma lonse. Koma
pitani ndi kudekha konse – Agalatiya 6:1. Mapitidwe amenewa amafunika kudzichepetsa.
Ngati mutatsatira njira imeneyi yolumikizana ndi mbale wanuyo, kuphatikizana ndi
kupepesa kwanu, ndiye kuti mbale wanuyo adzakhala ndi mwayi waukulu womvetsa
momwe inu mumamukondera. Ngati muchita ndi zolimbana zanu mwathupi osati mwa
malemba, ndiye kuti zimangokhala ngati mwapereka mwayi wothira mafuta anyali pa moto
wa mumtima mwa yemwe mukutsutsana nayeyo. Pewani kutsutsana ndi kulimbana poyera,
koma ngati zingatheke zosakhudza mpingo ndi ubale wanu.
6) Musalimbane kapena kuchita makani – Mateyu 12:18-21; 2 Timoteo 2:24-26. Gwiritsani
ntchito kudandaulira mwachikondi ndi choonadi choperekedwa mwa chifatso.
Musatengeke mtima ndi kuyamba kuonetsa khalidwe lofanana ndi yemwe akukutsutsaniyo
lomwe ndi loipa. Musabwezere choipa ndi choipa – Aroma 12:17-20. Musachiyese chosangalatsa ngati mugonjetsa mnzanu molimbana.
7) Funani Mzimu Woyera kuti uthandize inu ndi anzanu, chifukwa umodzi ndi wa Mzimu –
Aefeso 4:3; Agalatiya 5:22,23; 2 Akorinto 13:14; Luka 11:13.
8) “Gonjetsani choipa ndi chabwino” – aroma 12:21. Pemphererani adani anu. Kumbukirani
chitsanzo chomwe Ambuye Yesu anaonetsa pamene anazunzidwa ndi kunyozedwa – 1
Petro 2:21-25. Perekani ka Mulungu zolinga zanu zonse, nthawi zonse chitani zabwino
ndipo wongolerani bwino mzimu wanu. Palibe chifukwa chokubvomerani kuchita zoipa
chifukwa choti winanso akuchita zoipazo. Kuchitidwa zoipa chifukwa choti muli ndi
mzimu monga wa Ambuye Yesu ndi phunziro lalikulu lomwe mudzayenera kuchita.
9) Phunzirani kunena zoona zokhazokha momveka bwino ndi mwachikondi. Aefeso 4:15.
Mungathe kuyankhula muli monse mungafunire ngati muyankhula mokhoza ndi
mwabwino. Yankho loperekedwa modekha limatha kuthetsa kulimbana – Miyambo 15:1.
Mzimu amatithandiza kuyankhulana ndi kumvana bwino mothandiza ndi moombolana.
10) Zoyambitsa kulimbana zina ndi zoti mutha kungozinyalanyaza ndi kuziiwala ngati
mwayesa yesa njira zinazo – Nehemiya 6:1-13.
Umodzi 21
11) Ngati abale ali otsamira ndi kukhulupirira kwambiri pa miyambo ya makolo komabe
kwinaku ali nacho chikondi cha pa Mulungu, ziripo njira zina zomwe inunso mungachite
popanda kuwalakwira, kapena palinso njira ndi nzeru zina zomwe mungathe kukwaniritsa
zabwino pamene mukudikira ifike nthawi yoti njira itsekuke. Mudziganizira za
chikumbumtima cha abale monga momwe mungathere (Ngakhale kuti izi zichitike
molingana ndi udindo wanu pamaso pa Mulungu kuti mukathe kufikira otayikawo munjira ya uzimu.)
12) Samalirani pa zomwe mumayankhula kwa anthu pokhuza za omwe amakutsutsani. Ngati
simusamala mungathe kufesa mbewu zamnyozo chifukwa anthutu amamva zinthu
mwachangu. Mudziwenso kuti zomwe muyankhulazo tsiku lina zidzapeza yemwe
mukumunenayo.
13) Muzolowerane ndi osadziwa ndi ofooka powaphunzitsa modekha ndi mofatsatsirira bwino,
kuwadyetsa ndi kuwaonetsera chitsanzo chabwino. Pamene ofookawo ayesera kuchitako
bwino, ayamikireni.
14) Dandaulirani mfundo zomwe inu ndi okutsutsaniwo mungathe kugwirizana ndipo
mulimbike kugwira ntchito mu mfundo zimenezi ndi mtima wonse.
15) Taphunzirani ndi kuona momwe Yesu ndi ophunzira ake anamchitira ndi nthawi zobvuta
zomwe anali kutsutsidwa. Kodi ndi nthawi ziti zomwe anali kukana kugonja? Ndipo ndi
nthawi ziti zomwe anali kulolera kufooka kwa anthu?
16) Samalirani mwakuopa Mulungu momwe muweruzira okutsutsani, makamaka pa zokhudza
maganizo awo – Yohane 7:24; Mateyu 7:1-5; Yakobo 2:12,13. samalirani kuti
musafulumize kukhulupirira zomwe mumva za miseche yochokera kwa olimbana nanuwo.
Fufuzani kokwanira musanagwiritse ntchito zokumvazo.
17) Chenjerani kuti pasayambike magulu kapena timabungwe pakati pa abale ndi alongo
chifukwa chokhala ndi maganizo osiyana pakulimbana. Musakolezere moto pakutsutsana
ndi kulekana kwa anthu.
18) Pezani malangizo kwa oyera mtima odalilika ndi atsogoleri a akulu.
19) Musapangitse banja lanu kuti likhale ndi mkwiyo wa pa omwe mutsutsana nawowo kapena
mpingo chifukwa kayankhulidwe kanu. Phunzirani kupempherera ndi kufunira adani anu zabwino pamodzi ndi banja lanu lonse (pali nkhani zina zoti zimuyenera kukambirana ndi
ana anu aang’ono ndiponso zina ngakhale aakulu amene).
20) Potsiriza, pamene mwa ona kuti kutsutsako kukuchokera mkati weniweni mwa choipa,
ndipo mfundo zofunikira kapena mtendere wa ntchito za mpingo ungathe kusokonezeka,
iripo tsopano nthawi pamene zonse zalephereka yochotsera choipacho ndi kufotokozera
momveka bwino, posiya matsutso agwere komwe ayenera kugwera – Mateyu 23;
Machitidwe 13:6-12; Agalatiya 2:11-13.
a. Muyenera mutsikize kuti mukulondola ndi kuti mfundo za mpingo zikuopsezeka.
b. Tengani maganizo a anthu a mtima wolondola.
c. Mukhale okonzekera kulandira zotsatira zake.
d. Yesetsani kupanga zoti zisasokoneze kwambiri mpingo (mwa chitsanzo, ngati musiya
utumiki wanu, ndi chanzeru kuchoka ndi kumakasonkhana ku malo ena ampingo
womwewo wa Yesu koposa kukhala chida chothandiza kugawa anthu).
e. Yesetsani kuti ubale wanu wonse ukhale wosaonongeka kuti ubale wanunso ndi
Mulungu usaonongeke
Umodzi 22
21) Perekani moyo wanu ndi zolinga zanu kwa Mulungu – 1 Yohane 4:4; 1 Petro 2:23;
Masalmo 23:5.
22) Lolerani kulakwiridwa kapena kulakwira chifukwa cha Mulungu ndi cholinga chake, koma
osati chifukwa chofuna kukwaniritsa zolinga zanu. Muzidziwa kusiyana kwake!
Mu utumiki, zambiri ndi zosautsa ndi zokhumudwitsa. Komabe zimenezi sizingafanizidwe ndi chisomo cha
Khristu Yesu chomwe chaperekedwa kuti chitithandize ngakhale ndi chisangalalo chomwe utumiki
wopambana umabweretsa ku mizimu ya anthu.
Phunziro 5: Umodzi mu Mpingo wa Pamalo Gawo 1: Mzimu wa Utumiki wa Khristu
Chinthu chapamwamba chopusa zonse pa mpingo womwe ndi wogwirizana kapena pa banja ndi moyo
wotumikira wa Khristu. Mabvuto ambiri m’mipingo ndi m’mabanja amabadwa kukuchokera ku uchimo,
kudzikuza, ndi kudzikonda. Akhristu ali nayo njira yamphamvu yothetsera zimenezi kudzera m'moyo wa Yesu womwe uyenera kumabadwa m’miyoyo yathu. Palibe njira zopezekeratu “za mayankho ododometsa” ku
mabvuto am’mipingo ndi m’mabanja ndiponso palibe lonjezo lirilonse lomwe lingabweretse kusintha kwa
zinthu popanda kudzipereka kwa Ambuye kuti atilamule. Koma pokhala pansi pa iye monga Ambuye wathu
ndikutsatira chitsanzo chake, mipingo yathu ndi mabanja athu angathe kukhala ogwirizana monga momwe
Mulungu anakonzera! Mu phunziro loyambali tidzayang’ana za maziko a umodzi, moyo wotumikira wa Yesu.
1. Khristu anali nawo ufulu monga Mulungu wokhala kumwamba – Afilipi 2:5-7.; Yohane 1:1,2,14; 17:5.
2. Khristu anasiya padera ulemerero wake mwakufuna kwake ndi cholinga chofuna kuti atithandize –
Afilipi 2:5-8. “Iye anadzikhuthula yekha
A. Iye anabvomera pa chiyambi pomwe ndi Mulungu kuti adzachita zimenezi - Ahebri 10:4-7;
tawerengani Aroma 15:3; 2 Akorinto 8:9; ndipo mufanizire.
B. Izi zimafuna mphamvu zambiri koposa kuumirira ufulu wathu.
C. Pamene tiri kuphunzira chikondi chosadziganizira wekhachi, cha Khristu, moyo umenewu
wotumikirau, tidzatha kukhala ndi khalidwe lomwe mwa njira zina sitikanatha ndi kulikwanitsa
m’mabanja mwathumo.
3. Khristu anakhala wotumikira (kapolo) – Afilipi 2:5-8.
A. Pobadwa monga munthu – Yohane 1:14; Mateyu 1:23.
B. Ponyamula zolemetsa ndi zosowa za anthu ena – Mateyu 8:1-4; Luka 7:11-15; Yohane 8:2-11;
Marko 6:31-34; Mateyu 15:32; Luka 13:10-17; Yohane 5:1-15; Yohane 4:1-38; Luka 22:24-26;
Yohane 13:3-17; Luka 23:39-43.
4. Yesu anadzichepetsa yekha ndipo anamvera mpaka imfa ya pamtanda – Afilipi 2:8.
A. Uku kunali kudzikhuthula kwake kwa Yesu m’moyo wake kwachiwiri.
B. Imfa yake inali yodzipereka yekha, kutisenzera zolakwa zathu pamene ife tinali olephera –
Yesaya 53:3-6.
5. Popeza anataya ulemerero wake wonse kuti apulumutse ena, Mulungu anamukweza iye kopambana ndi
kumubwezera zonse mochuruka. – Afilipi 2:9-11. Ngakhale pakali pano akutisenzerabe zolakwa zathu
ndi kutipempherera – Ahebri 7:25; 1 Petro 5:7.
6. Yesu akutiimiranso ife kumoyo womwewo wodzikhuthula, wotumikira ndi cholinga chofuna
kupulumutsa.
Umodzi 23
A. Kuti tinyamule zolakwa za ofooka ndi kuti tisadzikondweretse tokha – Aroma 15:1-3;
tawerengani Machitidwe 20:35; 2 Akorinto 12:15.
B. Kuti tikonde ena monganso Khristu anaconda ife – Yohane 13:34; tawerengani 1 Akorinto 13;
Yohane 15:13; 10:11.
C. Kuti tidzikhuthule ndi kunyamula mtanda wa Khalidwe lofuna kuombola ena – Mateyu
16:24,25.
1) Njira yekhayo yotsatira nayo Khristu.
2) Dzikhuthuleni, osangoti machimo okha – Mateyu 16:24; Aroma 6:6; Agalatiya 2:20.
3) Kunyamula mtanda tsiku ndi tsiku – Luka 9:23
4) Ngati titaya moyo wathu chifukwa cha Yesu ndi cha ena onse, timaupezanso.
Mau otsiriza: Kodi ndingathe bwanji kukhala wopulumutsa monga anamchitira Yesu?
1. Mthane ndi zoyambitsa kupunthwa ndi kuchimwa m’moyo wanu – Mateyu 18:6-9.
2. Lapani ndi kusiya moyo wodziganizira nokha ndi kumaukonza nthawi iriyonse pamene muona kuti ufuna
kuyambiranso.
3. Yang’anani kwa Yesu ndi uthenga wake ndipo pemphani thandizo la Mzimu wake – 2 Akorinto 3:18;
Luka 11:13.
Kusinthika kwanu kudzathandiza kuti banja lanu lonse lipulumutsidwe ndi kukonzeka. Nthawi zambiri banja
limasinthika chifukwa cha kusinthika kwa munthu mmodzi wapabanjapo.
Gawo lachiwiri: Utsogoleri Wotumikira.
Mawu oyamba: Yesu anaphunzitsa kuti utsogoleri wa mu ufumu wake ndi wosiyana ndi utsogoleri wa dziko
lapansi.
Ndipo kunakula kutsutsana mwa iwo, ndani wa iwo ayesedwe wamkulu. Ndipo anati kwa iwo, mafumu a anthu
amitundu awachitira ufumu; ndipo iwo amene awachitira ulamuliro anenedwa, ochitira zabwino. Koma
sipadzatero ndi inu; komatu iye ali wamkulu mwa inu akhale ngati wamng’ono; ndi iye ali woyamba, akhale ngati wotumikira. Pakuti wamkuru ndani, iye wakuseyama pachakudya kapena wakutumikirapo? Sindiye
wakuseyama pachakudya kodi? Koma ine ndiri pakati pa inu monga ngati wotumikira. – Luka 22:24-27.
Koma amene aliyense akafuna kukhala wamkulu mwa inu, adzakhala mtumiki wanu; ndipo amene aliyense
akafuna kukhala woyamba mwa inu, adzakhala kapolo wanu; monga mwana wa munthu sanadza
kutumikiridwa koma kutumikira ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri. – Mateyu 20:26-28.
Wetani gulu la Mulungu liri mwa inu, ndi kuliyang’anira, osati mokakamiza, koma mwa ufulu, kwa Mulungu;
osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu; osati monga ochita ufumu pa iwo a udindo wanu, koma okhala
zitsanzo za gululo. – 1 Petro 5:2,3.
1 Yesu ndiye chitsanzo chathu cha utsogoleri wotumikira – Afilipi 2:5-11; Mateyu 20:28; Aroma 15:1-3.
A. Momwe amachitira ndi unyinji.
B. Anasunga nthawi yoganizira anthu osowa ndipo nthawi zonse ankakhudzidwa kwambiri chifukwa ena
koposa momwe ankadziganizirira yekha.
C. Ankasamalira osauka, osawerengedwa, akunja ndipo ankapeza nthawi yokhala nawo pamodzi.
Umodzi 24
D. Sanadzikweza yekha kapena kutenga maulemu adziko lapansi.
E. Ngati anakwiya, chinali chifukwa cha Mulungu, osati chake ayi.
F. Kudzichepetsa kwake sikutanthauza kuti anali wofooka ayi. Iye anali mwamuna wolimba koposa
ndinso mphunzitsi wamphamvu yemwe sanaonekepo ndikale lonse. Nthawi zina ankakalipa, koma zinali zoonekeratu kuti zinkachitika m’chikondi, osati chifukwa cha iye mwini ayi.
G. Pamene anakomana ndi mtanda, anatumikira zosowa zathu koposa zofuna zake za iye mwini. Tonse
tikuitanidwa ku moyo woterewu, wokonda ndi kutumikira modzikhuthula – Afilipi 2:5-11; Aroma
15:1-3; Mateyu 16:24,25; Yohane 13:1-17,34.
2. Akhristu sadzaphunzira utumiki pokhapokhapo atsogoleri awo atawaonetsera utumikiwo monga momwe
Yesu anamchitira – Yohane 17:19.
3. Utsogoleri wotumikira sungatheke ku moyo wathu wauchimo wathupi. Ungatheke potsatira moyo
watsopano wofanana ndi Khristu womwe umaperekedwa ndi Mzimu Woyera:
A. Moyo wathu wathupi wa uchimowo umalamulidwa ndi kudzikonda, ndi kunyada – Agalatiya 5:19-
21. Aliyense amafuna kukhala wotsogola, kuti enawo azingotsatira zomwe ife tifuna basi. – Mateyu
18:1-4.
B. Mzimu woyera amabwereka mwa ife chipatso chatsopano cha moyo wofanana ndi Yesu – Agalatiya
2:20.
4. Kodi atsogoleri otumikira amaganiza ndi kuchita motani?
A. Utsogoleri wotumikira sudzikondweretsa okha koma umafunafuna ulemerero wa Mulungu ndi
kuonetsetsa kuti ena apeze bwino – 1 Akorinto 4:8a; Aroma 15:1-3; Yohane 3:26-30.
B. Umalakalaka ndi kukonzekera kutumikira anthu ndi Mulungu – Ahebri 13:17; 1 Petro 5:4; Yakobo
3:7; 1 Timoteo 3:1-7; Tito 1:5-9; 1 Samueli 12:1-3. Mtsogoleri saopa kutumikirana ngati ali
woyeneradi, wosankhidwa munjira yoyenera ndi yobvomerezeka. Mtsogoleri wotumikira saopa
kupereka malipoti okwanira a chuma cha mpingo kumpingowo. Iye amafunsa anthu kuti apereke
maganizo awo kwa iye pa za ntchito ya pampingopo. Mtsogoleri wofana ndi Yesu amabvomera
kudzudzulidwa kothandiza komwe kungathandize utsogoleri wake. Utsogoleri wamtundu umenewu
umabweretsa umodzi mumpingo, pamene utsogoleri wofanana ndi wadziko lapansi umabweretsa kugawikana mumpingo.
C. Utsogoleri wotumikira umapulumutsa.
1) Kutumikira mwachikondi, ndi mopanda kudzikonda kumachita bwino, kumawala bwino m’dziko
lodzitumikira lokha. Kudzikonda ndi kunyada ndi chizindikiro cha moyo wathupi wa uchimo.
2) Anthu analondola Yesu chifukwa anamva mumtima mwawo kuti iwo ofunikira kwa iye. Iye anali
wokhudzidwa kwambiri pa za moyo wawo, osati pa za moyo wake.
3) Anthu amakopeka ndi kukokeredwa ku moyo wokonda, wosadzikonda ndipo amafuna atakhala
ndi khalidwe lotere.
4) Chikondi chotumikira chimasintha anthu pamene palibe china chirichonse chomwe chingathe
kuwasintha – Yohane 12:32; 1 Yohane 4:19; 2 Akorinto 5:14; 1 Petro 3:1-6.
D. Umathana ndi zolimbana mwa chiombolo.(Satana amagwiritsa ntchito kutsutsana moononga, koma
Akhristu odzala ndi chisomo amatenga kutsutsana ngati mwayi wowathandiza kuti aphunzire ndi
kukula.)
Umodzi 25
1) Sutenga kutsutsana mwa iwo okha. Mtsogoleri wotumikira anadzikhuthula. Nthawi zina Yesu
ankakwiya mwa chifuniro cha Mulungu, koma simunamuona akukwiya mwa chifuniro cha iye
mwini. Mtsogoleri wotumikira amaphunzira kuchokera mukudzudzulidwa pa za Madera omwe
iye ayenera kukonza – Mateyu 7:3-5, ndiponso amaphunzira kungosiya kudzudzula kopanda
phindu kupite, chifukwa anali ndi zinthu zambiri zofunika kuti achite poyamba koposa kudzitcha
wachilungamo. Iye amadziwa kuti onse otsutsana naye si adani ake; Satana, zofooka za munthu, kusadziwa ndiwo ali adani ake.
2) Umalumikiza koposa kusiya monga munthu wathupi wa zamdziko angachitire. Mtsogoleri
wotumikira sayembekezera kuti munthu winayo ndiye ayambe.
3) Pochita ndi wotsutsa, suchita monga mwa nkhondo kuchititsa kuti winayo akane kukambirana
ndi cholinga chodziteteza. Umafikira mwa chilungamo koma modekha poika njira za chimvano –
Agalatiya 6:1,2; 2 Timoteo 2:24-26.
4) Pokonza zoonongeka umagwiritsa ntchito dongosolo lomwe Yesu anatipatsa lothetsera
makangano mwachangu asanakule ndi kuononga kwakukuru. Cholinga choyambirira sichofuna
kuweruza ndi kudzudzula ayi koma kuthetsa kusiyana kwa maganizo kuti asachitinso monga
mwa chifuniro cha Satana – Mateyu 18:15-17; 5:23,24; Aefeso 4:26-27.
E. Mtsogoleri wotumikira amafikirika. Mtsogoleri sachepsa maganizo a ena kapena kukana Mafunso
awo koma amamvetsera ndi kuyankha modekha ndi kudzisunga konse – Yakobo 1:19,20; 3:17;
Aefeso 4:29; 2 Timoteo 2:24-26; 1 Petro 3:15; Afilipi 2:3; Akolose 4:6. Tingathe kulimbikitsa
dongosolo la Mulungu popanda kukhala oweruza aukali.
F. Utsogoleri wotumikira umalemekeza ndi kulolera maganizo osiyana ndi ake a ena pa nkhani zina
zomwe chifukwa cha umunthu wathu wolephera, sitingathe kuzimvetsa ndi kuzimasulira bwino,
zomwe siziri zofunika kwenikweni ku chikhulupiriro chathu. Nkofunika ndipo nkoyenera kuti
Mkhristu aliyense wokhulupirika ndi wodalilika aone zinthu zimenezi mosiyana. Mtsogoleri
wotumikira amadziwa kuti iye wangokhala munthu mmodzi m’gulu la anthu otumikira mofanana,
okhulupirira olemekezeka, ndipo sadzakakamiza anzakewo kuti akhulupirire ndi kukhala ndi
maganizo onga akewo pa zinthu zomwe zioneka monga zochepera mphamvu, kapena kuti akhale ndi
maganizo ofanana ndi ake pa momwe iye amvera Baibulo.
G. Utsogoleri wotumikira sulamulira ena kuti atsatire njira yake. Koma mtsogoleri amamvera ndipo
amakamba poyera, pofotokozera chifukwa chomwe iye amaganizira munjira yakutiyakuti. Amadziwa
kuti sichikhala chinthu wamtengo wapatali ngati angomvera mongomukondweretsa koma amvere mochokera pansi pa mtima wawo. – 2 Akorinto 3:17. Anthu omwe amatsutsana naye mwa
chilungamo amalandirabe ulemu wake.
H. Umakonda kukopa ndi kudandaulira momwe ungathere koposa kulamula – 2 Akorinto 13:10.
Utsogoleri weniweni suchita kupemphedwa m'njira iyiyonse. Umapezeka polandira ulemu wa iwo
omwe tiwatsogolera.
I. Umakhala ndi chidwi chogawana ntchito yotsogolera ndi kulekera nsakali kwa m’badwo wobwerawo
– 2 Timoteo 2:2.
1) Mipingo yambiri ikufa chifukwa asogoleri ake onse akula ndipo ayamba njira zawo zawo ndipo
akukanika kupereka mwayi kuti anthu aang’ono ndi maganizo a anthu ang’ono abwere
mumpingo.
2) Atsogoleri otumikira nthawi zambiri, ndi cholinga, amaphunzitsa atsogoleri aang’ono ndi
kumagawana nawo ntchito ndi maudindo kuphatikizapo ufulu woti athandizepo kukonza
dongosolo la tsogolo la mpingo (atsogoleri omwe lero akulawa, nawonso ankafuna ufulu
womwewo pamene anali kuyamba kumene).
Mawu otsiriza: Maganizo ndi njira za Mulungu ndi zosiyana ndi zathu – Yesaya 55:8,9. Utsogoleri womwe
cholinga chake ndi kutumikira ndi wamphamvu kuposa utsogoleri wina wamtundu uliwonse womwe
Umodzi 26
mungaudziwe. Unamthandiza Yesu kusiya chitsanzo chosaiwalika mpaka kalekale padziko lapansi, ndipo
udzatithandiza kutsogolera mpingo mwa mphamvu ndi mofuna kubweretsa anthu kuchiombolo, kuti tithe
kupyola ku zopunthwitsa zomwe sitikanatha kuzidutsa mu njira iriyonse, ndi kuwakopa anthu kuti akhale ndi
chidwi cholondola ndikutsatira. Kumvetsa zinthu zimenezi nkwamtengo wapatali koposa dongosolo lina liri
lonse.
Gawo lachitatu: Kupasirana Nsakali: Kumwetulirana Kapena Kuponyerana Nkhondo? (Kupewa Kulimbana kwa Pakati pa Atsopano ndi Akale.)
Sauli anamponyera nkondo Davide, chifukwa sanakondwere poganiza kuti Davide adzalowa ufumu wake tsiku
lina. Herodei anapha unyinji wa makanda a ku Betlehemu pamodzi ndi akubanja kwake komwe posakondwera
ndi kubvomera ganizo loti iye sadzakhala wolamulira mpaka kale kale, ena adzayeneranso kudzatenga malo
ake.
Kumbali inayi, tiona Eli wansembe wamkulu, mosiyana ndi omwe tamvawa, akudzipereka yekha pophunzitsa
Samueli mnyamata kuti adzakhale mtsogoleri wamawa. Eliya adaphunzitsa Elisa kuti adzatenge malo ake ndi
kupitiriza ntchito yake mtsogolo. Nawonso Elisa ndi Samueli anaphunzitsa pa sukulu yokonzekera aneneri
amtsogolo. Mtumwi Paulo analimbikitsa gulu la alaliki ang’onoang’ono ndi aphunzitsi omwe oti adzapitirize
kufalitsa uthenga wabwino pamene Paulo amwalira. Anali wokondwera chifukwa cha iwo. Ndipo anali
kumawapempherera. Kwa Timoteo monga wophunzira wake wopambana, anamlembera kuti, “zonse zomwe
wandimva ndikulankhula pamaso pa mboni zambiri uikize kwa anthu okhulupirika amene adzakhoza
kuphunzitsanso ena.”
1. Ife omwe tagwira ntchitoyi kwa nthawi yaitali tikadakonda tikupitirizabe kugwira ntchitoyi.
Sitikondweretsedwa kumva kapena kuganizira zakufooka kwathu. Koma tsopano taonani tisanazindikire za
kuzilala kwa mphamvu zathuku, timafika mundime yoti mphamvu zathu zimayambabe kulowa pansi.
Mphamvu zathu zimayamba kulephera. Timayamba kumangobwereza zomwezo zakale m’malo
moganizirabe njira zina zatsopano. Timayamba kusowa mphamvu za achinyamata kuti ayeserere ndi
kuganizira ndi kumanga. Timangoyamba kumayang’ana za m’mbuyo m’malo moyang’ana zamtsogolo. Sitithanso kumvetsa za makono zomwe ndi zofunikira. Timatopa msanga.
Choncho tiyenera kusiyira ntchitoyi ku m’badwo winawu. Koma tiri nawo mwayi wosankha njira yake
yochitira zimenezi. Tingathe kusiyira nsakali ya ntchitoyi mwa chisomo ndi mwanzeru kapena tingathe
kumakana zimenezi ndi kumangokhalira kulimbana ndi achinyamata, kumawatenga ngati adani. Pamene
tisankha njira imeneyi mpingo umabvutika ndipo umalipira dipo loopsa kwambiri.
2. Mulungu safuna kuti mpingo ugawikane pakati pa mibadwo mibadwo. Monga momwe uthenga wabwino
uyanjanitsa ndi kulumikizira mitundu ya anthu yosiyanasiyana, amuna ndi akazi, anthu azikhalidwe
zosiyana, umalumikiza ndi kuyanjanitsanso aakulu ndi achinyamata m’chikondi cha kwa aliyense ndi
cholinga. Ngati kukula msinkhu kuli nazo zofooka zake, kuli nachonso chuma chamtengo wapatali, ndicho
nzeru. Achinyamata ayenera kumvera mwa ulemu malangizo a achikulire. Nawonso achikulire ayenera
kulemekeza zolakalaka ndi zofuna za achinyamata. Akulu ndi achinyamata si adani; onsewo ali m’gulu
limodzi. Mphamvu zawo ndi zofanana.
A. Uwu ndi mutu wobvuta ndi wotenga mtima. Komabe ndikhulupirira ndiri nawo ufulu woti ndinene
ndithu pankhani imeneyi popeza nanenso ndi kuyandikira nthawi yoti ndipume, ndakhala woyang’anira
kwa nthawi yaitali ndipo ndaukonda mpingo. Ndakhala ndi kupemphera kuti ndilandire nzeru
yolankhula mosasonkhezera moto woyambitsa makangano koma kuti ndithandize ife atsogoleri
achikulire kuti tidziunike tokha ndi kukonza malingaliro athu ndipo potero tilandire udindo wathu
wauzimu wa kuti tithe kusintha mwa chisomo, ntchito ya Mulungu pakati pa mibadwo ndi misinkhu
yosiyana.
B. Umenewu ndi udindo wathu chifukwa 1) Ndife okhwima, olimba omwe tiyenera kunyamula zofooka
za ochepa mphamvu; ndipo 2) Ndife omwe tikutsogolera ndipo tiri ndi mwayi wosankha momwe
ntchito ipitire patsogolo.
C M’mipingo ina atsogoleri akupatsirana bwino nsakali ya utsogoleriyi ndipo anthu aakulu ndi
Umodzi 27
achinyamata akugwirira ntchito pamodzi. Koma m’mipingoyo yambiri zafika posukusa ngati
sikuonongeka kumene. Pamene kugawikana pakati pa akulu ndi achinyamata ndinso kulimbana
kubuka, achinyamata a amakambirana ndi achinyamata anzawo za achikulire ndipo achikulire nawonso
amakambirana ndi achikulire anzawo za achinyamata, ndipo palibe gulu lomwe limayankhula gulu
linzakelo. Nthawi zambiri amayankhana monga athupi amachitira, molimbana, mopanda moyo
wololerana wa chikondi monga momwe Akhristu otsogoleredwa ndi Mzimu amachitira.
Ndi kumbukira nthawi ina yomwe ndinali kukambirana ndi atsogoleri achikulire ku tauni ina yake,
pamene ndinali kuwalimbikitsa kuti asamafulumize kukhulupirira miseche yopanda umboni yonena
ogwira ntchito mu mpingo achinyamata, koma alumikizane nawo modekha poopa kuti mwina
achinyamatawo angayambe kusafuna kukhala pafupi ndi iwo. Ngati ife achikulire tipitiriza kukakamira
udindo, ngati tikaniza achinyamata mwayi woti athandize kutsogolera mpingo, ndiye kuti tidzathawitsa
achinyamata abwino pamodzi ndi nzeru zawo zomwe zikanadzathandiza mpingo mtsogolo.
3. Nchifukwa chiyani zimakubvutani kusiyira nsakali ya utsogoleri kuti muthandizane kutsogolera?
Choipitsitsa kwambiri ndi choti mwina kumangokhala kulimbanira ndi kukanirira udindo, zosasiyana ndi
zomwe Sauli kapena Herodi anaganiza zija. Tonsefe tili nako kufooka koganiza monga mwa thupi. Ngati
tizindikira moyo umenewu mwatokha, nkoyenera ndi kofunikira kwambiri kulapa, kudzichepetsa,
kufewetsa mitima yathu ndi kusintha mthandizidwa ndi Mulungu! Komabe nditha kuganiza kuti ambiri a
atsogoleri athu amakhala ndi cholinga kapena zolinga zabwino zowapangitsa kuti asachite zinthu
mofulumiza. Zina za zolingazo ndi izi:
A. Kukayikira kutuma ena. Mbali ina yakhalidwe limeneli ndi kudzitamandira (“ndine ndekha wodziwa
bwino”), komanso mbali ina ndi maganizo ongofuna kuti ntchitoyo igwiridwe bwino. Tiyenera
kudziwa kuti atsogoleri achinyamata sadzakhwima ndi kulimba ngati sapatsidwa mwayi weniweni woti
aphunzire kutsogolera. Tiyenera kuwapatsa mwayi woti okha aone chochita molakwitsa monganso
tinkachitira ife munthawi zathu zoyamba zija. Nthawi zina tidzadzidzimuka Poona mphatso ndi nzeru
zomwe sitimayembekezera kuti ali nazo.
B. Kukhudzidwa ndi tsogolo la mpingo. Kwa ambiri a ife atsogoleri ampingo achikulire, mpingo wakhala
monga moyo wathu. Tidzalolera kutaya moyo wathu chifukwa cha mpingo. Achinyamata amaonetsa
zikhulupiriro zina zomwe sitikondwera nazo. Timaiwala kuti nafenso pamene tinali kukula kumene
mumpingo tinkachita zomwezo, ndipo zinkatero ndi mibadwo yonse yakumbuyoku.
Masiku ano kusintha kukuchitika mowirikiza. Koma m’badwo uliwonse unaziganizira wokha
mamvedwe ake a zomwe Baibulo liphunzitsa. Timayesetsa kuphunzitsa ana athu kuti adziopa ndi
kulemekeza Mulungu kuti akonze okha chikhulupiriro chawo. Timakhumbira atakwera m’mapewa athu ndikudziwa zambiri koposa ife eni, koma taonani akateronso timayambanso kuganiza zina ndi
kusowa nawo mtendere. Kodi nanga, ngati Mulungu munjira zina, athandiza ana athuwa kutulukira
nzeru zina zomwe ife sitinadziwa? Kodi nanga monga Paulo wa ku Tariso titsutsa, ndi kusowetsa
mtendere pa ntchito yomwe Mulungu waikonza? Kodi nthawi zina timaponya mivi kwa anthu omwe
Mulungu wawasankha?
Kukhudzidwa kwathu pa nkhani ya mpingo kumakhala kolimba ngati tidzipereka ndi kukumbukira kuti
tiri nacho choonadi chonse ndipo maganizo ena onse abwera pamwamba pa chimenechi ndi monga
nkhamba nkamwa chabe (zakumva). Titha kumalepherabe kumvetsa kwenikweni za zomwe Baibulo
liphunzitsa za chisomo ndi zomwe Mulungu atilamulira pa kulemekezana ngakhale pamakhala
kusiyana maganizo “pa mfundo zina zazing’ono.” (Aroma 14,15). Nthawi zambiri takhala tikubvutika
polimbana ndi nkhani zazing’ono zoti titha kungozisiya, zomwe sitiyenera kuzitenga monga
zoyambirira kuganiziridwa, ngati ndi zofunikira kwambiri pa chikhulupiriro chathu. Inde ndiyenera
kumvera chikumbumtima changa, koma lemba liti ndidzatha kupulumutsidwa ngakhale ndalakwitsa pa
mfundo zina zomwe zagawanitsa okhulupirira. “Mubvomerezane wina ndi mnzake, inde, monganso
Yesu anakulandirani inu….” Izi zingapangitse kuti kukhale kosabvuta kukhalirana pamodzi ndi
achinyamata omwe ayenera kupatsidwa udindo wotsogolera. Komanso sitiyenera kumangololera
maganizo awo alionse; kuwamvera kwathu sikutanthauza kukhuthula maganizo athu onse ayi; pali zina
zoti tidzimusiyira Mulungu.
Umodzi 28
C. Kusokoneza pakati pa tanthauzo lenileni la mpingo logwirizana ndi Baibulo, ndi momwe titanthauzira
mpingo mogwirizana ndi chikhalidwe chathu cha makolo. Pamene Mulungu wamanga zinthu zina kuti
tisazisinthe, palinso njira zina zambiri zomwe watipatsa mwayi wosankha njira yotikondweretsa
malingana ndi nthawi ndi zinthu zotizungulira. Dongosolo la zambiri zomwe mpingo umachita lagona
m'gawo limeneli. Pankhani ya ufulu wosankhawu, m’badwo uliwonse umasintha mpingowo kuti uthe
kugwirizana ndi kuchita bwino mogwirizana ndi zofunikira za nyengo. Ife omwe takula tiyenera kubvomera kuti momwe chikhalidwe chathu chigwirizanira ndi kumvera tanthauzo la mpingo
chidzatha monganso momwe zakhala zikuchitira ndi mibadwo mibadwo yapitayo. Koma kufunikira
kwa mpingo monga mwa malembo kudzapitirirabe ndipo kudzalimbalimbane; zipata za akufa
sizidzaulaka. Ine ndatengeka ndi kusanalatsidwa ndi chikhulupiriro chopambana ndi kudzipereka
komwe kuli mwa m’badwo wa achinyamata.
4. Kodi tingasiyirane bwanji nsakaliyi mwa chimwemwe ndi kuchepetsa kulimbana pakati pa achinyamata
ndi achikulire?
A. Titha kumaonjezera atosogoleri ena atsopano mumpingo. Atsogoleri anzeru sadikira mpakana zinthu
zifike pofuna kuonongeka chifukwa cha mabvuto autsogoleri. M’malo mwake amalimbikitsa nthawi
isanafike, kugwirira ntchito pamodzi ndi achinyamata nthawi zambiri. Choncho kukonzekeratu
utsogoleri mwa choonadi kumaimirira mpingo wonse ndiponso maganizo a achinyamata amakhala ndi
gawo pa zamtsogolo la mpingo.
Podziwa kuti atsogoleri sakhwima tsiku limodzi, choncho pamafunika kukhala ndi cholinga chofetsa
mbewu ya atsogoleri amtsogolo ndi akazi awo nthawi isanafike. Ichinso chitanthauza kuti gawo la
utsogoleri lomwe liperekedwe kwa achinyamatawo liyenera kukhala leni-leni. Ngati mtsogoleri kapena
atsogoleri akale angodziikirabe okha mphamvu zina, atsogoleri atsopanowo sachedwa kutulukira
bvutoli. (choona ndi chakuti, gulu la atsogoleri lakhala ndi mibadwo yosiyana-siyana, ndi nthawi
zochepa mwinanso osachitika kumene kuti pakhale kugawanikana pakati pa misinkhu yosiyana.)
B. Ife omwe tiri achikulire pa zaka tiyenera kumamvera mwa ulemu maganizo a achinyamata ndi
kumaganizira maganizo awo ngakhale tikulekana ndi maganizo awo. Tinayenera, ndi nthawi yaitali
yomwe takhala padzikoyi, kukhala titadziwa momwe tingachitire modekha ndi moganizira bwino.
Koma ngati nthawi zomwe timangowaikira maganizo athu ndi kumangowakhumudwitsa,
timangowatalikitsa nafe ndipo m’badwo wawo kukhalanso pafupi nafe. Ndipo ngati achinyamata
amveredwa popanda kubvutikira, ndiye kuti kukhala kosabvuta kuti amvere nzeru za achikulire.
C. Titha kumabweretsa pang’ono pang’ono kusintha kwa muyezo woyenera mwa pafupipafupi. Apatu ndi
kutanthauza kusintha kwake kobvomerezeka, kofunikira, kusintha kukhala molingana ndi chikonzero cha Mulungu komwe mpingo wakhala akuchita kuyambira mibadwo yoyambayo mpaka tsopano ndi
cholinga choti mpingo ukhale wolimba ndi kutha kufikira otayikawo. Ngati sitikonza dongosolo
lomasintha mpingo pang’onopang’ono munjira yoti mpingo uthe kumvetsa, timafika pa ndime yobvuta
yoti achinyamata amafuna kusintha kochuluka kwa nthawi yomweyo ndipo mwa msanga koposa
momwe achikulire angathe kukonza. Nkhondo za pakati pa mibadwo zimauka, Akhristu amachoka
ndipo timaononga mphamvu ya mpingo yoti ukanachita kanthu. Atsogoleri anzeru amakonzeratu
zamtsogolo, osati ongochita modzidzimukira.
D. Ife atsogoleri aakulu misinkhu titha kulimbikitsa mizimu yathu ndi maganizo athu ndi mapemphero
pamodzi ndi maphunziro nthawi zonse. Kulimbana kungathe kuyamba nthawi iriyonse pamene anthu
achinyamata aposa achikulire pakamvetsedwe ka malemba ndi ubale kwa Mulungu. Ngati ena a
atsogoleri achinyamata ali ndi mfundo zoopseza, ambiri a iwo amakhala ndi mtima wolimbika zedi za
Mulungu ndi mawu ake. Ife atsogoleri akale nthawi zambiri timangotsamira pa “mfundo zochepa”
zomwe tinaphunzira kale m’masiku oyambirira aja, ndipo timangoona ngati basi, potero takwana,
palibenso china chomwe tikusowanso monga atsogoleri achikhulupiriro ndi okhulupirika. Ziphunzitso
zoyambirira, inde, ngakhale ndi zofunikira, si zilowa m’malo otifikitsa ku moyo wokhwima mwa Yesu.
Nthawi zina abusa amaonetsa kulephera ndi kusadziwa malemba. Ndipo mfundo za dzanja, ngakhale
zikhale zabwino chotani, si zokhazo zomwe ife atsogoleri tiyenera kudziwa. Kuti tithe kulemekeza
misinkhu yonse mumpingo, tiyenera kumvera lamulo la Yesu ndi mtumwi Paulo loti “tiyenera
Umodzi 29
kumvetsa za nthawi yomwe tiri.” Kodi ndiye kuti ndifedi atsogoleri oona ngati tikulephera monga
atsogoleri, kuphunzira ndi kupempherera zobvuta za makono zisanafike poopseza nkhosa zathu.
Ine monga munthu ndimakhuzidwa ndi momwe zakale zimabvutira atsogoleri achinyamata. Komatu zomwe
tibvutika nazo lero ndi zomwe tikubvutika nazo kale. Ngati ena akubvutika ndi zochitika zimenezi, ife akale
ndi omwe timathandiza kukhazikitsa zimenezi. Zomwe tiwasiyira achinyamata sikuti ndi zoipa kwenikweni. Ayenera kumakumbukira kuti tidawaphunzitsa kukonda Mulungu ndi mawu ake. Koma pamene tikuwasiyira
nsakali imeneyi, tikhale ndi chidwi chotani choonetsetsa kuti tipewe zomwe zimapangitsa kuti achinyamata ndi
ongophunzira kumene apunthwe! Tikhale osamala bwanji kuti tipewe mafano akale omwe ankathawitsa
achinyamata: kukhulupirira zinthu zosachitika, magawano osafunika ndi osatsatira malemba, kulimbikira pa
zinthu zazing’ono, kusokoneza pakati pa maganizo athu ndi malemba, kuchititsa kuti ziphunzitso ndi
zikhulupiriro zikhale amphamvu ndi zofunika kuposa Mulungu mwini.
Chitsanzo chopambana ndi chamtengo wapatali chochokera m’Baibulo cha kusiyirana muuni kwabwino ndi
cha Yohane Mbatizi. Pamene khamu linayamba kusintha ndikuyamba kutsata Yesu, Yohane anakondwera ndi
zimene Mulungu anali kuchita ndipo anati, “Munthu amalandira zokhazo zomwe iye walandira kuchokera kwa
Mulungu … Iye ayenera akule; ine ndikhale wamng’ono.”
Ndinamva ulaliki wina wosasunthika, wochirimika, wodzipereka ndi chikhulupiriro chonse, akulankhula pa
maphunziro zaka zapitazo. Moyo wake ndi chitsanzo chomwe Mulungu amafuna kuchokera kwa atsogoleri
aakulu ndi akale. Kwa ogwira ntchito achinyamata ananena mawu otere: “Ifetu tsopano kuno nkukula. Tiyenera
kuyang’ana kwa inu kuti mupitirize ntchito. Tilandireni udindowu. Tumikirani Mulungu mokhulupirika.
Maganizo anu ena atha kutibvuta ife omwe tiri akale. Komabe musaope kuchita zomwe mukukhulupirira kuti
Mulungu ndiye afuna kuti inu muchite kuti mubale zipatso. Iye adzakhala nanu monganso wakhala ndi ife.”
1. Kulandirira Muuniwo
Ngati nsakali ya utsogoleri ikapatsidwe kapena kusiyiridwa kuchokera ku mibadwo umodzi kupita ku
m’badwo winawo payenera pakhale wolandira wofunadi ndinso wopereka wofunadi. Zimadabwitsa kuti
m’mipingo mwina mulibe anthu ofunadi kulandira katundu wodzipereka wa utsogleri. Kodi zinthu ziri
chonchi chifukwa chiyani? Ndi chifukwa choti makolol asiya kuphunzitsa ana awo kulakalaka utsogoleri
wa Chikhristu kapena kuiona ntchito imeneyi ngati ganizo losiririka labwino? Kapena ndi chifukwa choti
sitiphunzitsa ndi kusula atsogoleri ndi cholinga cha mawa? Kapena ndi chifukwa choti anthu athu
atanganidwa ndi ntchito zawo zina zapadera? Kapena ndi chifukwa cha zobvuta zosiyanasiyana zomwe
asogoleri amakumana nazo masiku ano? Kapena ndi chifukwa choti timasasulira zoyeneretsa za
m’malemba munjira yomwe Mzimu Woyera sabvomereza?
A. Yambani kukonzekera tsopano lomwe. Mtsogoleri amakula pang’ono pang’ono monga mtengo
wamlambe kuchokera m'chiyambi chaching’ono kwambiri: Makolo omwe moyo wawo wonse
umadalira Mulungu ndi kumagawana malemba, mapemphero ndi utumiki pamodzi ndi ana awo
kuchokera adakali ang’ono. Makolo omwe nthawi zonse sangokhalira kutsutsa alaliki ndi abusa koma
amaonetsa kuthokoza pa ntchito zawo ndi kupangita ana awo kuti aganize kuti kukhala mlaliki kapena
mbusa ndi chinthu cha ulemu. Atsogoleri omwe analimbikitsa achinyamata kuti akule ndi kuphunzira.
Makolo achinyamata omwe amaphunzira ndi cholinga choti akule mwayiwo okha. Sukulu za Baibulo
zingakonze maphunziro a masiku ochepa a atsogoleri ozungulira dziko lino ndinso ena omwe afuna
kudzakhala atsogoleri. Abusa angathenso kutumiza achinyamata omwe akuonetsa kuti ali ndi tsogolo
labwino ku uzimu kumaphunziro “a maluso ena.” Ndi kuwalola kuti aphunzirebe pomakhala nawo pa
misonkhano ya abusa ndi kumatsagana ndi abusawo ku ntchito zoyendera nkhosa. Oyang’anira wa
angathe kutuma ophunzirawa ntchito zina.
B. Utsogoleritu siwa wina aliyense. Munthu yemwe akhumbira utsogoleri ayenera kuzindikira ndi
kudziwiratu za kudzipereka nsembe ndi udindo womwe umayenerana ndi utsogoleri. Pamene munthu
wina anafuna kutsata Yesu, Yesu anamchenjeza kuti, “nkhandwe ziri napo pogona pawo ndiponso
mbalame ziri nazo zisa zawo, koma mwana wa munthu alibe poikapo mutu wake.” Woyang’anira
yemwe amayang’aniradi adzasiya nthawi yochita zinthu zake yambiri kuti akonze dongosolo la ntchito
ya Mulungu ndi kutumikira anthu pa zosowa zawo. Adzasamala pochepetsa ufulu wake kuti
asapunthwitse ofooka. Yakobo akutichenjeza, “Musafune kukhala aphunzitsi ambiri a inu, abale anga,
Umodzi 30
chifukwa mudziwa kuti ife amene tiphunzitsa tidzaweruzidwa moposa enawo.” Atsogoleri ndiwo ali
ndi udindo ndipo ndiwo adzayankhe kwa Mulungu pa nkhosa zomwe iwo ayang’anira. – Ahebri 13:17.
C. Koma Mulungu ndiye amayang’anira iwo omwe alakalaka komanso ali ndi mphatso zamtsogoleri. Iye
amachita izi poyankha mapemphero athu a ogwira ntchito kuti tikolole zipatso. Iye amachita zimenezi
D. pamene anthu payekha payekha apemphera kuti Mulungu awagwiritse ntchito monga mwa mphatso
zawo.
E. Ndi chinthu chofunika kuti okalaka ntchito ya utsogoleri adzichepetse pansi pa ulamuliro wa Mulungu.
Ngati oyang’anira ndi atumiki “oyambira kuphunzitsa” anthu omwe akuoneka kuti ali ndi mphatso,
tiyenera kumvetsa bwino pamenepa kuti dongosolo limeneli silitanthauza kuti amenewa ndiye
angolowa ndi kukhala atsogoleri. Zotsatira zake ziyenera kusiyidwa m’manja mwa Mulungu. Ndipo
ngati mpingo ufunsidwa kutchula maina a atumiki ndi oyang’anira kuti aonjezedwe ku mpingo, iwo
omwe alandira mavoti ochepa, ayenera akukonzekeratu zisanachitike izi kubvomereza zomwe mpingo
wachita popanda kuwawidwa mtima. Mzimu Woyera ndi amene amapanga abusa mumpingo
(Machitidwe 20:28) ndipo imodzi ya njira zomwe amachitira zimenezi ndi yoyankhula kudzera
kusankha komwe mpingo umachita.
Pamene Mulungu aitana anthu ena kuti akhale atsogoleri, izi zimatsimikizika ku mpingo pamene ayesa
moyo ndi khalidwe la iwo omwe aitanidwawo. Ngati wina sanasankhidwe padakali pano, mwina
zingatanthauze kuti Mulungu akufuna nthawi yokwanira yoti amukonze munthuyo. Kapena zitha
kutanthauza kuti Mulungu anampatsa munthuyo mphatso yoti atumikire m’njira zina. Tidziwe kuti
simtumiki aliyense amakhala woyang’anira wa mawa. Inde tikudziwa kuti ntchito zonse ziwirizi
zimakhudzana ndi nzeru za utsogoleri ndi moyo wa chitsanzo, udindo wa woyang’anira ndi wa paokha.
Pali atumiki ena abwino omwe sangathe kutumikira bwino ngati akhala oyang’anira, ndiponso pali
abusa ena omwe sakanakhoza kukhala atumiki abwino.
Popeza zimatenga nthawi yaitali kuti pakhale mtumiki, mlaliki, mphunzitsi ngakhale mbusa, tiyenera
tidzikonzekera ndi kuchitiratu dongosolo lero lomwe lino ngati tikufuna kuti tikhale ndi atsogoleri okwanira ku
mibadwo yakutsogoloyo.
Gawo Lachinayi: Momwe Tingachitire ndi Kasinthidwe ka Zinthu.
Mawu oyamba: Nkhani ya kusintha kwa zinthu ndi nkhani imodzi yobvuta kwambiri mumpingo ndi ntchito
zake, chifukwa kusintha, kaya kwabwino ndi kololedwa komanso kofunika, ndi kobvuta malingana ndi
chizolowezi ndi chilengedwe cha munthu. Chikhalidwe chathu ndi miyambo yathu ikusintha mofulumira
kwambiri moti sizinachitikenso m’mbiri yadziko ndipo zimenezi zikubweretsa mabvuto mumpingo. Mipingo
yambiri konsekonse ikusauka ndi makangano. Anthu ena mumpingo amafuna ufulu wosintha kuti mpingo uthe
kugwirizana ndi kufikira m’maganizo a anthu amakono. Ena amaopa kutaya mpingo ndi choonadi cha
m’Baibulo chifukwa chakusintha kumeneku, ndipo amalimbalimba ndi kukana kusinthika. Alipo ambiri
okhulupirika omwe ndi okonda Mulungu ndi mawu ake ku mbali zonse zakulimbana kumeneku. Komanso
kumakhalanso ena odzikonda, akhungu ndi aukali ku mbali zonse zakukanganako. Tiyeni tiyese kuona
modekha pa cholinga cha nkhani ya kusintha zinthu mumpingo.
1. Kusintha ndi nkhani yamphamvu: ndi nkhani yoopseza ndi yosowetsa mtendere.
2. Kusintha kungathe kukhala kwabwino kapena koipa.
A. Kusintha kungathe kukhala koononga ngati kuli kusintha kochoka pa zabwino kupita pa zachabe,
kapena kusintha ndi zolinga zofuna kudzikondweretsa, kapena kungosintha pofuna kutsatira nkhosa.
Ngakhalenso kusintha kwabwino kumaononga nthawi zonse ngati mpingo ungokakamizidwa popanda
kupatsidwa nthawi yoti umvetse bwino.
B. Komanso kusintha ndi kofunika kwambiri. Ndi mbali ya moyo wathu. Popanda kusintha palibe yemwe
angathe kukula ku uzimu kapena kuthupi. Palibe munthu kapena gulu lomwe lingachize bwino kapena
kuthandiza kwambiri. Palibe yemwe akanatha ngakhale kulapa kumene kapena kufika pafupi ndi
Umodzi 31
Mulungu ndi cholinga chake. Ndipo mpingo sungathe kufikira anthu a makono osinthika ngati susintha
njira zake zofikira anthuwo.
C. Ziripo mfundo zina zoona zenizeni za mpingo zomwe siziyenera kusinthidwa; ndi zomwe zimachititsa
mpingo kuti ukhale monga momwe ulirimo. Ziripo ziphunzitso zina zofunikira kwambiri, zobweretsa
umodzi zomwe sizisowanso kukambirana kwa mtundu uliwonse – Aefeso 4:4-6; 1 Akorinto 15:1-4. Mpingo nthawi zonse uyenera kukhala woyera, wokhala ndi makhalidwe a Yesu. Nthawi zonse
udzakhala pansi pa ntchito yaikulu yopanga ndi kutuma ophunzira. Udzakhala ndi mangawa
opembedza Mulungu ndi kutumikira anthu osowa.
D. Koma Mulungu wapereka ufulu wambiri ku mpingo kuti usinthike pamene nthawi ziri kusinthanso,
potilola kuti tigwiritse ntchito njira iriyonse, zochitika, ndi mwambo uliwonse. Munthawi zimenezi
mumpingo wakhala ukusintha kuchokera ku m’badwo uwu kupita ku m’badwo wina ndipo kuchokera
ku zaka mazana mazana kufikira zaka mazana ena. Titati tibwerere kumpingo woyamba ija, tingathe
kudabwa poona kusiyana maganizo komwe kunali pakati pawo, chimodzimodzinso ndi iwowo
angadabwe Poona kusiyana maganizo kwa pakati pathu lero.
E. Choncho mu zinthu zina kusintha kungaononge cholinga cha Mulungu. Mu zinthu zinanso Mulungu
amayembekezera kuti zisinthike kuti ziyende bwino, choncho kusasintha kungaononge cholinga ndi
chifuniro cha Mulungu.
3. Miyambo ya makolo ingathe kukhala yabwino kapena yoipa.
A. Miyambo yagawika pawiri:
1) Matanthauzidwe ndi magwiritsidwe ntchito a malemba omwe mibadwo yopitayo inasiira anthu
kuchokera kwa atsogoleri olemekezeka, ndinso
2) Miyambo ndi “njira zabwino” zochitira zinthu zomwe tinasiyiridwa ndi makolonso.
B. Miyambo ndi ya umunthu, osati uzimu. Iribe ulamuliro ndi mphamvu mofanana ndi mawu a Mulungu
ayi. Koma chodabwitsa ndi choti timailemekeza pafupifupi ngati mawu a Mulungu amene, mwinanso
kuipatsa ulamuliro ndi mphamvu ndi kumaisokoneza ndi mawu a Mulungu. Kotero kuti wina akayesera
kusinthako miyambo yanuyo, zimachitika ngati wachita kusintha malamulo a Mulungu.
C. Miyambonso ndi yofunikira mu njira zambiri. Mpingo uliwonse uli nayo. Imathandiza kusunga nzeru
zakale. Imatithandiza kudziwa momwe tingapitirizire mtsogolo ntchito ya Mulungu. Imatipatsa moyo wozindikira mtundu wathu ndi chitetezo. Imapereka dongosolo labwino lakagwiridwe ka ntchito.
D. Miyambo imafika poononga pamene ifika pa ndime yooneka ngati yofunikira kwambiri ndi kumaona
ngati ndi kosayenera kuisintha ndi kuikonza pophunzitsa zomwe Baibulo linena, ndipo ndi kumaganiza
kuti sikwabwino kuisiya pamodzi ndi njira zina zomwe tazolowera ngakhale malinga ndi nthawi
sizikuthandizanso.
E. Ngati miyambo ya anthu iyamba kulepheretsa chiphunzitso cha m’Baibulo kapena utumiki wabwino
ndinso mafikiridwe a anthu ena, iyenera kusiyidwa (ngatitu tifuna kuti tikhale omvera Mulungu ndi
kuika chifuniro chake patsogolo). Tidziwe kuti tidzayankha kwa Mulungu ngati tikonda kwambiri
miyambo ya makolo athu koposa osochera omwe tiyenera kukawafikira. Yesu anamdzudzula atsogoleri
aChiyuda aja chifukwa chonyalanyaza mawu a Mulungu ndi cholinga choti alemekezebe miyambo
yomwe makolo awo anawasiyira – Mateyu 15:1-9.
4. Mfundo zothandiza pa kagwiritsidwe ntchito ka kusintha zinthu kobvomerezeka ndi Mulungu.
A. Mfundo yofunikira kwambiri yomasula nayo kumangiririka ku miyambo ya makolo ndi kuthandiza
Akhristu kuti akule m’chikondi cha pa osochera. Pamene tikukhwima m’Chikhristu, tikuphunzira kuti
kupulumutsa mizimu ndi kofunikira kwambiri koposa mtendere wathu, koposa kudzikondweretsa
tokha. Timaphunzira kuti njira yeniyeni ya Khristu ndi chikondi, kudzipereka ndi cholinga chofuna
Umodzi 32
kupulumutsa – 1 Akorinto 9:19-23; Aroma 15:1-3; Mateyu 16:24,25. Pamene mpingo ulimbikira
kufikira osochera ndi kupanga ophunzira, pameneponso mpingo udzalimbikira kufuna kusiyiratu
miyambo ndi zizolowezi zomwe zingalepheretse ntchito imeneyi ndi zolinga zimenezi.
B. Pezani nthawi yoti muphunzitse mpingo za kusiyana kwa miyambo ya anthu ndi malemba. Nthawi
zambiri timalimbana chifukwa miyambo imasokonezedwa ndi chiphunzitso cha Mulungu. Upezeni
C. mtima ndi kobvuta kuti anthu amvetse bwino zimenezi.
D. Chitani mosamala ndi modekha monga momwe mungathere. Ine ngakhale ndi kusintha komwe
Mulungu amakondwera nako, anthu ambiri ali ndi muyezo wawo wachilengedwe womwe angathe
panthawi yakuti yakuti. Mulungu amaonetsa kudekha mtima akamachita ndi anthu motere:
1) M’malo mosintha zinthu zambiri nthawi imodzi, amayamba pa zofunikira kwambiri.
2) Amabweretsa kusintha m’magawo oyenera. Mwa chitsanzo, kuphunzitsa nyimbo imodzi yokha
yatsopano pa mwambo ndi nyengo yoperekedwayo.
3) Kupitirira kuonjezera atsogoleri ku gulu la atsogoleri ena ndi cholinga, kuchokera kwa
achinyamata kuti utsogoleri wampingo ukhale woimiriridwa ndi mibadwo yonse ndi kutinso
utsogoleri usakhale monga chinthu chakale chongokhazikika.
E. Thandizani mpingo kukhala wozindikira chifukwa chomwe kusinthika kuyenera kukhalapo.
F. Musalole kuti mpingo ukhale womangiririka kumaganizo ofooka kwambiri, mokakamizika malingana
ndi pamalopo. Kumatheka kuti abale 98 apa malopo abvomereza kuti pakhale kusintha kuti anthu
ambiri akafikiridwe koma awiri aona kuti sikwabwino. Monga mwachizolowezi timangosiya chifukwa
cha awiriwa chifukwa malembo ati musakhumudwitse mbale. Tiyenera kukhala ndi mtima wodekha
ndipo mwa mapemphero kuyesetsa kubweretsa umodzi. Koma ponena zoona Paulo zingatanthauze kuti
maganizo ochepa mphamvu ndi ofookawo, akalamulire ntchito za mpingo.
Pa kuphunzitsa za kusiyana kwa maganizo, Paulo ananena molimbika kuti sibwino kwa iwo omwe
akhulupirira pa chinthu china kuti aweruze ena monganso anauzira iwo omwe alibe bvuto ndi chinthu
china kuti asalakwitse enawo. M’mbuyo monsemu sitinaganizire ndi kuzindikira mfundo imeneyi.
Paulo anatiphunzitsa kuti tidzisiya kuweruza kwina kuti kukhale m’manja mwa Mulungu ndi kupitiriza
pamodzi ntchito ya Mulungu. Pa zinthu zina zazing’ono ndi bwino kugonja pa zomwe
zikanakhumudwitsa winayo. Koma pamene tikuona kuti ntchito ya malemba ingaonongeke yomwe ikadakhoza kupulumutsa miyoyo 50, ndipo ife tingoganiza chifukwa cha miyoyo iwiri, kodi pamenepa
ndiye kuti tawakondadi anthu makumi asanu aja moyenera? Posaganizira za kudekha ndi kukonda
komwe atsogoleri ali nako, nthawi imafika pamene utsogoleri umayenera kungochita chimene
akudziwa kuti ndi chomwe ntchito ya Mulungu ifuna.
G. Sizimachitika kawirikawiri kubweretsa kusintha kwa padera mumpingo wakale, wokhulupirira
miyambo. Kuti zitero ndiye kuti mwina pafupifupi mpingowo ungagawike kapena ena ambiri
adzachoka. Ndi bwino kukonza dongosolo mpingo watsopano womwe udzalemekeza zolinga za
uthenga koposa miyambo ya makolo koma mwa mtendere.
Mawu otsiriza: Kusintha zinthu mofunikira ndi chinthu chobvuta, koma tingathe kupirira ndipo kenako
kukwanitsa kusinthako ngati atsogoleri ndi Akhristu onse ali odzazidwa ndi moyo wa Khristu.
Gawo Lachisanu: Kuchita Mwanzeru Pamene Talekana Maganizo.
Mawu oyamba: Werengani 1 Akorinto 3:1-17. Ngakhalenso mipingo yolimba iri nazo “zowawa zake
zanthawi zonse.” Nthawi zimene tikumana ndi zolimbana ingakhale monga mwayi wotithandiza kuti tikule
mwa uzimu chifukwa timakakamizika kuphunzira ndi kuzidziwa tokha. Kulekana maganizo mumpingo
kungatithandize kuona zambiri; kumva chinthu mosiyana kumathandiza kukonza, kufananiza, kapena
kuonjezerana nzeru wina ndi mnzake.
Umodzi 33
1. Kodi zina za zoyambitsa akulimbana ndi kukokana mumpingo wathu ndi ziti?
A. Zochitika “zachilendo” kapena “zatsopano” zimayamba kugwiritsidwa ntchito mumpingo ndi iwo
amene amafuna zomwe iwo amati kusintha zinthu mwa phindu. Zinthu zatsopano zimenezi zisakhale
zosiyana ndi malemba ndi cholinga choyambitsa kutsutsana. Monganso momwe zinthu zosiyana ndi
zomwe tinazolowera kuchita, zoyambitsidwa mochuluka ndi mwa msangamsanga, zingachitire.
B. Kusintha kwa utsogoleri ku guwa nthawi zonse kumayambitsa maganizo abwino ndi oyipa.
C. Takhala tikusiyira “nsakali ya utsogoleri” kwa achinyamata, pophunzira kugawana nawo utsogoleri.
1) M’badwo uliwonse uyenera kuchita zimenezi.
2) Iwo omwe ali achichepere adzaona zina za zinthu mosiyana ndi momwe m’badwo winawo
umaonera, monganso momwe ife akalefe tinali nawo maganizo athu pamene tinali achichepere.
3) Ngati akalefe sitinapitirire kuphunzira kuti tikule mwa uzimu ndi m’maganizo anzeru, ndiye kuti
kulekana pakumvetsa kwathu kudzakhala kwakukulu ndiponso kulimbana ndi kutsutsana
kudzakhala ku kukulirabe.
4) Talera ndi kuphunzitsa achinyamata athu kuchita zinthu zoposa kungolimbana ndi zoganizira
zina ndi zina. Tawaphunzitsa iwo kufuna zakuya zauzimu mwa kutsata zolemba. Nthawi zina
sizimakhala bwino pamene achita. Komabe timafuna kuti ana athu aimebe pa mapewa athu ndi
kukula kulabe mu choonadi koposa ife.
D. Mipingo ya Khristu yonse pamodzi yafika munthawi zomwe sitikuzindikira kuti kodi ndife yani? Kodi
tiri nacho choonadi chonse, kapena ziripobe zinthu zina zoti tiphunzire?
E. Pamalo pomwepo mumpingo pangathe kupezeka anthu amitundu yonse iwiri omwe atsamira pa
miyambo ya makolo ndi osasunthika, ndi enanso omwe ndi omasuka ndi okonzekera kusintha nthawi
zonse ndi cholinga chofuna kuti zinthu zikhale bwino.
[ ZOFUNIKA KUONA: Mu mphunziroli, pamene tikunena za “kusintha” tikunena za miyambo ya
makolo ndi zina zachilendo zomwe Mulungu watipatsa mpata woti tokha tichitepo chisankho. Komatu
tiribe ufulu wosintha chirichonse chomwe Mulungu wachikhazikitsa m’malemba.]
1) Anthu amaganizo onsewa nthawi zina amaononga. Anthu amaganizo osasunthika aja amati, “uwutu ndiye simpingo. Anthuwa akuusintha. Ukutayika.” Nawo omasuka posintha zinthu aja
amati, “ziripobe zambiri zoti tichite kuti mpingo ufikepo penipeni pa mpingo wa malemba.
Bwanji nanga tipitirirebe mtsogolo?”
2) Anthu amaganizo onsewa ndi okhulupirika ndipo amamkonda Mulungu.
3) Titha kumangwiriza maganizo ndi zomwe malemba atiphunzitsa komabe ndi kumasiyanabe pa
zinthu zina zazing’ono zoti tiri nawo ufulu wosankha pa kachitidwe kake.
Taonani zitsanzo za momwe mipingo imasiyanirana mu machitidwe ake:
a. Amaona maimbidwe ndi Amaona maimbidwe ndi machitidwe
machitidwe a nyimbo monga a nyimbo monga kupereka
chinthu chongopangidwa chopereka chamtengo wapatali
kapena kuonetsedwa” kwa Mulungu.
Amakondwera kuti anthu Ntethemya za kaimbidwe zimaonetsanso
Kudzipereka kwa mitima mtima wa munthu. Nyimbo monga ulaliki
Yathu, osati za ukatswiri zimamangirira. Nyimbo zoyimbidwa
womwe timauika m’mayi- mwa uthetemya ziri chimodzimodzi ndi
Umodzi 34
mbidwe athu.” Ulaliki wokonzedwa bwino.
b. Amakondwera kuti anthu Amakondwera kuti okhawo
ambiri agwire ntchito akukhosi kwabwino atsogolere
yotsogolera nyimbo nyimbo lamulungu lija.
lamulungu lija. ”Mulungu sayang’ana zakuja, “Timaika alaliki odziwa ntchito
kaya sikome chotani, guwa la Mulungu lija, chonchonso
m'mayimbidwe athu. Kutsogolera nyimbo, monga gawo
lina la kupembedza, sizinasiyane.
c. Kuomba m’manja sikuloledwa kuomba m’manja ndi kofunikira
ndipo sikuli kofunikira ndipo kumaloledwa m’nthawi
m’nthawi zopembedza. Zopembedza.
”Kuomba m’manja kusonyeza Kuomba m’manja kwa sinthika
Kugonjetsera kapena kuyambira matanthauzo lake pa chikhalidwe
kuti ena aone, koma tiri ku chathu chamakono. Ku kusonyeza
mpingo kuti tipembedze Mulungu kukondwa kapena kuthokoza
osati kuti tionetse anthu monga momwe zinalili m’Chipangano
kapena tiimbire anthu” chakale panthawi yopembedza
(nthawi imeneyo Mulungu analamulira
kuti anthu aziomba m’manja ndipo iye
sanakuone ngati chinthu chosayenera)
Ndipo ndikoyenera “kupereka ulemu
kwa iye womuyenera” ngati iye
salowerera ndi kulandira ulemu wa
Mulungu mwini.
d. Panthawi za chipembedzo Magulu ena apadera amaloledwa
tiyimbe nyimbo za m'bukhu munthawi zina zapadera.
lodziwika zokha basi. Anthu ena anadalitsidwa ndi
Nyimbo zapadera “zimakhala mphatso yokopa ndi kulimbikitsa
monga zoyimbiridwa ena. M’mayimbidwe monga momwe
Tonse tikulamulidwa kuti alaliki achitira pa guwa. Nyimbo
tiziyimba pamodzi. imakhala yoimbira wina (Aefeso 5:19; Akolose 3:16) pokhapokhapo ngati maganizo ake
ali oterowo. Mumpingo woyamba
“aliyense anali ndi nyimbo
mawu ……” (1 Akorinto 14:26).
Zikuoneka nati iyeyu ankaimbira
ku mpingo monga anali nawo”
e. Amaona kuwerenga malembo Amaona kuwerenga malembo
pa gulu lonse monga chinthu pamodzi pagulu lonse monga
chosavomerezeka, zochitidwa chimodzi mmodzi ndi kuimba
ndi mipatuko. Nyimbo pamodzi mofanana ndi
kusangalala komwe mpingo
woyamba uja unkaimbira.
f. Amaona ngati kukweza Amaona ngati kukweza manja
manja m'mwamba ndi njira m’mwamba ndi kusefukira kwa
imodzi yoyamba kuchita kuyamikira ndi kukweza Mulungu,
ngati anthu opembedza maganizo m’Chipangano Chats-
mofuula ampatuko. pano (1 Timoteo 2:8).
g. “Amakonda nyimbo zauthenga Amakonda nyimbo zoyimbidwa
Umodzi 35
zakale.” Mwaluso,” zoikiriridwa ukatswiri
pozikonza,” kapena amakonda
“nyimbo zomwe zikuyimbidwa
makono.”
”Nyimbo zosazolowereka “Tiyenera kupereka kwa Mulungu sizikondweretsa anthu ndipo zinthu zabwino zomwe tingathe;
nyimbo zina zimangowadutsa maimbidwe akhale odzala ndi
anthu osamva bwino zomwe chauzimu chopambana momwe
ziri m’menemo.” Tingathere. Nyimbo zikhale
zotha kukulumikizidwa bwino
ku maganizo a anthu amakono.
h. Amafuna mapembezedwe Amafuna ufulu wokwanira kuti
olondolezeka bwino, olongosoka athe kuonetsa chisangalalo ndi
ndi odziwika. kuyanjana.
”Chipembedzo chichitike “Kupembedza kuzichokera mumtima
molongosoka ndi moyenera. - osati zooneka zokha ayi. Kumasuka
sikutanthauza chisokonezo.”
Zonsezi ndi zizolowezi ndi miyambo yoti tikhoza kusankha kuichita kapena kuisiya. Munkhani
zonsezi mbali iri yonse imakhala nacho choonadi chake. Zimenezi ziribe umboni weniweni wa
malemba. Koma anthu amabvutika ndi kukhuzidwa ndi nkhani zimenezi koposa nkhani zomwe
ziri zofunikira kwambiri malinga ndi malemba.
4) Kodi nafenso tiri nako kusiyana maganizo pa zinthu zazing’ono ngati izi mofanana ndi momwe
mpingo woyamba uja unaliri? Ena amasungabe maphwando apadera ndi masiku monga Sabata,
koma ena ayi. Ena ankadya nyama ena ayi – Aroma 14.
2 Kodi timachita bwanji pamene tasiyana maganizo?
A. Osati:
1) Kunyoza omwe ali ndi maganizo osiyana nawo kapena kuwatsutsa ndi zolinga zoipa.
2) Kunenanena za zovuta zathu ndi wina aliyense osakhala omwe tinayenera kunena nawo, motero
timangoonjezera ndi kukulitsa kulimbana kwathu.
3) Kukana kuganizira ndi kubvomereza maganizo ena.
4) Ndale, mphamvu, kulamulira, kunyozetsa, kunenana zoipa ndi okutsutsani, kupatsana maina
achabe (wachilamulo, waufulu, wauzimu, wampatuko)
B. Koma mwa:
1) Kumvetsa mfundo zina:
a. Nthawi zonse padzakhala kusiyana maganizo pa mpingo uliwonse
womwe
ukukula. Padzakhala kulolerana ndi kugwirizana munkhani zina
zazing’ono, apo ayi, mpingo udzagawika ndi kukhala m’magulu. Paulo
amatiphunzitsa kuti tidzikhala ololerana munkhani zina zazing’ono –
Aroma 14,15.
Umodzi 36
b. Pamene tikukula kusintha kwina kumakhala kofunika. Tiribe ufulu
wosintha zomwe zinamangirika ndi malemba, koma pa nkhani
zakumasuka tiyenera kusintha kuti tithe kufikira bwino ku khalide
losinthikali (ngati tikufuna kutsatira chitsanzo cha Paulo ndi kufikira
mizimu yochuruka – (1 Akorinto 9:19-23). Kusinthika pakokha sikuli
koipa kapena kwabwino.
c. Kusintha nthawi zonse kumatisautsa. “zakale zomwe zija zinali bwino.”
d. Nthawi zina anthu amaukirana wina ndi mnzake chifukwa chosamvetsa
zomwe mpingo ndi mapembedzedwe ake uliri malingana ndi malemba.
e. Kulimbana kwathu m’mipingo nthawi zambri kuli pa momwe timvera
malembo osati pa chiphunzitso chenicheni cha malemba.
f. Kulimbana kotigawa kumayambika ndi “mbali zonse” zokakamiza kuti
zisinthe ndi kulimbana pokana kusintha. Cholakwika chimodzi chachikulu
chomwe tingachite ndi chodzudzula mbali imodzi yokha ya vutoli.
Mu Aroma 14 ndi 15 timaphunzira kuti anthu okhala ku mbali zonse
zankhaniyi ayenera kufewetsa zofuna zawo ndi maganizo awo kuti athe
kusamalirana ndi kukhala amodzi. Uwu ndiwo moyo wa mtanda – Aroma
15:1-3. Mpingotu sungathe kukula ndi kuyendera pamodzi popanda
chimenechi.
2) Pomvetsa ndi kubvomereza kuti tiri ndi umunthu wochimwa ndi wodzitamandira.
a. Nditha kumafuna kudzikondweretsa ndekha koposa kukondweretsa
zofunikira za mpingo.
b. Nditha kukhala wopanda chidwi chosenza zofooka ndi zosowa za ena.
c. Nthawi zina nkhawa zanga za kunyumba kwanga kapena zina zodziwa ine
ndekha kapena kuntchito kwanga ndimazipitiriza ndi kuzilowetsanso
kumpingo.
d. Zolimbana zambiri mumpingo ndi m’mabanja nkhani za “mphamvu” osati
zimene zimaonekerazo.
3) Pochita zinthu zosagwirizana ndi umunthu m’malo mochita za umunthu pamene titsutsana ndi
ena.
a. Umunthu wathu umatikakamiza kusakomanso ndi anthu omwe
sitigwirizana nawo. Choncho anthu olekanawo amangopitirirabe
kulekana.
b. Onetsani kupepesa kwanu chifukwa cha umunthu wanu wa uchimo
pochita zomwe anthu sangaziyembekezere:
1. Khalani ndi nthawi yoyanjana ndi omwe simugwirizana mu zambiri.
2. Yesetsani kuyamikira ndi kumvetsa maganizo a enawo mosakondera ngakhale
simugwirizana nawo.
3. Onetsani zolinga zabwino kwa okutsutsaniwo – 1 Akorinto 13:4-7.
4) Yambani mwaganiza bwino kwambiri musanayankhule kapena kuchita.
Umodzi 37
a. Tidzayankha mlandu pa mawu onse opanda pake omwe tidzayankhula – Mateyu 12:36-37.
b. Mulungu amadana ndi anthu omwe amafetsa mbewu zodanitsa abale – Miyambo 6:19.
c. Yesu amapempherera kuti tikhale amodzi kuti dziko likhulupirire kuti Mulungu ndi amene
anamtuma – Yohane 17:20-21.
d. Kukanakhala bwino kuti munthu amizidwe m’nyanja yakuya koposa kuchimwitsa mmodzi
wa aang’ono – Luka 17:1,2.
e. Ngati tiononga kachisi wa Ambuye pogawanikana, nayenso adzationonga – 1 Akorinto
3:16,17.
f. Tiyenera kumadziunika tokha koposa enawo – Mateyu 7:1-5. Mwina chifukwa cha
kusadziwa, nditha kutsutsa zomwe Mulungu afuna. Nditha kumalimbikitsa zomwe Mulungu
safuna. Polimbikira kusunga miyambo ndi zizolowezi nditha kumangofuna maonekedwe
osati zenizeni zofunikira. Pofunafuna kusintha kwa zinthu nditha kumangofuna kuti ndione
momwe zikhalira m’malo moti zikhale molingana ndikufuna kwa Mulungu kapena kumvera
kwathu kwa tsiku ndi tsiku. Ngati ndikana kusintha chifukwa cha chiphunzitso chomveka
bwino cha malemba, Iye adzandipatsa mphoto. Ngati ndikana kusintha chifukwa chakufuna
kungokondweretsa maganizo anga ndi zofuna zanga, Mulungu adzandilanga chifukwa
ndalepheretsa ntchito yabwino yobereka zipatso ya mpingo. Nditha kuchita zinthu
kumpingo zomwe sindinachitepo.
4) Pouza zotisautsa zathu kwa wotilakwirayo, ndipo kenako ngati nkofunikira kwa
atsogoleri a mpingo – Mateyu 18:15f.
a. Popereka kwa enawo chilolezo chomwe ifenso tikadakonda atatipatsa.
a. Popita ku tchalitchi ngakhale kuti pali poti dongosolo lomwe
likukonzedwalo sitikondwera nalo patokha.
b Poganizira kuti nditha kuupeza mtima ndi kudzibweza ngakhale wina
atachita china chomwe ine sindichibvomereza monga cholondola.
c Pokhala ndi mtima wodekha mwachikondi kwa omwe sagwirizana ndi
maganizo anga osintha zinthu.
6) Atsogoleri athu pomvetsera mosamala ku maganizo ndi zofunikira zonse mumpingo ndi
kusankha njira yodekha yomwe idzakhoza kukwaniritsa zosowa za mbali zonse monga momwe
kungathekere. Mpingo suyenera kukhala ndi maganizo a anthu a mbali imodzi yokha.
Abusa oyenera azikhala owonetsetsa ndi odziwa zonse zochitika pa mpingo, akonze ndi
kugwiritsa ntchito mfundo yodekha yosinthira miyambo ndi zizolowezi, kulemekeza zonse
zokhazikitsidwa mwa malemba, kuphunzitsa mpingo kuti uonjezere chidziwitso chake, ndi kuika
chitsanzo chabwino cha kulolerana pakati pa atsogoleri okha. Ayenera kumadziwitsiratu mpingo
kusintha kuli konse kusanachitike.
Mawu otsiriza: Palibe chinthu china chomwe mdierekeze angachikonde chopusa kucheptsa ndi kunyoza
ntchito yabwino yomwe ikuchitika m’mipingo. Iye amafuna kuti ife tidziika maganizo athu kwambiri pa zinthu
zazing’ono, ndi kutichotsera moyo wodalira Yesu ngati Ambuye wathu, ndinso kutichotsera moyo wofuna
kukafikira ndi kukachiritsa mizimu. Tiyenera kupereka ulemu wathu wonse kwa Khristu pochita ndi kulekana
maganizo kwathu munjira yoti siting’amba thupi lake, mpingo. Tiyenera kulemekeza atsogoleri athu ampingo
pamene akuyesetsa kutitsogolera mu umodzi. Ndipo tiyenera kupempherera atsogoleri athu pamodzi ndi
mpingo wa Khristu.
Umodzi 38
Mutu 6: Umodzi ndi Malekano Mumpingo wa Khristu -
Yesu anapempherera omtsatira ake kuti akhale amodzi kuti dziko lapansi likamkhulupirire Iye – Yohane 17:20-
21. Ntchito yopititsa mtsogolo ufumu wa Mulungu yokhala ikusokonezedwa kwambiri ndi kugawanika pakati
pa Akhristu koposa zifukwa zinazo. Ndipo ufumu wa Satana wapindula kwambiri potengera mwayi
kugawanika kumeneku. Ngati tiri ndi mtima wonga wa Khristu, tidzalakalaka umodzi wapakati pathu ndi anthu ena okhulupirira ndipo tidzachita china chirichonse, poyesa yesa kuti pakhale umodzi. M’masiku ano, pamene
mipatuko ikuchepera ndipo pali njala yomwe ikukulira yofuna kubwerera ku zoona zokhazokha, nkhani
yotsatira itithandize kuganizira mozama.
1. Kodi onse okhulupirira Yesu angathe bwanji kukhala amodzi? M'zaka za m’ma 1800 ku Britain ndi ku
America, kunapezeka aphunzitsi ambiri ochokera m’ziphunzitso zosiyanasiyana za mpingo omwe
anasautsidwa m’mitima yawo chifukwa cha malekano ndi kulimbana pakati pa okhulupirira, omwe anafuna
kuyanjanitsa okhulupirira onse pobwerera ku ulamuliro umodzi wa malembo achikhulupiriro ndi zochitika
za mpingo. Padali Abner Jones ndi John Wright a gulu la a Baptist; James O’kelley a gulu la a Methodist;
ndi Barton W. Stone, Walter Scott, Thomas Campbell ndi mwana wake Alexander Campbell a gulu la a
Presbitale. Aliyense wa amenewa payekha payekha anakhumudwa ndi kulimbana ndi kupatukana komwe
kunalipo pakati pa otsatira Khristu chifukwa cha ziphunzitso. Ndipo aliyense anaona kuti njira yabwino
yoyanjanitsira okhulupirirawa inali yekhayo yobwerera ku ulamuliro wa malembo. Thomas Campbell
anayesetsa kugwira ntchito yoyanjanitsa Akhristu a m'gulu la a Presibiteriani omwe anali kulimbana ku
mpingo wa ku Ayalandi (Irelandi).
2. Thomas Campbell, Alexander Campbell ndi Barton W. Stone anali atsogoleri opambana omwe anadziwika
nthawi imeneyo pa ntchito yoyesetsa kubwezeretsa chikhulupiriro cha pa malemba ndi kuchita komwe. A
Thomas Campbell anapita ku America kuchokera ku Scotland. Iye anali pasitala wa mpingo wa a
Presibitare, ndipo kudziko la chilendo iye analandiridwa napatsidwa ulamuliro ku mipingo ina yakomweko
komwe iye ankayendera. Campbell anabvutikanso m’maganizo pamene anapeza kuti ku America nakonso
kunali magawano ndi magulu omwe anawasiya kwawo ku Scotlandi kuja. Omwe anali a gulu limodzi
samalola kuyanjana pamodzi ndi a gulu lina lija ngakhale kuti onse anali a Pulesibitare okhaokha. Ndipo
m'matauni monse munali magulu odzipatsa maina osiyanasiyana namataya nthawi yawo ndi mphamvu
zawo kulimbana wina ndi mnzake, mphamvu zoti anayenera kudzigwirira ntchito yopulumutsira osochera
ngati mipingo ikanakhala yogwirizana.
3. Pamene Campbell anafuna kuyanjana ndi gulu lina lija mwa mgonero, iye anatsutsidwa ndi akulu a
mpingo. Kenako iye anangoganiza zosiya kugwiritsa ntchito dzina loti “Pulesibitare” nayamba
kumangotumikira Mulungu wake monga Mkhristu basi popanda kuonjezeranso dzina lina la padera la chipembedzo. Anayamba kuzindikira kuti maina opangidwa ndi anthu ndi zikhulupiriro zake zomwe,
zimangolimbikitsa zipupa zamalekano pakati pa magulu otsatira Khristu. Iye anatsimikizika kuti ntchito
yake yonse ikangotsamira pa mphamvu za malemba basi, ndipo anayamba kudandaulira ena onse omwe
anali m’mipingo kuti asiye kulimbana pakati pawo chifukwa cha miyambo ndi zikhulupiriro zoikidwa ndi
anthu ndikuti agwirizane pomangoyang’ana pa malembo kuti adziwe komwe akupita ndi choyenera
kuchita. Iye analibe cholinga chofuna kuyambitsa mpingo watsopano. Iye anangofuna kuti mipingo
isinthike posiya miyambo ndi zizolowezi zomwe inadzipangira ndi kudziunjikira ndipo m’malo mwake
agwirizane ndi kuyanjana pansi pa chiphunzitso ndi machitidwe a atumwi.
4. Pamene Thomas anapita ku America, Alexander, mwana wake, anatsala ku Scotland kwa kanthawi
pamodzi ndi mayi wake ndi ana ena onse. Panthawi imeneyi Alexander anali kuphunzira pa univesite ina.
Nayenso, monga bambo wake, anatulukira kuti panali kulekana kwa maganizo mumpingo pa zifukwa
zazing’ono, ndipo kuti anthu a gulu linalo sanali kulola kuyanjana pa mgonero ndi anthu a gulu linali
ngakhale onse anali a Pulesibitare okhaokha. Iye anaonanso kuti makonzedwe ndi dongosolo la zochitika
za mumpingo wa a Pulesibitalewu zinali zosiyana kwambiri ndi zomwe iye anaona m’malemba. Pasanapite
nthawi Alexander pamodzi ndi ena onse a pa banja lawo anapita kukhala pamodzi ndi Thomasi ku Amerika
kuja. Ali ku Amerikako Alexander anayamba kuthandiza bambo ake mu ntchito yodandaulira kuti pakhale
umodzi wosadalira zoikika ndi maganizo a anthu koma zotsamira pa malembo.
5. Thomas Campbell analemba bukhu labwino lofotokoza za umodzi pakati pa Akhristu ndi zoyambitsa
Umodzi 39
kupatukana. Linatchulidwa “Kunena poyera ndinso kuyankhulira” (Declaration and Address), (onani gawo
lake ku zoonjezera). Thomas ndi Alexander anaona kuti Baibulo linali chimodzimodzi ku mipingo yonse,
koma ziphunzitso ndi zikhulupiriro ndizo zinasiyana. Mipatuko siichokera mu Baibulo limodzi ayi, koma
ichokera ku zikhulupiriro ndi ziphunzitso zolekanazo zomwe ndi zopangidwa ndi munthu. Mpingo
uliwonse unali wokonzekera kumvera unzakewo ngati unzakewo ukanasiya zikhulupiriro zake ndi
ziphunzitso zake ndi kubvomereza za winawo. Koma zonse sizinayenda bwino popeza mpingo uliwonse pawokha unakakamira kugwiritsa zikhulupiriro zake monga zoulamulira.
6. Thomas Campbell anayamba kupempha okhulupirira onse kuti ayambe kusiya zikhulupiriro ndi
ziphunzitso zonse zolembedwa ndi munthu ndi kubwerera ku malemba, omwe ali olandiridwa ndi onse,
monga maziko enieni owalamulira ndinso umodzi. Iyenso anapereka maganizo oti anthu asamachite
chirichonse mumpingo chifukwa choti atsogoleri awo akale ankachita motero, koma kuti tiwerengenso ndi
kuphunzira bwino malemba ndi kuchita chirichonse chomwe tichita chifukwa cha mphamvu ndi ulamuliro
wa malembo.
7. Ndipo pamene anapitirira kuphunzira mawu a Mulungu, Thomas ndi Alexander Campbell, mabanja awo,
ndi ena omwe ankaphunzira nawo pamodzi anabatizidwa mwa ubatizo weniweni womizidwa. Iwo
anazindikira kuti ubatizo wawo wa poyamba wa pamutu sunalingane ndi ubatizo wa mawu a Mulungu,
ndipo kuti ubatizo wa pa mutu unali wonga njira za chidule zopangidwa ndi munthu monga chizolowezi
chabe chomwe chinayamba kuchokera munthawi za atumwi. Anasiyanso kumayang’ana malo ena a dziko
kapena bungwe monga boma kapena likulu la mpingo, chifukwa anaona kuti m’mawu a Mulungu mpingo
uliwonse unali nawo atsogoleri ake osakhalanso pansi pawina aliyense koma pa ulamuliro wa Khristu basi.
Anasiya kudalitsa makanda ndi ana aang’ono chifukwa sanapeze ulamuliro kapena chitsanzo cha
mchitidwe umenewu m’mawu a Mulungu. Anayamba kumayanjana ponyema mgonero wa Ambuye sabata
iriyonse pokumbukira imfa ya Khristu tsiku loyamba la Sabata iriyonse chifukwa anaona ndi kuphunzira
kuti mpingo woyamba unkatero. Anapitiriza kuphunzirabe ndi kutsatirabe zambiri ziphunzitso ndi
machitidwe a mpingo wa Chipangano Chatsopano, ndi kutaya zikhulupiriro ndi ziphunzitso zomwe
anakhulupirira kuti zinangoonjezedwa ndi anthu m mibadwo yobwera nthawi ya atumwi itapita. Patapita
nthawi, Campbell ndi mwana wake anagwirizana ndi Walter Scott ndi Barton W. Stone omwenso nawo
anali kulakalaka ndi ntchito yobweretsa umodzi potsamira pa mawu a Mulungu.
8. Chiwerengero cha anthu omwe anakhulupirira mfundo zimenezi chinachulukira chulukira ndipo mipingo
inabadwa. Zinthu zonga zomwezi zinali kuchitikanso ku Britain. Ntchito yonseyi pamodzi inatchedwa
“Ntchito yobwezeretsa” (Restoration Movement). Komatu atsogoleri antchito imeneyi analibe maganizo
ndi zolinga zofuna kuyambitsa mpingo winanso ayi. Iwo anangofuna kuti magulu onse olekana aja akhale
amodzi monga thupi la Khristu motsamira pa malembo. Komabe ngakhale anthu ambiri anabvomereza
pempho limeneli, anthu ambiri m’mipingo yambiri anakana, ndipo “Osinthitsa zinthu aja” kapena “obwezeretsa zinthu aja” pamodzi ndi owatsatira awo anangopitiriza monga gulu chabe. Choncho konse ku
America ndi ku Britain anthu a m'gulu limeneli ankatchedwa “Akhristu”, ndipo mpingo wa pamalo
unkatchedwa “mpingo wa Khristu,” “mpingo wa Chikhristu,” kapena “Ophunzira a Khristu.” Koma ndi
maina amenewa sanatanthauze kuti iwo okha ndi amene anali anthu ake a Khristu. Sanali kuyeserera
kutenga malo a Mulungu ndi kuweruza zotsatira zake za okhulupirira enawo. Koma anangokhulupirira kuti
ngati mpingo uli wake wa Khristu, uyenera kumlemekeza pobvalanso dzina lake, monganso momwe
mkwatibwi amabvalira dzina la womkwatira wake. Sanafune dzina lomwe silinachokere m’mawu a
Mulungu, ndipo anakhulupirira kuti maina oikidwa ndi anthu osiyanasiyana amangolimbikitsa kusiyana
komwe kulipo pakati pathu.
9. Bungwe limeneli lobwezeretsa silinakwaniritse zomwe limayembekeza ndi zolinga zake monga momwe
zikanakhalira. Panabukanso kugalukirana kwakukulu mzaka za m ma 1900. Pankhani ya nyimbo
zoimbidwa pogwiritsira ntchito zida munthawi yachipembedzo ndi kukhazikitsa bungwe la a mishonare.
Kugawikanaku kunapitirirabe pamene mpingo tsopano unasowa ndi kutaya masomphenya a zolinga zake
zoyamba zija. Ena omwe anali kugulu lopanda ukali mubungwe limeneli anayamba kusalemekeza ndi
kukhulupirira mphamvu ndi ulamuliro wa malemba. Nawo oumirira za miyambo aja anasokonekeranso
kumbali inayo, nayamba timagulu tina tambirimbiri, namadzitcha kuti iwo okhawo ndiwo ali mpingo
weniweni wopulumutsidwa. Zolinga zenizeni zomwe zinatsogolera ntchito imeneyi zinali za kufunika kwa
mphamvu ndi ulamuliro wa malemba ndi kuipa kogawanikana chifukwa chosiyana maganizo ndi
kumvetsana pa nzeru zina ndi zikhulupiriro zina. Mipingo ya Khristu inapitiriza ganizo loyambalo koma
Umodzi 40
unalephera kumvetsetsa ndi kukumbukira cholinga cha ganizo lachiwiriro. Tinalepherakusiyanitsazinthu
zenizeni zotumikira ndi maganizo chabe. Tinali monga gulu limodzi la palokha, logawika
m'timagulu tambiri mwa magulu a chipembedzo ku America, logawikana m’magulu opitirira 25. Gulu lathu
lotchedwa ‘mipatuko’ ndipo kenako tinawapitirira mu njira yolekanitsa, moyo wa mpatuko.
Monga momwe kusintha ndi kubwezeretsa kumafunikira nthawi zina, komanso kuli nako kuopsa kwake komwe kuli kwa mitundu iwiri: Pa momwe amatengera machitidwe a m’Chipangano Chatsopano, angathe
kunyalanyaza chiphunzitso cha m’Baibulo pazakusinthika mtima kwa mumtima (komwenso umodzi
umatsamira). Ndipo angayambe kukhala ndi moyo woyang’ana ndi kudalira malamulo, kukhulupiriro kuti
Mulungu amatilandira chifukwa cha kusunga malamulo kuposa chifukwa cha chisomo cha ulere cha
pamtanda wa Khristu. Ntchito yosintha ndi kubwezeretsa imeneyi nthawi zambiri yakhala ikugwera m
misampha yonse iwiri. Ngakhale panthawi yomwe ntchitoyi inali pa kaindeinde, sikunatheke kubwezeretsa
chiphunzitso cha m’Chipangano Chatsopano, machitidwe ndi moyo wabwino sizinatheke kufika pomwe
zinali kufunikirapo. Iyi ndi ntchito yoti imangopitirira.
Wolemba ameneyu akukhulupirirabe kuti “mfundo yobwezeretsa” ndi yofunikirabe yoyenera kupitirira,
makamaka kusiya miyambo ndi zizolowezi zopangidwa ndi anthu ndi kupitiriza kuyanjanitsa okhulupirira
onse mwa kutsamira pa mphamvu ndi ulamuliro wa mawu a Mulungu basi. Palibe yemwe angatsutse
mfundo imeneyi. Ngakhale mfundoyi yakhala ikulephera m’magawo ena, ntchito yobwezeretsayi yalalika
ndi kufalitsa uthenga wamtengo wapatali ndi wofunikira kwambiri wonena za kutsamira ndi kudalira pa
mphamvu ndi ulamuliro wa malembo, ndiponso waturutsa atumiki a Mulungu ambiri omwe agwira ntchito
yotamandika kwambiri. Ndipo sionse a atsogoleri a gulu limeneli omwe anakhala ndi mtima wampatuko.
Abambo anga a ine anakana kulowa m’gulu la mpatukolo ndipo zotsatira zake ndi zoti anazunzidwa
kwambiri. M’masiku atsopanowa, magulu ena omwe anachoka mogalukira analapa ndipo analandiridwa
m’chiyanjano chathu.
10. Mpingo uyenera kumayendetsedwa mwa ulamuliro ndi mphamvu za malemba okha m’chikhulupiriro ndi
m’machitidwe wokha basi, chifukwa:
A. Miyambo ndi ziphunzitso zongoonjezeredwa ndi anthu zimagawanitsa Akhristu – Aroma 16:17.
B. Akhristu ayenera kumvera mawu a Khristu Ambuye wawo ndipo ayenera kumachita chifuniro chawo
monga momwe chinaululidwa m’Baibulo. Iwo alibe mphamvu ndi ulamuliro wosintha chimene
chinalamulidwa ndi Ambuye kapena atumwi awo. Onse okonda Khristu ayenera kumalakalaka
kumukondweretsa pomvera ndikudzipereka ku mawu ake – Yohane 14:21,23; Luka 6:46.
C. Mulungu sakondwera ndi mapemp0hero athu pamene tilowetsa miyambo ndi zizolowezi zopangidwa ndi anthu m’malo mwa malamulo a Mulungu – Mateyu 15:3-9.
D. Sitingathe kupeza nzeru za mtundu woposa nzeru za Mzimu Woyera zomwe zifotokozedwa
m’malamulo a atumwi ndi zitsanzo za mumpingo woyamba.
11. Atsogoleri oyamba a gulu la kubwezeretsa aja, anali okhudzidwa kwambiri ndi nkhani ya umodzi pakati pa
Akhristu. Iyi ndi nkhani ya Baibulo. Mu Aefeso 4:4-6 Paulo akutiuza wapereka mndandanda wa
ziphunzitso zisanu ndi ziwiri (7) za zoonadi zake zomwe mipingo yonse pamodzi ndi Akhristu onse
ayenera kugwiritsa ndi kukhala nazo mofanana ngati afuna kukhala ndi “umodzi wa Mzimu Woyera” mwa
Khristu. Iye akutchula thupi limodzi, Mzimu mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, Ambuye mmodzi, ubatizo
umodzi, ndi Mulungu mmodzi. Awa ndiwo maziko enieni a chiphunzitso cha umodzi.
Komabe kungomvana ndi kugwirizana pa chiphunzitso chokha sikungayanjanitse Akhristu. Koyambirira
kwa ndime yomweyo ya umodzi, pa Aefeso 4:1-3, Paulo akutiuza za mtima womwe Akhristu ayenera
kukhala nawo kuti asunge ndi kusamalira umodzi pakati pawo. Iye akutchula, kudzichepetsa konse,
chifatso, chipiriro ndi kulolerana mwachikondi. Malingana ndi Pauloyo, umodzi ndi chinthu cha Mzimu,
ndipo zoyeneretsa zomwe zasanjidwa pamenepazi ndizo chipatso cha Mzimu Woyera – Agalatiya 5:22,23.
Kulikonse komwe Paulo anapita, iye amaphunzitsa kuti Akhristu sayenera kuweruzana wina ndi mnzake
kapena kulekana chifukwa cha mfundo zazing’ono, zomwe angathe kukambirana ndi kusankha maganizo
omwe afuna ponena za m’Baibulo ndi ziphunzitso zake, koma ayenera kungosiyira nkhani zimenezi
Umodzi 41
Mulungu pamene iwo apitiriza kugwira ntchito pamodzi. – Aroma 14:1-15:7. Kugawanikana pa zinthu
zimenezi pakokha ndiko kusamvera malemboko. Baibulo litiphunzita kuti ife timayanjanitsidwa ndi
kukhala amodzi chifukwa choonadi chenicheni cha chilungamo osati chifukwa choti tagwirizana ndi
kufanana maganizo pa mfundo zina zazing’ono. Ndipo kupatukana kwambiri sikumabwera chifukwa
chosamvana pa ziphunzitso koma chifukwa mtima wofuna kudziganizira wekha, ndinso makani chabe –
Agalatiya 5:19-21; Aroma 16:17,18. Nthawi zambiri nkhani za chiphunzitso ndi chikhulupiriro zimaperekako mwayi wa ulemu; zoterezi zikanatha kukonzedwa ngati pakanakhala mtima wabwino ndi
kulakalaka kwenikweni kwa umodzi. Titha kukhalabe okhulupirira ndi kudalira malemba pa chiphunzitso
ndi chikhulupiriro chathu ndi machitidwe athu, koma ndi kulekanabe maganizo ndi kumagawikanabe,
kumapitirirabe kupikisana kufikira mitima yathu itasinthika ndipo umulungu utabadwa mwa ife mwa
Mzimu Woyera ndi mawu. Nthawi zambiri kupatulana chifukwa cha zipembedzo, sichifukwa ayi, koma
kungofuna kulimbana kudzifunira kutchuka, kudziyeretsa pobvala mwinjiro wa chipembedzo. Ngakhale
ntchito yobwezeretsa inachita gawo lalikulu pobwerera ku kudalira ku maziko a chiphunzitso ndi
machitidwe a malemba, sunathe kupitiriza mpaka pa ndime yokonzanso za bvuto la kufunika kwa kusintha
kwenikweni kwa uzimu ndi kusinthika kwenikweni kwa mkati mwa mtima.
Choncho pofuna kukhala ndi umodzi wachipembedzo, chiphunzitso chathu chiyenera kupitirirabe kusinthika
pogwiritsa ntchito malemba, ndipo mitima yathu nayonso isinthike pogwiritsa ntchito Mzimu Woyera. Zonsezi
kuti zitheke pamafunika kudzichepetsa. Munthu wodzitukumula ndi wonyada sangathe kusiya ndi kuiwala
zikhulupiriro ndi zizolowezi zake za umunthu pamodzi ndi moyo wake wozolowera zolimbana ndi zotsutsana.
Ndipo kudzichepetsa kumeneku kumatheka pokhapokha pamene tibadwanso mkatikati mwa mtima wathu mwa
Mzimu Woyera ndi kupatsidwa umoyo watsopano wa Yesu Khristu. Tiyeni tidzipereke kumoyo womvera ndi
kukhulupirira malemba ndi Mzimu Woyera. Pakutero tidzakwaniritsa pemphero la Ambuye Yesu: “[Ine ndi
pemhera] kuti onsewa akakhale amodzi … kuti dziko lapansi likakhulupirire kuti inu munandituma ine” –
Yohane 17:20,21.
Mutu 7: Mpingo wa Khristu ndi Zipembedzo Zina za Chikhristu.
Ngati umodzi uli wofunikira kwambiri mu ntchito yofalitsa uthenga wabwino, ndi koyenerera kuti tionenso
bwino pa za momwe timaganizira magulu omwe analowa nawo mu gulu losintha sintha zija. Nkhani zina za
ziphunzitso zomwe zimatigawanitsa pakati pathu zimakhala zokulirapo. Komanso mwa chiyero, timayenera
kuyamikira ndi kuthokoza pa zinthu zomwe anthu achita bwino, poonjezera pakudzudzula ngati alakwitsa.
Ndiri wokondwa chifukwa ambiri pakati pa abale alibenso mtima wofuna kutenga udindo wa Mulungu
woweruza ena omwe ali mu “zipembedzo zina.” Tingathe kukhala okhulupirika m’malembo popanda kutero.
Ndimasanalatsidwa ndi mawu amphamvu omwe ena a abale m’mipingo ina amanena, “osati Akhristu okhawo,
koma Akhristu okha.” Yesu analangiza ophunzira ake kuti asaletse iwo omwe anali kutumikira m’dzina lake
ngakhale sanali nawo m’gulu limodzi. Paulo anali wokondwera chifukwa Yesu analalikidwa ngakhale ena a
olalikawo sanali ndi zolinga zowona.
1. Mipingo ya Khristu mzaka zatsopanozi, zaposachedwapa inayamba kudziwika mona yokhulupirira kuti ndi
yekhayo yodziwika kuti ndi yopulumutsidwa. Ndiri wokondwa chifukwa tsopano pali kusintha, chifukwa
izi si zomwe abale athu omwe amayamba ntchitoyi anakhulupirira. Abale omwe anayambitsa kuti Mulungu
anali nawo anthu ake omwe anali m'zipembedzo zosiyanasiyana. Anapempha Akhristu onse kuti asiye
ziphunzitso ndi zikhulupiriro ndi kugwirizana mwa kumangiririka pa malemba basi. Bambo wanga
anandiphunzitsa kuti munthu aliyense yemwe wabadwanso kawiri, nalandiridwa ndi Mulungu, ali gawo la
thupi la Khristu ngakhale mipingo yathu isamdziwe kaya imdziwe. Tikanakomana nako kuzunzidwa
mwadzidzidzi, maganizo athu onse akadasinthika tsiku limodzi pa umodzi wathu. Tikanayamikira
kwambiri aliyense yemwe alemekeza Yesu monga Ambuye ndi kuyeserera kumumvera.
2. Gulu lathu lachita ndi ziphunzitso zina zofunikira zomwe enawo amazifuna. Mwa chitsanzo, Alexander
Campbell anali mmodzi wa anthu omwe anayambirira kuona ndi kulalikira za kusiyana kwa pakati pa
mapangano akale ndi atsopano, ganizo iri tsopano likuvomerezedwa ndi kulandiridwa ndi zipembedzo zina
zomwe zimakana kusintha mwa chisawawa. Ndimakhulupirira kuti tiri nazo nzeru zofunikira pa za ubatizo
ndi utsogoleri mu mpingo.
3. Anthu adzatimvera ngati tiwalemekeza ndi kuwakonda. Kwa zaka zambiri, ndakhala ndi kuganizira kuti
ngati tifuna kuti anthu amvetse bwino zikhulupiriro zathu, kunali bwino tikanakhala nayo njira yabwino
yochitira zimenezi. Kudzichepetsa ndi chikondi kungatithandize kukalowa m’mitima yomwe kuuma moyo
Umodzi 42
ndi chipongwe, ndi kupikisana sikungalowe (2 Timoteo 2:24-26). Mmodzi wa ophunzira anga, mkulu
wampingo, anandiuza kuti sanakhulupirira kuti mipatuko ingadzathetsedwe kufikira pamene anakhala ndi
kuphunzira mu maphunziro a SHBI ndi kuona anthu ochokera ku mipingo yosiyanasiyana mwa chidwi
akubvomereza chiphunzitso cha Baibulo. Mkulu wina anadabwanso Poona momwe anthu amenewa
anachita pokhalabe m’maphunziro ake omweo amfundo za kubwezeretsa omwe takhala tikuphunzitsa
nthawi zonse.
Tsiku lina madzulo ndinali kuphunzitsa pofotokozera chiphunzitso cha Calvinistic chomwe chimati
chirichonse chimatsogoleredwa ndi Mulungu ndipo palibe mwayi wopanga chisankho chifukwa Mulungu
ndiye amaoneratu zonse. Wina anathirira ndemanga yoti “zimenezi ndiye zitinso?” Ife timakhulupirira kuti
Mulungu amatipatsa mwayi wosankha chifuniro chathu.” Tsiku lina usiku ndinafotolozera za nkhani ya
Namani wakhate yemwe chikhulupiriro chake chinayesedwa polamulidwa kuti akasambe mu mtsinje wa
Yordano. Ndinafotokoza kuti nthawi zambiri Mulungu amafuna muyezo wina wake wa chikhulupiriro
monga njira yoonera chikhulupiriro chathu. Mkulu wina wopuma pa ntchito monga mphunzitsi wamkulu
yemwe anali ndi zaka 80, wampingo wa Baptist, wa nzeru zake ndithu, anafunsa kuti, kodi nawonso
ubatizo ungakhalenso njira yoyesera chikhulupiriro? Nthawi zonse ndimafotokoza kuti ubatizo ndi gawo
ndi nthawi yomwe chikhulupiriro chathu chimakumana ndi chisomo cha Mulungu ndi kubweretsa
chikhulupiriro. Ndi kukhulupirira kuti kupambana kwathu kungathe kufanizidwa bwino ndi kwa wina
aliyense pamene tifika pa ndime yolandira ulemu pa maganizo a chiphunzitso ndi chikhulupiriro chathu.
4. Ine ndimakhulupirira kwambiri monga ndakhala ndi kuchitira nthawi zonse pa za ubatizo, ngakhale
ndimaganizanso kuti pena pakenso sitinaganizire bwino ndipo tinasokoneza chiphunzitsochi chifukwa
chochita nacho mopitirira. Ngati mwana analandira ubatizo wa pamutu ali mwana, ndingamulimbikitse kuti
akwaniritse ndithu chiphunzitso cha Ambuye cha ubatizo ndipo achite zimenezi ndi chikhulupiriro
chakechake. Ngakhale kuti asanatulukire ndi kuona kufunika kwa zimenezi, sikuti ndikanakhala naye ndi
ubale wofanana ndi womwe ndingakhale ndi wina yemwe amakaniratu Yesu kukhala Ambuye wake.
5. Nimakhulupirira kuti kulakwitsa kumodzi kuopsa komwe kunachitika mu mbiri ya nthawi zosinthayi, pa
mbali yogawanitsa thupi la Khristu, kunali kukhulupirira kuti, “kuti ubatizo ukhale waphindu,
wobatizidwayo ayenera kumvetsa kuti ubatizowo umachotsa machimo. Maganizo amenewa amafalitsidwa
ndi mzaka za 1900 ndi Austin Mc Garry, yemwe anali mlembi woyamba wa bukhu lotchedwa “maziko
olimba” (Firm foundation). Chifukwa chenicheni cholembera bukhu limenelo chinali choti anthu aunikire
ndi kuona ngati kubatizidwa kawiri ndi kwabwino malingana ndi maganizo a David Lipscomb, mlembi wa
bukhu lotchedwa “kuyankhula mogwirizana ndi uthenga” (Gospel advocate) ku Tennessee ku America.
A. A Baptist ambiri akhala akuphunzitsa kuti chikhululukiro chimabwera panthawi yomwe munthu
akhala ndi chikhulupiriro mwa Khristu monga mpulumutsi, ndipo kuti ubatizo umangoonetsera kuyeretsedwa komwe kwa chitika kale. Mbale Lipscomb anali mmodzi wa atsogoleri omwe anagwira
ntchito pakati pa mipingo ya Khristu kumwera kwa America. Iye anakhulupirira monganso ambiri a ife
tichitira, kuti ubatizo ndi nthawi yomwe ife timalandira chikhululukiro cha machimo. Koma iye
anakhulupirira kuti sikwabwino kubatizanso kawiri mbaptist yemwe anafuna kulowa m’misonkhano
yathu. Iye anafotokoza kuti popeza anthu omwe anatembenuka mwa a Baptist amakhulupiriranso
mpulumutsi yemweyo amene ifenso timkhulupirira, anamva chisoni chifukwa cha machimo awo,
ndipo anafunitsa kukhululukira machimo ndi kubwera kwa Khristu monga mpulumutsi wawo ndi
Ambuye wawo, ndipo popeza ambiri a iwo ndi cholinga choti akadzichepetse ndikudzipereka ku
cholinga cha Mulungu, onse omwe anachita zimenezi analandira ubatizo woyenera ndi wolondola.
Lipscomb anakhulupirira kuti ngati panali chikhulupiriro chodzichepetsa mwa Mulungu, sikunalinso
kofunikira kwenikweni kuti munthu amvetse bwino machitidwe a nthawi yomwe iye anayeretsedwa,
kapena kutsatira mwatsatanetsatane lemba lirilonse lofotokozera za dongosolo la ubatizo. M’Njira ina,
amanena kuti, ife tomwe tinabatizidwa popanda kumvetsetsa bwino za mphatso ya Mzimu Woyera
tinayenera kubatizidwanso kawiri kuti tilandire Mzimu Woyera. Nkhani yonse iri mu bukhu
Lolembedwa ndi Jimmy Allen lothedwa “kubatizidwanso” (Rebaptism).
B. Alaliki athu oyambirira aja a m'gulu losintha zinthu aja sanabatiza kawiri a Baptist aja ayi koma
anangowatenga iwo ngati ziwalo za thupi la Khristu. Mipingo yambiri ya Khristu ya ku mmawa kwa
mtsinje wa Mississippi ku America anachitanso mogwirizana ndi maganizo a Lipscomb, ndipo pa
Umodzi 43
mafika mzaka za m'ma 1980 iwo ochitira umboni uthenga anali kugwirizanabe ndi maganizo a
Lipscomb obatizanso kawiri. Mipingo yambiri ku Texas ku America, kumbali inayi, inakopedwa ndi
Mc Garry ndipo anayamba kuwatenga onse obatizidwa ndi a Baptist ngati osapulumutsidwa. Ine ndi
kukhulupirira kuti Lipscomb amalondola. Panalibenso njira ina yomwe tikanagwirizana kapena
kuganizira monga momwe taganizira kapena kugwirizanira pa ubatizo. Mwa chitsanzo, ngati malamulo
a boma lathu akanakhala kuti amafuna zonse, malumbiro a akwatiwo ndinso ………. Kuti apange ukwati weniweni wobvomerezeka, ndipo ngati akwatiwo adachita zonsezo koma ndi kuganiza iwo
analowa kale banja pochita malumbiro awo basi, ndani wa ife angathe kuwachititsa kuti abwererenso
nakayambenso ukwati wawo? Kodi sitikanakwanitsidwa popeza cholinga chawo chenicheni chinali
chofuna kulowa banja ndipo anachita zinthu zonse zofunikira? Ine ndi kuona njira ya Mc Garry
yobatizanso kawiri ngati gawo limodzi pa zochitika zoloza ku magawano ndi kulekana maganizo pa
malamulo, ndiponso losagwirizana ndi mtima kapena Mzimu wa uthenga. Ndipo ngati Lipscomb anali
wolondola ndi wokhoza, ndiye kuti tiri ndi abale ndi alongo ochuruka koposa momwe timaganizira.
6. Poonjezera pa kuononga komwe kumabwera chifukwa cha kugawanikana ku uthenga, munayamba
mwaganizira za momwe timachimwira pamene tikana abale ndi alongo omwe Mulungu anawalandira?
Kumbukirani wamkulu uja anamutcha mwana wolowerera uja kuti “mwana wanu uja” m’malo moti
“mbale wanga.” Kodi ife mwa kusadziwa kwathu sitinanenepo zinthu zina zonyoza anthu ena omwe ndi
odzadza ndi chikhulupiriro ndi odzipereka kwambiri kwa Khristu ndiponso ali a nzeru ndi odziwa malemba
monga ife tiriri? Mzaka zanga zoyamba ntchito yanga yotumikira ngati m’mishonare, ndinalemba nkhani
za ubatizo zomwe ndimaika kunja ana a Mulungu ambiri. Ndiri wodzadzidwa ndi manyazi ndipo ndi
kupempha chikhululukiro kwa Mulungu ndi kwa inu a mumpingo.
A. Ngati Mulungu amagwiritsa ntchito chizindikiro cha Mzimu Woyera monga chomdziwitsa za anthu
ake, kodi ife tingathe kunyalanyaza chipatso chobadwa chifukwa cha Mzimu Woyera wopezeka
m’miyoyo ya okhulupirira odziperekawa?
B. Kodi ife tokha tiri ndi choonadi chonse? Tiri ife kodi olungama, kapena tidalira pa chisomo? Ngati
tidalira chisomo, kodi ndiye kuti chisomocho chimangogwira ntchito pa kuperewera kwathu kokha,
kapenanso ngakhale zolakwika zosiyanasiyana ndi zofooka za anthu ena? Kodi tikudziwa ntchito
yaikulu yomwe chisomo chimagwira pamene anthu alemekeza Khristu monga Ambuye
mokhulupirika? Kodi tidayamba tapanga chisankho pakati pa chisomo ndi lamulo?
7. Tinasochera kuchoka pa kumvetsa bwino zomwe malemba anena za umodzi womwe unaphunzitsidwa ndi
omwe anayambitsa ntchito yobwezeretsa. Tiyenera kulapa ndi kupempha chikhululukiro cha Mulungu
chifukwa chokaniza ana ambiri a Mulungu powatcha akunja, osapulumutsidwa. Ntchito ya gulu lathuli
yakhala ikutsutsa ena chifukwa chogawikana ndi kulowa m'mpitatuko. Komanso pamene nafenso tiri ndi tchimo longa lomwelo. Mau oti “mpatuko” satanthauza “munthu yemwe amaphunzitsa kuti kudzilekanitsa
wekha podzitengera dzina la padera lakolako. Nakhale dzina loti mpingo wa Khristu ndi dzina labwino
ngati cholinga chathu chiri chongofuna kulemekeza Khristu, nkotheka kusagwiritsa ntchito dzinali
moyenera wampatuko ngati cholinga chathu ndi chodzilekanita ndi anzathu monga mpingo wokhawo
wokhulupirika woyenera kumasonkhana wokha. Baibulo limapereka maina ambiri ampingo, koma mipingo
yambiri yomwe tipembezako singalole kutchulidwa “mpingo wa Mulungu,” kapena “Banja la Mulungu,”
“ana a Mulungu.” Izi zikungoonetsa momwe ambiri a ife takhalira amipatuko pa za dzina loti “mpingo wa
Khristu.”
Tikukhala m’masiku oyipa ndipo kuipitsitsa kungabwerebe. Tiyenera kufikira ambiri a osochera monga
momwe tingathere. Ndi kovuta kukonza zofooka ndi zotchinjiriza zomwe zimasokoneza uthenga
zoyambitsidwa ndi malekano osafunika osabvomerezeka ndi Baibulo. Posachedwapa tidzaima pamaso pa
Mulungu. Tiyenera kuopa Mulungu koposa zinthu zomwe munthu sadzibvomereza. Tiyenera
kudzichepetsa ndikachita ndi pemphero la Ambuye lija la umodzi ndi chidwi chonse. Tiyenera kugwirana
dzanja ndi okhulupiria ena omwe anabadwanso mwatsopano kuzipembedzo zinazo, ndi anthu omwe mwa
iwo Mzimu Woyera akuchita nawo mwa chionekere. Kuti tichite izi sikuti tiyenera kutaya chimodzi cha
zikhulupiriro zathu za m’Baibulo. Pamene ubale pakati pathu ndi iwo ukukula, ndipo pamene akuona
Khristu mwa ife, adzayamba kulemekeza kwambiri Khristu pa china chirichonse chomwe Khristu
Umodzi 44
adzawaphunzitsa kudzera mwa ife. Ndipo ngakhale atapitirira kulekana maganizo pa zina zazing’ono
m’malemba, izi siziwachititsa kuti akhale anthu osochera ayi. Anthu sapulumutsidwa chifukwa
kukhulupirira bwino za mphamvu za Mulungu pozifanizira ndi chifuniro chake cha munthu, kapena pa za
Baibulo lotanthauziridwa bwino, kapena pa za mphatso za Mzimu Woyera kapena pa za makhalidwe ake a
pakutha pa zaka chikwi. Chomwe chimafunikira kwambiri ndi ubale wathu ndi Khristu. Ngati ena a ife
adzapulumutsidwe, chidzakhala chifukwa cha mphatso ya mwazi wa Khristu, osati chifukwa choti tinali olondola ndi ochita bwino pankhani zonse za malemba ayi.
Malekano akufa pang’onopang’ono m’malo ambiri. Anthu tsopano akukhala ndi chidwi chofuna kuiwala
kusinjirirana za mipatuko ndikuyamba kungomvera chiphunzitso cha Baibulo chosavuta. Mipingo yambiri
m’dera la kwathu posachedwapa yasiya maina odzipatsa chifukwa cha kupatukana. Mipingo yambiri ya
ganiza zomatsogoleredwa ndi akulu a mpingo kaya kuti oyang’anira – Abusa. Anthu a m’zipembedzo
zambiri akuitanitsa ziphunzitso zotsamira ndi kudalira Baibulo. Anthu mazana anayi (400) ochokera ku
zipembedzo zosiyanasiyana m’dera la Houston amalembetsa kuti alowe m’maphunziro ochitika pa sukulu
ya Baibulo ya South Houston chaka chiri chonse. Ife timaphunzitsabe zomwe tikhulupirira za Baibulo,
ndipo popeza timawaphunzitsa anthuwa mwa ulemu ndi modekha mwa Mzimu ndi moyo wa Khristu, iwo
amakondweretsedwa kubwera ndi kudzaphunzira.
Ngakhale mu Chikatolika mulinso kubwerera kumachitidwe a mpingo woyamba; mpingo uliwonse womwe
ndi womangidwa m’masiku ano ku Houston udzakhala nalo damu lobatizira pobiza thupi lonse. Mkulu
wina wachinyamata wa mpingo wa Hispanic anabwera ku ofesi kwanga sabata yathayo ali wosangala ndi
wotengeka chifukwa anali wofuna kuyamba maphunziro. Iye amachokera ku mpingo womwe unasankha
kudzitcha kuti “mpingo wobwezeretsa”. Iye amafulumiza kuzindikira za malingaliro athu obwerera ku
Baibulo. Sikuchokera zaka mazana awiri (200) zapitazo pamene takhala ndi mwayi wothandiza anthu kuti
akhale amodzi mwa kudzichepetsa kwa malemba.
Zoonjezera: Zothandizira Zina pa Phunziro la Umodzi
Mafunso Othandizira Phunziro la Aroma 14:1-15:13
1. Kodi anthu onse a mumpingo amamva mofanana, kapena ali ndi chidziwitso cha chikhulupiriro
chofanana? 14:1.
2. Kodi “nkhani zazing’ono” ndi chiyani? (14:1). Kodi mawu amenewa a masuliridwa motani m’mabuku
enawo?
3. Kodi mfundo zonse za choonadi cha chipembedzo zimamveka mofanana m’malemba? Kodi mfundo zonse
ndi zofunikira monga maziko a chipulumutso?
4. Kodi alipo Mafunso ena okhudza za chipembedzo kapena makhalidwe a Chikhristu omwe kungatheke kuti Akhristu awiri okhulupirika angathe kusiyana maganizo?
5. Kodi ndi nkhani ziwiri ziti zazing’ono zomwe Paulo apereka mona zitsanzo mu Aroma 14:2-8? Kodi
muganiza kuti kusiyana maganizo kumeneku kunachokera m’maganizo ati?
6. Kodi chikhulupiriro chofooka (kapena chidziwitso cha choonadi cha chikhulupiriro) chidampangitsa
bwanji kukhala ndi moyo wolimbikira kukana zina?
7. Kodi ndi zinthu zinanso ziti zomwe timaonetsa kulekana kwathu (zazing’ono) zomwe ziriponso pakati pa
Akhristu lero?
8. Kodi Mkhristu wolimbayo (wosabvutika ndi chikumbumtima chodziletsa) anayesedwa pokhala ndi moyo
wotani kwa mbale wake wofookayo? Kodi mbale wofookayo anayesedwa ndi moyo wotani kwa mbale
wake wosamangikayo? 14:3,10.
9. Kodi Paulo anamlamulira chiyani mbale wolimbayo? Nanga wofookayo, womangikayo? 14:3,10.
Umodzi 45
10. Kodi pamenepa ndiye kuti Paulo akunena kuti anthu angathe kukhala ndi zikhulupiriro zosiyana ndinso
machitidwe osiyana munkhani zimenezi komabe ndi kumakhalirana bwino mwa mtendere mumpingo
umodzi?
11. Kodi ziripo mfundo zina zofunikira ndinso choonadi chomwe tonse tiyenera Kudzibvomereza ndi
kuzilandira ngati tifuna kuti tikhale amodzi? Aefeso 4:1-6; 1 Akorinto 15:3-8; 1 Timoteo 3:16.
12. Nchifukwa chiyani payenera kukhala kulolerana ndi kugonjerana pokhudza nkhani zazing’ono ngati tifuna
tigwire ntchito ngati mpingo?
13. Nchifukwa chiyani kuli kobvuta kugwiritsa ntchito chiphunzitso ichi cha kulolerana ndi kugonjera pa
mfundo zokhudza kupembedza kwa gulu lonse osati pa mfundo zokhudza kungosintha chabe?
14. Kodi tilipire yani nkhani za zolimbana zazing’ono zing’onozi? 14:10-12.
15. Kodi abale omwe asiyana maganizo ayenera asachite chiyani? Ayenera alimbikire chiyani? 14:13.
16. Ngati munthu akayika ndi china kapena mfundo ina, kodi iye mwini ayenera kuchita chiyani? 14:14,23.
17. Ngati mbale wofookayo womangika m'chikumbumtima ali pomwepo kapena zimkhudza, kodi mbale
wolimbayo wosakaikayo asachite chiyani? 14:13-21.
18. Nanga naye mbale wofookayo, kumbali yake asachite chiyani? 14:3,13.
19. Kodi ndi kulakwa kuti mbale wofookayo odzudzula ufulu wa mbale wake wolimbayo monganso momwe
mbale wolimbayo kuchita zinthu zomwe zikhumudwitse mbale wofookayo? Kodi machitidwe awiri
onsewa amalimbikitsa kulakwirana ndi magawano pakati pa Akhristu?
20. Kodi tiyenera kuika umodzi ndi moyo wabwino ndinso kuchita bwino kwa mpingo patsogolo pa chiyani?
21. Kodi olimba ayenera kumachita chiyani? Nanga sayenera kumachita chiyani ngati atsata chitsanzo cha
Khristu? 15:1-3.
22. Nchifukwa chiyani kumakhala kosabvuta kuti mbale wolimba azindikire kuti nkhani iyi ndi yaing’ono
kusiyana ndi mbale wofooka? Kodi zingatheke kuti mfundo ina iwoneke ngati lamulo koma ndi kutheka
kuti ine ndizindikirebe kuti pali mpata woti ndi sagwirizane nazo mokhulupirika?
23. Tiyenera kumalolerana wina ndi mnzake m'njira yomweyo yonga ndani analandira ndani?15:7.
24. Kodi zimene zija zinangochitika chifukwa cha kuchita bwino kwathu, kapena chifukwa cha chisomo?
25. Ngati mbale wolimba uja ndi wofooka uja analibe chidwi chochita ndi kulekana maganizo kwawo
mogwirizana ndi maganizo a Paulo aja mundimeyi, koma kulimbikira pa kudzudzulana kapena
kunyozana, kapena kulakwirana mwadala kotero kuti kulekana kukanayambika, kodi mpingo
ukadatani nawo? 16:17,18.
26. Yemwe anachita motere sanatumikire Khristu kapena kukonda koma anali kutumikira chiyani?
27. Kodi 1 Akorinto 8:1-13 ndi 10:23-33 akulozera chiyani munkhani imeneyi?
28. Sititaya kwakukulu ngati titaya nyama ndi cholinga chofuna kupewa choyambitsa kupunthwa. Koma nanga
bwanji ngati palinso china chomwe mpingo ukanapindula nacho ndi kufikira mizimu yambiri, koma
chikhumudwitsa m’modzi kapena awiri mumpingo? Kodi nthawi zina timathawitsa abale kapena
kufooketsa abale ambiri ndi cholinga chofuna kupewa kukhumudwitsa ochepa? Kodi Paulo amatanthauza
zimenezi pa chiphunzitso chake cha m’misonkhano chija?
Umodzi 46
Zothandiza Powerenga Aroma 14:1-15:7
Mu Aroma 14:1-15:13 Paulo akupitiriza kuphunzitsa za machitidwe akhalidwe ndi moyo wa Mkhristu
malingana ndi chifundo chomwe Mulungu wationetsera. Gawo limeneli likuona mwapadera momwe
tingakhalire ndi umodzi mumpingo ndinso monga abale ndi alongo mwa Khristu, ngakhale timakhala nako
kusiyana m’maganizo ndi zikhulupiriro pa nkhani zina “zazing’ono.” Iri ndi bvuto lomwe limakhalapo chifukwa cha umunthu wathu wauchimo kuchokera mu zifukwa zosiyansiyana ndi masiyanidwe a makulidwe
m'nzeru ndi kukhwima.
Zoyenera kuyang’ana mu Aroma 14:1-15:13
14:1: Yemwe chikhulupiriro chake chiri chofooka mumlandire. Yemwe ali womangika malinga ndi
chikumbumtima chake ndipo “amangosiya” zinthu zambiri zomwe Mulungu sanaletse; yemwe sanakhwime
m’chikhulupiriro ndi chidziwitso cha Khristu kokwanira kuti amvetse ufulu womwe tiri nawo mwa Khristu.
Popanda kuweruza pa zinthu zazing’ono [NASB: osati ndi chifukwa chofuna kuweruza malingana ndi
maganizo ake; RSV: koma osati chifukwa cholimba pa maganizo.]
Mawu a Mulungu anazindikira kuti chifukwa cha kufooka kwathu kwa umunthu, mfundo zonse zolondola
kapena zolakwika zimamveka bwino kwa ife, choncho zina ndi zoti titha “kulekana maganizo.” Komanso
m’malembo sananenemo zambiri za Mafunso ena koposa enanso. Mpata ulipo kwa anthu okhulupirika, oopa
Mulungu wosiyana maganizo munkhani ngati zimenezi.
Malembonso amazindikira kuti sinkhani zonse za chikhulupiriro cha Chikhristu chachikulu mofanana kapena
mofunikira – Mateyu 5:19; 23:23. Alipo malemba omwe ali ndi mndandanda wa ziphunzitso ndi zikhulupiriro
zazikulu – Aefeso 4:4=6; 1 Akorinto 15:3=4; Aroma 14:17; Mateyu 22:35-40. Ziphunzitso zazikulu zimenezi
zomwe ziri monga maziko zimaphunzitsidwa m’malemba kawirikawiri komanso mwadongosolo kuposa zina
zazing’ono zija. Palibe mwayi waukulu wololedwa kulimbana pa ziphunzitso zazikuluzi.
Mulungu amvetsa mwangwiro, koma amadziwa kuti ife sitiri choncho ayi. Gawo limeneli likuonetsa poyera
kuti titha kukhalirana pamodzi ndi kumagwira ntchito pamodzi mumpingo popanda kugwirizana pa mfundo
zina zazing’ono, zomwe pa umunthu wathu mwayi ulipo woti titha kutsutsana mokhulupirika. Palibe wina wa
ife yemwe amaona zinthu mwangwiro, kapena yemwe amamvera mwangwiro. Chisomo chiyenera kutchinjiriza
kusamvetsa kwathu monga momwe chimatchinjirizira kusachita mwangwiro kwathu. Ndipo tiyenera kuchitira
chifundo iwo omwe timalekana nawo maganizo monga momwe Mulungu amapatsiranso ife chisomo. Tiyenera
kukana yemwe akana chiphunzitso ndi chikhulupiriro chachikulu, chofunikira chenicheni cha Chikhristu – 2
Yohane 9-11. Koma tiyenera kulandira, osati kukana, yemwe tasiyana naye mu nkhani ndi mfundo
“zazing’ono.”
Kodi tingadziwe bwanji zomwe ziyenera kutengedwa ngati nkhani zazing’ono?
14:2-12: Kuchokera mu mpingo wa ku Roma, Paulo akupereka zitsanzo ziwiri za nkhani zazing’ono zomwe
Akhristu angathe kusiyana maganizo komabe ndi kumagwira ntchito pamodzi mwa Khristu. Chikhulupiriro cha
munthu wina chimlola kudya chirichonse (iye akudziwa kuti Yesu “anayeretsa zakudya zonse” – Marko 7:19 –
ndi kutinso “fano sirili kanthu” – 1 Akorinto 8:4) – Koma munthu wina, amene chikhulupiriro chake chiri
chofooka, adya masamba okha. Iye akhulupirira kuti ndi kuchimwa kapena kungakhale kuchimwa kudya
nyama. Omasulira ena amaganiza kuti yemwe akumangikabe ndi lamulo la Chipangano Chakale la zakudyali
ndi Myuda. Ena amaganiza kuti ndi wa amitundu yemwe wangotembenuka kumene kuchokera ku kupembedza
mafano yemwe tsopano ali wosamala kwambiri pa za chakudya chomwe chikuperekedwa ku mafano poyamba
ndipo kenako kugulitsidwa ku misika yakunja. Atha kuganiza kuti chakudyacho chaipitsidwa mwa uzimu
chifukwa chinaperekedwa kwa mafano m’mbuyomo. Myudanso angaganize mwa mtundu womwewo.
Chikhulupiriro cholimba chingamuthandize munthu ameneyu kuti aone kuti chakudya ndi chakudya ndiponso
kuti fano liribe uzimu weniweni. Fano ngakhale mdierekeze wokhala pambuyo pa fanolo alibe mphamvu ya pa
munthu wina aliyense kupatula munthu yekhayo amene aopa fanolo m’maganizo mwake. Koma ngati fanolo
alilumikiza m’maganizo ake mwa uzimu ndi chakudyacho pamenepo ndiye kuti chakudyacho chiri
chosayeretsedwa kwa iyeyo.
Umodzi 47
Mwa chitsanzo china, mundime 5, munthu wina atenga tsiku lina monga loyera kuposa linzake; wina
angotenga masiku onsewo monga chimodzimodzi. Kusunga tsiku loyamba la Sabata monga “tsiku la Ambuye”
pokumbukira kuukanso kwa Khristu sinkhani yomwe iri mumtima ayi. Tsiku limeneli linalandiridwa ndi
Akhristu onse oyamba aja ngakhale anali ndi maganizo osiyanasiyana pa za masiku enawo. Pano Paulo
akunena za masiku achipembedzo a padera, a munthawi za Chipangano Chakale ndi malamulo ake aChiyuda:
masabata kapena masiku opumula Mulungu uliwonse, kulemekeza “kutuluka kwa mwezi uliwonse”, ndi miyambo yina yachipembedzo yochitika chaka ndi chaka mwa chitsanzo paska, Pentekoste, kumasulidwa ndi
zina zotero
Chikhulupiriro cha uthenga wabwino chidawamasula Akhristu, kaya Ayuda, kaya amitundu ku kudalira pa
zinthu zimenezi (Akolose 2:13-17), koma ngati china chinali cholinga cha Mulungu, nkobvuta kuti tichisiye
ndikuyamba choonadi chinanso chatsopano. Choncho tiri ndi Akhristu ena mumpingo wa ku Roma omwe
akudya nyama pamene ena sadya; ena akusungabe mwambo wakale cha Chiyuda wosunga ndi kulemekeza
masiku ena pamene ena satero ayi.
M’masiku ano tiribe bvuto limeneli kwenikweni mumpingo koma tiri ndi mabvuto ena olekana maganizo pa
nkhani zina “zazing’onozing’ono”. Pali nkhani za khalidwe labwino, lobvomerezeka: Kodi kubvala kwabwino
ndikuti? Kodi amuna ndi akazi asambe malo amodzi kunyanja? Kodi Mkhristu abvine dansi? Kodi ndi zithunzi
ziti zomwe Mkhristu sayenera kuona? Kodi nyimbo zonse za magatala ndi zachabe? Kodi Mkhristu achite ndi
fodya? Kodi kungolawa pang’ono ndi kwachabe, popeza munthu saledzera nako? Kodi pa nthawi yochezerana
mwamuna ndi mkazi, khalidwe lobvomerezeka ndi liti?
Palinso Mafunso ena a chipembezo ndi ntchito za mpingo, zomwe zina za izo zitsatidwa ndi kuchitidwa ndi
maganizo osiyana pakati pathu mobwerezabwereza: Kodi tikhale ndi mgonero wa Ambuye kangati? Kodi
tiyenera kukhala ndi kalasi mumpingo? Kodi tikhale ndi zikho zingati zomwera chipatso cha mpesa munthawi
ya mgonero? Kodi nyimbo zoimbira ndi zida ndi zobvomerezeka m'chipembedzo? Kodi mwamuna amene
analekana ndi mkazi wake mwa malemba angathe kukhala woyang’anira/mbusa? Kodi nchoyenera kuika
atumiki achikazi? Kodi mipingo ingathe kugwirizana kudzera mu utsogoleri wa mpingo womwe wayambitsa
ntchitoyo pa ntchito zina zazikulu? Kodi ndi chobvomerezeka kuomba m’manja mumpingo? Kodi zisudzo
zimaloledwa mumpingo? Komanso pali Mafunso ena a ziphunzitso ndi zikhulupiriro: Kodi Khristu adzabwera
patapita zaka chikwi kapena pasanapite zaka chikwi? Kodi mphatso za zozizwitsa zikuchitikabe mumpingo
lero? Kodi zimatheka kuti Mkhristu agwe kuchoka m’manja mwa Khristu ndi kutayika?
Pamene Akhristu asiyana maganizo “pankhani zazing’ono,” machimo awiri amayenera kufika: mbale wolimba
yemwe mwa chikhulupiriro chake amadya nyama anganyoze mbale wofooka yemwe chikumbumtima chake
chimletsa; ndipo mbale wofookayo angadzudzule mbale yemwe ali ndi ufulu uja. Paulo akuletsa zonsezi.
Munthu yemwe adya zonseyo asanyoze (NASB): tiganizirane mosanyozana; RSV: osanyoza) iye amene sadya;
ndipo munthu amene sadya chirichonse asadzudzule (NASB: asaweruze; RSV: asaike chiweruzo pa) munthu yemwe amadya. Chifukwa chiyani? Popeza Mulungu amulandira iye. Mulungu angalandire munthu yemwe
kwa ine aoneka monga wolakwa.
Munthu yemwe ali ndi chikumbumtima cha choonadi, yemwe adziwe zambiri za chikhulupiriro, nthawi zonse
amakhala pa mayeso odzitukumula podziona ngati wapamwamba kuposa wina yemwe sanadziwe kwambiri
uja, pomutenga ngati wosafunikira kwa Mulungu ndi mpingo. Chidziwitso chimatukumula, koma chikondi
chimamangirira. Munthu yemwe aganiza kuti adziwe zambiri alinakonso kuperewera kwina” – 1 Akorinto 8:1-
2. Kudzitukumula ndi dzenje la anthu omwe amaganiza kuti iwo ndiye odziwa kuposa ena onse. Munthu
womangidwa ndi chikumbumtima uja, ngakhale kuti kwenikweni zimachitika chifukwa cha kusakhwima mu
uzimu, nayenso amakhala pa mayeso oganiza kuti mbale wake wokhala ndi ufulu uja, ngati wosasamalira
malamulo a Mulungu ndi kumudzudzula. Kumakhala kobvuta kwa iye kuti azindikire “nkhani zazing’ono”
monga momwe ziriri ndi kusiyira zina zonsezo kuti Mulungu ndiye aweruze pamene iye apitiriza kutumikira
Mulungu.
Bvuto la maganizo a mbale wolimbayo lingathe kuononga ubale ndi kubvulaza umodzi wampingo. Kudzudzula
komwe mbale wofooka uja amachita mwa chisawawa kwa ena kungathenso kuononga ubale ndi umodzi. Ngati
mmodzi wa onsewa achita zimenezi mpaka kufika poti pakhale kulekana ndi kugawikana, Paulo akulamulira
Akhristu kuti tisamale naye ndi kupatuka pa iye. Munthu woteroyo angodzisangalatsa ndi zomkondweretsa iye
mwini (kukakamira kufuna kutchedwa wochita bwino mwa yekha kapena chakudya, kapena kuchita
mwangwiro). Iyeyo sakutumikira Khristu – Aroma 16:17,18.
Umodzi 48
Bvuto la maganizo a mbale wolimbayo lingathe kuononga ubale ndi kubvulaza umodz wampingo. Kudzudzula
komwe mbale wofooka uja amachita mwa chisawawa kwa ena kungathenso kuononga ubale ndi umodzi. Ngati
mmodzi wa onsewa achita zimenezi mpaka kufika poti pakhale kulekana ndi kugawikana, Paulo akulamulira
Akhristu kuti tisamale naye ndi kupatuka pa iye. Munthu woteroyo angodzisangalatsa ndi zomkondweretsa iye
mwini (kukakamira kufuna kutchedwa wochita bwino mwa yekha kapena chakudya, kapena kuchita
mwangwiro). Iyeyo sakutumikira Khristu – Aroma 16:17,18.
Ndi kulakwa kuti mbale aliyense aweruze mbale wake (kumtsutsa kapena kumtenga ngati wopanda pake). Kodi
ndiwe yani woti ukaweruze wantchito wa mwini wake? Mbale aliyense amayang’aniridwa ndi kuyankha zonse
kwa Mulungu poyambirira. Sindiyenera kutenga udindo wa Mulungu wakuweruza. Munthu amaima kapena
kugwa kwa Ambuye wake (yemwe ndi Mulungu). Ndipo adzatha kuimanso, chifukwa Ambuye angathe
kumthandizanso kuti aime, ngakhale atakhala ndi zomwe zioneka ngati zolakwika, malingana ndi zomwe ine
ndiganiza ndi kukhulupirira pa nkhani zina zazing’ono.
Paulo atipatsa mitu itatu yoti ititsogolere pa khalidwe lathu mu ndime imeneyi:
1. Aliyense akhale wokhutitsidwa mumtima mwake (v5c). Aliyense wa ife ali ndi udindo womvetsa ndi
kuganizira mosamala kwambiri chomwe akukhulupirira kuti ndicho cholinga ndi chifuniro cha Mulungu pa
nkhani kapena mfundo iriyonse. Ngakhale sitingathe kumva mvemvemve monga amachitira Mulungu,
tiyenera kukhala ndi njala ya kumva malembo monga momwe tingathere. Tiri ndi udindo wophunzitsa
chikumbumtima chathu. Ife sitiri oweruza maganizo a wina aliyense ayi.
2. Ngati wina aliyense aona chinthu china monga chodetsedwa (choipa) ….. kwa iyeyo ndi chodetsedwa ……
munthu yemwe akaika achimwa ngati adya, chifukwa sadya ndi chikhulupiriro (vv. 14b,23). Ngati
ndilakalaka kuchita chinthu chomwe ndi kuchikaikira kapena kukhulupirira kuti ndi choipa, ndiye kuti ndiri
ndi mzimu wa wochimwa wa chilakolako ngakhale kuti Mulungu saletsa chinthu chomwe ndikuchitacho.
Ndiyenera kumalolera maganizo a ena pa nkhani ndi mfundo zazing’ono, koma ndiyenera kumvera
mosamalitsa chomwe chikumbumtima changa chindiuza kuti ndi chobvomerezeka.
3. Ganizirani kuti musaike chopunthwitsa kapena cholepheretsa chirichonse m’njira ya mbale wanu.
Malingana ndi kukhwima kwa chikumbumtima chanu, chingathe kukulolani kuchita zinthu zina zomwe ena
amaziona ngati zoipa ndi zolakwika, komabe musamangochita zimenezi nthawi iriyonse kapena pamalo
pena paliponse pomwe zingabvutitse ndi kuyambitsa mabvuto kwa mbale kapena mlongo wanu.
Iye yemwe aona tsiku limodzi ngati lofunika kuposa linzake, atero kwa Ambuye. Iye yemwe adya nyama kwa
Ambuye, chifukwa ayamikira Mulungu, ndipo iye yemwe sadya, atero kwa Mulungu. Ndi chinthu chofunika
kudziwa ndi kuchita chifuniro cha Mulungu molondola monga momwe tingathere, koma koposa zonse, ndi kofunikira kuchita zonse zomwe timachita ndi cholinga cholemekeza Mulungu. Ngakhale sitimvetsa
bwinobwino, Mulungu amazindikira cholinga chathu chofuna kumulemekeza ndi kumumvera. Kaya moyo
kaya imfa, ife ndife ake a Ambuye. Ife tiri m’manja ake mu zonse, pa zonse ndipo timayankha china chiri
chonse kwa iye, tiri pansi pa ulamuliro wake m’zonse, koposa wina aliyenseyo, ndipo tiyenera kuchita china
chirichonse chomwe tingathe kuti timkondweretse.
Uweruziranji mbale wako ….. upepusiranji mbale wako? Popeza tonse tidzaima pampando wachiweruzo wa
Mulungu. Ngati ndiweruza mbale wanga yemwe “ali womasuka” kusiyana ndi ine munkhani zazing’ono, ndiye
kuti ndi kutenga malo ndi udindo wa Mulungu wakuweruza. Ngati ndinyoza ndi kupepusa mbale wanga
womangiririka ku chikumbumtima chake, chimodzimodzinso ndiye kuti ine ndi kudzikweza koposa iyeyo,
chinthu chomwe ndi Mulungu yekha angathe kuchichita mwa mphamvu yake. Podziwa kuti tonsefe tidzaima
pampando wachifumu ndi kunena ntchito zathu zonse kwa Mulungu tiyenera kukhala odzichepetsa pochita ndi
anzathu pamene pabuka kusamvana. “Musaweruze pakuti inunso mungaweruzidwe. Popeza m’njira yomweyo
muweruzira ena, inunso mudzaweruzidwa nayo.” – Mateyu 7:1,2. “Choncho aliyense wa ife adzafotokoza
yekha ntchito zake kwa Mulungu. Choncho ziripotu zinthu zina zomwe ndiribe ufulu woweruza. Nditha
kungozisiyira pakati pa Akhristu anzanga ndi Mulungu.
Izitu sizitanthauza kuti sitiyenera kuweruza pa chirichonse chabwino kapena choipa. Mu Aroma 14, Paulo
sakunena za zinthu zazikulu, zodziwikiratu za zabwino ndi zoipa, koma iye akunena za zinthu zazing’ono
zomwe tiri nawo mpata wokambirana. Akhristu pamodzi ndi atsogoleri, nthawi zina amapatsidwa mwayi
Umodzi 49
woweruza zina zazing’ono – 1 Yohane 4:1-3; 1 Akorinto 5; Mateyu 18:15-20; Machitidwe 17:11. Tiyenera
kukhala ndi luntha pamodzi ndi nzeru zotithandiza kusiyanitsa mfundo zazikulu zosayenera kusewera nazo
mwa uzimu ndi mfundo zazing’ono zomwe tingathe kuweruza. Kufooka kwathu pa mfundo imeneyi ndiko
kuwalowetsa “libolonje” m’mbiri ya mpingo.
14:13-23: Choncho (popeza tonse tidzaweruzidwa ndi Mulungu), tiyeni tisiye kumaweruzana (kaya ndi mbale wamphamvu kunyoza mbale wofooka, kapena wofooka kudzudzula ndi kuweruza wamphamvu ndi
wolimbayo) m’malo mwake sankhani kusaika chopunthwitsa kapena chokhumudwitsa, m’njira ya mbale wako.
Ngati ine mwa ufulu wanga, ndichita chomwe chioneka cholakwika ndi chosabvomerezeka kwa wofooka uja,
ndiye kuti ndingamupunthwitse munjira ziwiri:
1). Ndimupangitsa kuti kukhale kobvuta kwa iye kuti iye ndi ine tikhale “amodzi” – angathenso kusiya
kusonkhana ndi kupembedza;
2). Ndimupangitsa kupitiriza kuchita zomwe inenso ndi chitazo ngakhale zioneka zolakwika kwa iyeyo ndipo
potero adzaswa maganizo a chikumbumtima chake pochita zimenezi. 1 Akorinto 8:1-13 ndi 10:23-33 ndiwo
maziko a chaputala chimenechi omwe ayenera kuwerengedwa ndi mavesi omwe alembedwawo. Ine
ndikhulupirira kuti palibe chakudya chomwe ndi chodetsedwa mwa chokha. Koma ngati wina aona chinthu
china ngati chodetsedwa, ndiye kuti chinthucho ndi choipa kwa iyeyo ndipo zidzakhala chomwecho mpaka
pomwe chikumbumtima chake chidzamasuke chifukwa cha kukula mu chikhulupiriro. Taonani vesi 23 ndipo
mufanizire. Munthu yemwe akaikira aweruzidwa ngati adya, chifukwa sadya ndi chikhulupiriro; ndipo china
chirichonse chomwe sichichokera ku chikhulupiriro chiri tchimo.
Chikondi chenicheni sichikondwera kubvutitsa anthu ena. Ngati mbale wako akhumudwa ndi chomwe iwe
ukudya, ndiye kuti iwe suchita mwa chikondi. Chakudya chanu (kaya china chirichonse) pamenepa ndiye kuti
chafika pa ndime yofunikira koposa mtendere wa mbale kapena mlongo wanu komanso ndi ubale wanu.
Khristu anafa, anapereka moyo wake, kupulumutsa mbale wanuyo. Simaganizo abwino ngati simudzalolera
kusiya nyama ya nkhumba (kaya china chirichonse) ndi cholinga chofuna kupewa kumutengera kukuonongeka.
Taonaninso ndime 20: Musaononge ntchito ya Mulungu (Mzimu wa mbale wanu ndi ntchito yonse yomwe
Mulungu anachita kuti aipulumutse) chifukwa cha chakudya.
Musalole kuti chomwe muchiona ngati chabwino anthu anene kuti ndi choipa. Paulo sakunena kuti “musalole
mbale wanu wofooka kukuletsani chomwe chikumbumtima chanu chikulolani kuchita.” Koma akunena kuti
chomwe muchiona ngati choyenera ndi chabwino chingathe kukhala chodetsedwa ngati muchigwiritsa ntchito
yoti muvulaze moyo wa uzimu wa mbale wanuyo. Ngati khalidwe lanu limadalira kapena lilingana ndi ufumu
wakumwamba, chiyero, ufulu, chimwemwe ndi zokhazo zomwe mudzakhala mukuganizira kwambiri, osati
kaya mudya kaya mumwa chomwe mumakonda, kaya kubvala chirichonse, kaya kupita kuzikondwerero zina.
Ngati tiika chiyero, ufulu, chimwemwe ndi mtendere wa abale anthu ndi alongo athu patsogolo koposa zonse zodzikondweretsa tokha, ndiye kuti tikukondweretsa Mulungu ndipo tiri kubvomerezedwa ndi anthu.
Choncho tiyeni tiyesetse kulimbika ndithu kuchita chirichonse chomwe chikapherezere ku mtendere ndi kukula
koyenera. Ngati ichi chitanthauza kusiya zinthu zina zomwe ziri zobvomerezeka nane koma zokhumudwitsa
kwa mbale wanga wofookayo, zikhale chomwecho. Chakudya chonse ndi choyeretsedwa, koma sibwino kuti
munthu adye china chirichonse chomwe chingapunthwitse winayo.
Chirichonse chomwe mukhulupirira zinthu zimenezi (zakudya, masiku ndi zina zotero) zikhale pakati pa inu
eni ndi Mulungu wanu. Paulo sakutanthauza kuti nkosayenera kukambirana za zimenezi ndi mzimu wabwino
pakati panu ndi iwo omwe tisiyana nawo maganizo, kapena kuphunzira nawo pamodzi ndi cholinga chofuna
kuchepetsako kusamvanako. Iye akutanthauza kuti kaya maganizo anga “ndi omasuka” kaya omangika,
sindiyenera kumangoumirira pa maganizo anga omwewo ndi kulimbikitsa makangano. Maganizo athu
asadzadze ndi moyo wongofuna kulimbana pa mfundo zazing’ono koma adzadze ndi mfundo zazikulu ndi
zofunikira za Khristu. Paulo afuna kuti tonse tigwirire ntchito pamodzi ngakhale timasiyana m’maganizo ndi
mfundo zazing’ono ndikuti tisiyire kuweruza komaliza pa mfundo zazing’ono kwa Mulungu mwini.
15:1-3: kumbukirani kuti panalibe kulekanitsa machaputala ndi mavesi pamene Paulo anali kulemba kalata
imeneyi. Iye akupitirizabe kufotokozera maganizo ake pa bvuto limodzi lomweli mu chaputala 15. Ndipo ife
amene tiri olimba tiyenera kunyamula zofooka za opanda mphamvu ndi kusadzikondweretsa tokha - podya
kapena kuchita chirichonse chomwe chitikondweretsa. Ndi zoona kuti mbale wofooka womangidwa ndi
Umodzi 50
chikumbumtima akulamulidwa kuti akhale wololera anzake ndi wosaweruza chimodzimodzi mbale wake
wamphamvu uja ndi wosamangika uja yemwe alamulidwanso kuti ataye ufulu wake chifukwa cha mbale wake
wofooka uja. Koma popeza mbale wolimbayo ndiye ali nazo mphamvu, ntchito yaikulu yosunga ndi kusamalira
mtendere ndi kupewa kulakwa iri kwa iyeyo. Thupi lathu lakale la uchimo lodzikonda silifuna kunyamula
ntchito imeneyi. Iyi ndi ntchito yotheka kwa munthu watsopano wopulumutsidwa. Munthu wakale uja ayenera
kupachikidwa ndi Yesu.
Yesu anati, “ngati wina afuna kunditsata ine, iye ayenera kudzikana yekha ndi kunyamula mtanda wake tsiku
ndi tsiku ndi kunditsata ine. Pakuti aliyense wofuna kupulumutsa moyo wake adzautaya, koma yense wotaya
moyo wake chifukwa cha ine adzaupeza – Luka 9:23-24. Mtanda uyimirira moyo wobvuta ndi wopweteka kwa
ife koma wobweza ndi kupulumutsa ena. Moyo wathu wakale umafuna kudzikondweretsa okha, osati
kukondweretsa enawo mwa kutaya ufulu wathu. Ichitu ndi chifukwa chake “kudzikana” liri monga gawo
loyamba pa ulendowu monganso anamchitira Yesu. Aliyense wa ife akondweretse mbale wake kuti
zimuyendere bwino, kuti amlimbikitse akule bwino.
Paulo anasiya ufulu wake wolandira thandizo lochokera kwa abale ampingo wa ku Korinto ndi cholinga choti
ntchito yofalitsa uthenga ikhale ndi mphamvu – 1 Akorinto 9:12. Iye anangokhala “chirichonse kwa anthu
amitundu ulionse,” kusiya zina zomwe iye anali kudzikonda koposa mu nkhani za miyambo yake ndi
chipembedzo kuti akathe kugwirizana bwino ndi gulu liri lonse lomwe iye akapezeke akugwirako ntchito ya
Mulungu – 1 Akorinto 9:19-23. Kuchotsa zizolowezi za miyambo yamakolo ake zomwe zikanakhoza
kulepheretsa uthenga kufika kwa anthu kunali kofunikira kwambiri kwa iye koposa kungochita zomsangalatsa
iye kumbali yake. Paulo anali wokonzeka “kuononga chirichonse chomwe anali nacho ngakhale kudzipereka
iye mwini kuphatikizaponso Akorinto aja mu uzimu – 2 Akorinto 12:15. Iye sanachite zimenezi chifukwa
zimamukondweretsa iye mwini, koma chifukwa anasamalira kwambiri za chipulumutso cha ena koposa zinthu
zina zodzikondweretsa nazo yekha mwini.
Paulo anafotokoza zikhulupiriro zake mu 1 Akorinto 10:31-33:
1 “Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani
zonse kuulemerero wa Mulungu”
2 “Musachimwitse wina aliyense, kaya ndi Myuda, Mhelene kapena mpingo wa Mulungu.”
3 “Ndimayeserera kukondweretsa aliyense m’zonse, chifukwa sindifuna kuti wopindula ndikhale ine koma
unyinjiwo, kuti apulumutsidwe. Ndiponso anati, “mutengere chitsanzo changa monganso ine nditsanzira
Khristu.” 11:1.
Popeza ngakhale Yesu sanadzikondweretsa yekha. Iye sanasiye malo ake abwino ndi ufulu wokhala
m’ulemerero wakumwamba chifukwa pansipano panali pomkomera, koma chifukwa chakuti Iye anali
wamphamvu ife tinali ofooka, ndipo sitikanatha kudzithandiza tokha. Khristu anali “Mulungu m’zonse,” koma
“anadzichepetsa kotheratu nakhala wapansipansi” (RSV: “anadzikhuthula yekha”) – Afilipi 2:5-8. Iye anakhala
kapolo wathu, potiganizira ife, osati yekha. (Ndi chifukwa chake timsirira koposa) Iye anatinyamulira machimo
athu ndi zolemetsa zathu. Ndipo mfundo yaikulu ya ife Akhristu m'moyo ndi makhalidwe athu ikhale yofuna
kufanana ndi Khristu munjira zomwe tichitira ndi anthu onse.
15:4-7: Pakuti zonse zomwe zinalembedwa kale, zinalembedwa ndi cholinga choti ife tiphunzire. Pamenepa
Paulo anangotenga malembo amenewa kuchokera mu Chipangano Chakale. Ife Akhristu sitiri omangidwa ndi
lamulo la m’Chipangano Chakale, koma malembo a m’Chipangano Chakale ali odzala ndi umulungu ndi
mfundo zake. Ife timaphunzira zambiri za Mulungu ndi makhalidwe ake kuchokera mu malemba amenewa.
Ndipo kuti tithe kumvetsa bwino Chipangano Chatsopano tiyenera kukumba kuchokera ku maziko a
Chipangano Chakale.
Mulungu yemwe amapereka chipiriro ndi chilimbikitso (zofunika ziwiri pa umodzi wa abale) akupatseni inu
Mzimu wa umodzi pakati panu pamene muli kutsata Yesu Khristu. Umodzi ndi chinthu cha uzimu monganso
cha chikhulupiriro. Mzimu wa umodzi ndi wofunikira monga kufunikiranso kwa kugwirizana pa zikhulupiriro
za mfundo zazikulu zikulu.
Umodzi 51
Anthu atha kumabvomerezana pa zikhulupiriro ndi ziphunzitso komabe kumapezeka osiyana maganizo
m'zambiri chifukwa cha mtima wa makani ndi wodzitukumula. Malekano ambiri omwe anthu amati amayamba
chifukwa cha kusamvetsa bwino ziphunzitso ndi zikhulupiriro, ponena zoona amayambira pa uzimu
wodzikondweretsa makani ndi kulimbanira kupambana – “ndikhale wamkulu.” Nkhani ya ziphunzitso ndi
zikhulupiriro imangopangitsa kuti kulekanako kukhale ngati ndi kwabwino. Pakanakhala kuti panali chikondi ndi kudzichepetsa kwa mzimu, ndiye kuti abale akanatha kupeza njira yothetsera bvuto la kukhala ndi
ziphunztso ndi zikhulupiriro zosiyana yomwe ikanatha kuwathandiza kugwirira ntchito pamodzi.
Theka lamachimo omwe asanjidwa “m’ntchito za thupi” – Agalatiya 5:19-21 – nthawi zonse zimapezeka
m'kugawanika kwa mpingo. Kumbali inayi, “chipatso cha Mzimu ‘Woyera” – Agalatiya 5:22-23) ndicho
chenicheni chomwe chimapangitsa kuti abale ndi alongo athe kugwirira ntchito pamodzi ngakhale ali nazo
zofooka zawo aliyense payekha.
Mwa chidziwikirenso, choncho, umodzi mumpingo umadalira kwambiri pa “kufa kwa munthu wakale wa
uchimo, kubadwanso mwa uzimu, moyo watsopano monga momwe zimakhalira ndi momwe timvera
ziphunzitso ndi zikhulupiriro. “Mu chaputala chonena za umodzi” cholembedwa ndi Paulo Aefeso 4, Paulo
watenga nthawi m'mavesi atatu oyamba pofotokoza za mmodzi wa uzimu, ndipo mavesi ena atatu otsatiranawo
Paulo wafotokozera za ziphunzitso ndi zikhulupiriro.
Kuti ndi mtima umodzi ndi mawu amodzi mukalemekeze Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu.
Izi sizitanthauza kumangobvomerezana pa mfundo zirizonse zazing’ono; zitanthauza kukhala ‘amodzi’ mwa
Yesu ngakhale pakhale kusiyanako. Milomo yathu iyankhule mosasintha pa zinthu zazikulu zosayenera
kusinthidwa zofunikira. Timalemekeza ndi kutumikira Ambuye mmodzi yemweyo.
Choncho mulandirane wina ndi mnzake, monganso momwe Khristu analandira inu. Kodi Khristu
anakulandirani inu pokha pamene munaona ndi kubvomereza za choonadi chake chonse? Ngati kudali tero,
bwenzi pakali pano mu kudikirabe kuti mulandiridwe. Ayi iye anatifera ife pamene tinali ochimwabe ndipo
anatilandira ife ku thupi lake pamene tinali tiri makanda pa momwe tinali kumvetsera malemba ndi
kudzipereka kwathu. Ngati anatilandira mwa chisomo pamene tinali ochimwa kopambana, ifenso tiyenera
kulandira abale ndi alongo athu omwe ali osachita mwangwiro.
Ndi cholinga chofuna kuti Mulungu atamandidwe. Pamene Akhristu achitana mwa chisomo, Mulungu
adzatamandidwa chifukwa cha magwero a chisomocho pamene dziko liona momwe Akhristu akondanirana
ngakhale pamakhala kupunthwa ndi kulephera, dziko lidzadziwa kuti pali china chake choona ndi chamtengo
wapatali chomwe chikuchitika mumpingo. Pali munthu wina yemwe anadzacheza pa msonkhano wampingo la
Mulungu anati, “Ine ndi kuona ndinso kumva mumtima mwanga kuti kuno kuli mtendere ndi chikondi.”
15:8-13: Khristu wakhala kapolo wa Ayuda – Anabwera monga Myuda natumikira pakati pa Ayuda – m’malo
mwa choonadi cha Mulungu = kuti abweretse uthenga wa chipulumutso ku dziko lonse ndi kutionetsa ife Atate
– kukwaniritsa malonjezano operekedwa kwa makolo oyamba a m’Chipangano chakale kuti mafuko onse
adziko lapansi adzadalitsidwa kudzera mwa obadwa wochokera mwa iwo – Genesis 12:1-3 – kuti amitundu
akalemekeze Mulungu chifukwa cha chifundo chake.
Asanabwere Khristu, Israyeli yekha ndiye anali ndi phangano ndi Mulungu. Amitundu analibe gawo opanda
chiyembekezo – Aefeso 2:11,12. Koma Khristu anafera anthu onse natumiza uthenga wake kwa amitundu ndi
Ayuda omwe. Paulo anagwiritsa ntchito malemba anayi a m’Chipangano Chakale omwe anali kulosera za
chifundo cha Mulungu chomwe analandira nacho amitundu.
Kunakhala kobvuta kwambiri kubweretsa ndi kusunga umodzi pamene mpingo wapangidwa ndi anthu
ochokera ku zikhulupiriro ziwiri zosiyana za miyambo ya makolo, zipembedzo, chikhalidwe, mitundu kapena
kapezedwe kachuma. Nkhani zambiri zazing’ono mumpingo woyamba uja zinalimonso, ndipo izi zinali
chomwecho chifukwa kusiyana kwa zikhulupiriro ndi ziphunzitso kuja kumawatengera ku Mafunso
ochokeranso ku zikhulupiriro zosiyana. Izi zimaoneka kwambiri makamaka pakati pa Ayuda ndi amitundu
omwe anayamba kukhulupirira aja, monga afotokozera mu Aroma 14. Pa kuphunzitsa kwake, Paulo analimbika
kufotokoza cholinga cha Mulungu pa Ayuda ndi amitundu kuti akhale ogwirizana napanga munthu mmodzi
watsopano mwa Khristu. Anthu okhulupirika akukumanabe ndi mabvuto mumpingo amenewa lero, mabvuto
Umodzi 52
amenewa olephera kuona zinthu mofanana chifukwa chakusiyana m’chikhalidwe, miyambo, zaka, maphunziro,
ndi zina zambiri.
Pali chinthu chimodzi chomwenso tiyenera kuchiona: Paulo akutitsimikizira ndi chiphunzitso choti pa mbale
ndi mbale, tiyenera tidzikhala okonzeka kusiya zathu zina monga nyama pa nthawi yomwe tikuona kuti
tingapunthwitse mbale wina yemwe ali womangidwa ndi chikumbumtima chake. Nthawi zambirinso takhala tikuganiza kuti tiyenera kusiya mchitidwe kapena njira ya kapembezedwe mumpingo kapena ntchito ina ya
mumpingo yomwe ikhumudwitsa mtima wa mbale aliyense mumpingo kuti mwina tingapangitse kuti wina
achimwe.
Izi zimachitika chifukwa cha chikondi cha kwa anthu chilakolako choonadi chofuna kupewa kulakwirana
kapena kupatukana. Chikondi chidzayesetsa kupewa kukhumudwitsa monga momwe chingathere. Komatu
tiyenera kusamalira kwambiri pogwiritsa ntchito mfundo za Paulozi pa nkhani za pa mpingo; sizikhala
zosabvuta monga momwe zikhalira pakati pa aliyense payekha, m'modzimodzi.
Mwa chitsanzo, ngati mpingo ukuganizira za ntchito yofalitsa uthenga ndi kutembenuza mizimu 50, ndipo
pafupifupi mpingo wonse ukukhulupirira kuti ntchitoyo ikugwirizana ndi malemba ndipo ndi yokhoza, kodi
mpingo usiye kugwira ntchitoyi chifukwa m’[bale mmodzi kapena akukhulupirira kuti ntchitoyi ikulakwira
mawu a Mulungu? Kodi nkwabwino kupunthwitsa osakhulupirira 50 (kuwalepheretsa kulandira ndi
kukhulupirira uthenga wabwino) ndi cholinga chofuna kupewa kukhumudwitsa mmodzi kapena awiri
mumpingo? Kodi ndi chifuniro cha Mulungu kuti chikumbumtima chofunikira cha abale ofooka
m’chikhulupiriro chidzingololedwa kulamulira njira zomwe mpingo udzigwirira ntchito zake? Kodi kusiya
ntchito yofunikira kwambiri mumpingo kukhala kosabvuta monga momwe zikhalira ndi kusiya kudya nyama?
Ngati mu Aroma 14 timaphunzira kuti mbale wolimba asachite china chirichonse chomwe chingapunthwitse
mbale wofooka, kodi pameneponso sakuphunzitsa mwa chimvekere kuti mbale wofookayo
asaweruze/asadzudzule iwo omwe chikumbumtima chawo chiwapatsa ufulu? Kodi kupembeza pa mpingo
kutanthauza kuti tibvomereze zonse zomwe mpingowo umachita? Kodi Aroma 14 sitiphunzira kuti tingathe
kugwira ntchito ndi mpingo, koma pewani kuchita nokha chirichonse chomwe chikumbumtima chanu
chikutsutsani, ndipo siyirani kuweruza pa zinthu zina kwa Mulungu?
Nkhani zina zazing’ono zimakhudza zochitika pa kupemphera mwangwirizano. Chikumbumtima cha wina
sichimlola kukhala nawo pa chipembedzo chosonkhana m'nyumba imodzi monga zikhalira masiku ano.
Pamenepa munthuyu angathe kuchoka pa mpingo umodzi ndi kukayamba kusonkhana kumpingo wina komwe
mapembezedwe ali obvomerezedwa ndi chikumbumtima chake. Komabe ngakhale ziri chomwechi, mipingo
iwiri ija itha kutsatira moyo wololerana wa mu Aroma 14 pakati pawo, kugwirizana mu zinthu zomwe afanana
m’maganizo ndi kusiyira zina zonsezo kwa Mulungu kuti aweruze. Mipingo isatayenso Chiyanjano chawo chifukwa cha nkhani zazing’ono zoti angasankhe kukambirana kapena kungosiyira Mulungu kuti aweruze
koposa Mkhristu payekha payekha/m'modzimodzi.
Mafunso Othandiza Pokambirana:
1. Kodi malemba amaphunzitsa zotani pakulimbana kosatha chifukwa cha nkhani zazing’ono za
chipembedzo? 2 Timoteo 2:14; Tito 3:9-12.
2. Tchulani zina za zitsanzo za masiku ano za “nkhani zazing’ono” zokhudza khalidwe la Mkhristu? Ntchito
ya mpingo ndi mapembedzedwe?
3. Kodi tidzalolera motani ngati wina apempha kumasonkhana nafe komanso nafuna kulemekeza Sabata
(Loweruka) pa iye yekha, kwinaku namasunga ndi kulemekeza tsiku la Ambuye Lamulungu, monganso
kunalili ndi Aroma aja?
4. Taganizirani mfundo, nkhani kapena chinthu china chirichonse chomwe abale anu a Chikhristu
amakhulupirira kuti ndi chobvomerezeka koma inu mumachikaikira?
5. Taganiziraninso china chirichonse chomwe mukhulupirira koma ena a Akhristu anzanu amakhulupirira kuti
ndi cholakwika?
Umodzi 53
6. Kodi ndi chifukwa chiyani nthawi zambiri kumakhala kobvuta kwa basi kwa munthu yemwe amaumirira
zimene anazidziwa zokhazo, wokhala womangiririka pa chikumbumtima chake kuona nkhani yaing’ono
yoti mutha kukambirana ndi kusankha maganizo amodzi, ngati yoyenera kutero?
7. Nanga ndi zinthu ziti zomwe mumaziika pa mndandanda wanu wa zenizeni zomwe mumakhulupirira pa
Chikhristu chanu, zomwe kaya zitani simungalole kuzisintha mokambirana? Kodi ndi ziphunzitso ndi zikhulupiriro ziti zomwe tiyenera kugwirizana nazo pasanakhale umodzi? Kodi kapena nkhani yake ndi
yomwe iri pa Aefeso 4:4-6.
8. Kodi nthawi zina timatenga nkhani zazing’ono kukhala zofunikira koposa “Chiyero,” mtendere, ndi
chimwemwe mwa Mzimu Woyera?” Nanga tingapewe bwanji moyo umenewu?
9. Nanga tingachite chiyani kuti zitheke kumvera chiphunzitso cha Paulo chakulolerana mu Aroma 14 ndipo
panthawi yomweyo kusamalira ndi kusunga mzimu womvera malangizo onse a Mulungu aang’ono ndi
aakulu omwe? Kodi kungatheke kukhala wosalolera kusiya zomwe ukhulupirira iwe mwa wekha ndi
kukhala wololera za ena panthawi imodzi?
10. Ndi chiyani chomwe munayamba mwa chisiyapo m’nthawi ina yake pofuna kupewa kulakwira maganizo a
wina?
11. Kodi zimatheka kukhala kumbali yolondola “pankhani yomwe pali maganizo awiri” komabe ndi kukhala
woweruzidwa ndi Mulungu chifukwa akuonetsa kugawanitsa malinga ndi njira yomwe akutengera
nkhaniyo?
12. Nchifukwa chiyani umodzi uli wofunika? Yohane 17:20,21; 13:35.
MBALI ZOBVUTA POTANTHAUZIRA MALEMBA
Mawu oyamba: Matanthauzidwe a gulu lija lakubwezeretsa:
1) Ponena za chikhulupiriro ndi machitidwe athu onse, malembo ndiwo atitsogolera ndi kutilamulira.
2) Baibulo limalamulira popereka lamulo pomwepo, chitsanzo chobvomerezeka ndi maganizo
oyenera.
3) Pamene Baibulo linena, ifenso timanena ndipo pamene Baibulo likhala chete ifenso tikhala chete.
Ndi kukhulupirira kuti maganizo onsewa ndi omveka ndi obvomerezeka ndiponso kuti tonse tingathe
kugwirizana nawo. Komatu Sali osabvuta kuwagwiritsa ntchito m’machitidwe athu. Tamvani ndemanga ya
katwiri wina wotchedwa Dr. Bill Humble:
Nkosabvuta kungonena mfundo ya gulu lobwezeretsa lija yoti – mpingo uliwonse mumbadwo
uliwonse ukhale pafupifupi wofanana ndi mpingo wa m’Chipangano Chatsopano. Ndi chinthu
chobvuta kuti tizindikire ndi kuganizira zomwe Chipangano Chatsopano chifuna mu nthawi iri
yonse pa yokha. Mpingo uyenera kumafunsa, kodi ndi ziti zomwe ziri zoyenereka kutsatidwa
malinga ndi dongosolo la Chipangano Chatsopano? Nanga ndi ziti zomwe tingazichotse popeza
zinangokhala monga gawo la chikhalidwe ndi miyambo ya nthawi zakale ndipo kuti ndi
zosamangiririka ku mpingo mu m’badwo uliwonse? Iri ndi bvuto lokhudzana ndi
katanthauziridwe ka Baibulo ….. bvuto la njira ya kamasuliridwe ka malemba ndipo mayankho
ake sakhala okhweka nthawi zonse.
Ntchito yobwezeretsa inagawanikana chifukwa chabvuto lakamasuliridwe kamalembo. Phunziroli likhala
likuunika Madera a ena a mabvuto amenewa.
1. Kodi kukhala chete kwa malemba kumatiletsa kapena kumatiloleza?
A. Mu nthawi zakusintha ndi kukonzanso zinthu zija Martin Luther anakhulupirira kuti chirichonse
Umodzi 54
chomwe sichinaletsedwa mwatchutchutchu m’malemba chiri chololedwa, pamene Ulrich Zwingli
anakhulupirira kuti chirichonse chomwe sichilamulidwa mwatchutchutchu nchosaloledwa. Munthawi
yakubwezeretsa, Barton W. Stone anabvomera kunyema ndikumwa pa mgonero pamodzi ndi
osabatizidwa mobizidwa chifukwa sanapeza lemba lenileni loletsa zimenezi. Koma Alexander
Campbell anatsutsa zimenezi, ponena kuti panalibe lemba lolamulira machitidwe amenewa Palinso
kusiyana kwa maganizo ngati komweku pokhudza za kugwiritsa ntchito zida poyimba nyimbo.
B. Zitsanzo za zochita zina zomwe gulu limodzi kapena gawo lina la anthu obwezeretsa aja anatsutsa
chifukwa sanazipeza m’malemba: amasiye Akhristu, makoleji Achikhristu, mgwirizano wodzera mu
mpingo umodzi wothandizira, mabungwe a amishinale, zikho zambiri pa mgonero wa Ambuye,
thumba la chuma cha mpingo, nyumba za mpingo, mabuku a nyimbo, mgonero wa madzulo
(wachiwiri) alembi ampingo, alaliki oyang’anira za achinyamata, alaliki a uthenga wabwino,
misonkhano ya achinyamata, anthu oyendetsa ntchito, makalasi ochitidwa m’nthawi zofanana, malaudi
sipikala, mabukhu ophunzitsira Baibulo, maholo achitira mafeloshipi, ndi zina zotero.
C. Ambiri akhulupirira kuti pamene Mulungu afotokoza mwapadera njira yochitira chinthu china, ichi
chitanthauza kuti pasachitikenso njira za mtundu winanso osakhala umenewu.
Zitsanzo:
1) Ubatizo wobiza sulola wina monga wotsira madzi pamutu, kapena kungowaza.
2) Mnjale, mtengo womwe anapangira chombo cha Nowa osati mkungudza kapena mitengo ina –
Genesis 6.
3) Moto woyera wokha pa guwa, osati miyoyo ina wamba – Levitiko 10.
4) Mkate ndi chipatso cha mpesas pa mgonero wa Ambuye osati chakudya china chirichonse kapena
chakumwa.
5) Akulu pa mpingo uliwonse osati utsogoleri wamtundu wosiyana ndi umenewu.
6) Mapembedzedwe a padera a m’Chipangano Chatsopano osatinso monga ena ali onsewo.
Ngati kukhale chete kwa malemba sikutiletsa, ndiye kuti machitidwe ena onse achilendo
adzakhalanso obvomerezedwa. Komanso palibe yemwe akhulupirira kuti machitidwe onse omwe
sitilamulidwa mwapadera kuchita ndi oletsedwa. Ambiri a ife timagwiritsa ntchito timakapu ting’onoting’ono tayekha tayekha pa mgonero ngakhale Khristu anagwiritsa ntchito chikho chimodzi.
Ambiri timakhulupirira kuti zothandizira zina kuti lamulo lina likwaniritsidwe ngakhale sizinachite
kutchulidwa kapena kufotokozedwa m’malemba, zimalamulidwa ndi chilamulo chongoganizira, koma
pokhapokhapo ngati chachita kuletsedwa mwapadera penapake.
Komanso, palibe yemwe amakhulupirira kuti machitidwe alionse omwe sanaletsedwe mwa dongosolo
ndi ololedwa. Mipingo yomwe imangwiritsa ntchito zida mu nyimbo zawo imatsutsa ponena kuti zidazi
zimaloledwa m’Chipembedzo chifukwa siziletsedwa mwapadera; koma amakana ubatizo wowaza
madzi pamutu ngakhale siziletsedwa mwapadera.
D. Dr. J.D. Thomas anapereka maganizo oti, “kukhala chete pamene malemba akhale chete” si mfundo
yaikulu ayi, koma amagwiritsidwa ntchito m’malo okhawo omwe malemba afuna kuti machitidwe
kapena m'chitidwewo usachitike. Naye Clinton Lockhart analemba kuti, “kutsimikizira pa choonadi
kumachotsadi chomwe chikutsutsana nacho basi.
2 Kodi ndi zitsanzo ziti zomwe zatimanga lero?
A. Pamene tiona atumwi kapena mpingo woyamba uja ukuchita kanthu, mwina uwu ungakhale umboni
wa atumwiwo pa lamulo lomwe iwo analamulidwa nalo ngakhale kuti lamulolo silifotokozedwa bwino
kwa ife m’malemba. Chitsanzo:
Umodzi 55
1) Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu – Machitidwe 5:28,29.
2) Woyang’anira wa ndende yaku Filipi anatembenuka nthawi yomweyo – Machitidwe 16:33.
3) Paulo anamtumiza Onesimo, kapolo wathawa uja Filimoni mbuye wake.
4) Ambuye anawaonjezera tsiku ndi tsiku iwo omwe anali kupulumutsidwa – Machitidwe 2:47.
5) Paulo anakhala “chili chonse kwa anthu onsewo”, ndi cholinga chofuna kuti afalitse bwino
uthenga – 1 Akorinto 9:19-22.
6) Antchito ampingo anali kudzodzedwa “powaika manja” – Machitidwe 6:1-6.
7) Ophunzira oyamba anali kutchedwa Akhristu – Machitidwe 11:26.
8) Anthu omwe ubatizo wawo woyamba sanali watanthauzo anabatizidwanso – Machitidwe 19:1-6.
B. Koma ndi anthu ochepa omwe amakhulupirira kuti chitsanzo chirichonse mumpingo woyamba
chipereka lamulo lomwe tiyenera kulitsata m’masiku ano.
1) Alaliki ankapita awiriawiri – Luka 10:1-4.
2) Paulo anafotokozera chiphunzitso ndi ndakatulo ya osapembedza – Machitidwe 17:28.
3) Paulo analalika mu kachisi wa Ayuda – Machitidwe 13; 14:1; 17:1,2.
4) Analalika miyezi itatu m'kachisi mmodzi – Machitidwe 19:8.
5) Anali kuphunzitsa tsiku ndi tsiku pa “sukulu ya ku Turano” – Machitidwe 19:9,10.
6) Anasonkhana pa mgonero wa Ambuye usiku m’chipinda chapamwamba – Luka 22:7-20;
Machitidwe 20:7,8.
7) Paulo analalika mpaka usiku ndi kupitiriraponso – Machitidwe 20:7,11.
8) Mgonero wa Ambuye unachitika pogwiritsa ntchito chikho chimodzi – Mateyu 26:27.
9) Mpingo wa ku Yerusalemu unasankha atumiki 7 kuti athandize pa chakudya – Machitidwe 6:1-6.
10) Nthawi zambiri Paulo ankayenda pa ngalawa pokalalika.
C. Kuganizira chitsanzo chomwe chiri chomangirira inali ntchito yaikulu m’nthawi yobwezeretsa.
Zitsanzo:
1) Iwo omwe anatsutsa anaunikira pempho la alaliki ku chitsanzo cha Paulo chosalalikira kumalo
komwe Khristu akudziwidwa kale – Aroma 15:20.
2) Omwe amatsutsa kugwirira ntchito kwa mipingo pamodzi amati mumpingo woyamba uja,
chithandizo chimachokera kuchokera ku mpingo umodzi kupita ku winawo pa nthawi zamabvuto
zokha ndiponso kuchokera ku mpingo wopeza bwino kupita kumpingo wosauka.
3) Gawo lina la zitsanzo zomwe chithandizo chinali kupita kwa a mishonale osadzera ku mpingo
womwe unali kumthandiza – Afilipi 4:15,16; 2 Akorinto 11:8.
4) Omwe amatsutsa za Sunday sukulu amati chitsanzo chomwe timaona cha maphunziro a gulu ndi
chokhacho chomwe timaona mpingo wonse uli pamodzi, ndipo amati chimenechi ndicho
chimaletsa malasi otsatana – Machitidwe 11:26; 1 Akorinto 14:23.
Umodzi 56
5) Dr. J.D. Thomas amapereka maganizo oti “pokhapokhapo ngati pali chisonyezo choonadi ndi
chomveka bwino choti machitidwewa anali oyenera kuchitidwa, [ndi Akhristu oyamba, ndi
ulamuliro wa atumwi]. Ifenso tidzachita koma mwa ufulu wosankha m’masiku ano. (mawu ali
m'mikutirowo ndi anga).
3 Ndi maganizo ati omwe ndi ofunikira?
A. Malembo ndi malamulo ena amphamvu opezeka, ngakhale sanafotokozeredwe mwatchutchutchu,
akhoza kungoganiziridwa mwa chilungamo kuchokera ku zonenedwa ndi mfundo zina. Zitsanzo:
1) Kaini ndi Abele anauzidwa mtundu wansembe yomwe Mulungu anafuna, - Genesis 4:3-5; Ahebri
11:4.
2) “Kulalikira Yesu” kunaphatikizana ndi kulalikira ubatizo – Machitidwe 8:36-39.
3) Ubatizo siwamakanda ayi – Marko 16:16, Machitidwe 2:38.
4) Kusiyana pakati pa mwamuna ndi mkazi chifukwa cha chigololo kumaloledwa kwa mwamuna
ngakhalenso mkazi – Mateyu 19:9; Marko 10:11,12.
5) Mpingo uliwonse wa pamalo udzikhala woima paokha monganso iriri mipingo ina yonse –
Machitidwe 14:23; Tito 1:5.
6) Kulibenso Atumwi padziko lapansi masiku ano – Machitidwe 1:21,22.
7) Munthu wathupi la uchimo sikuti ndiwongotaikiratu – Luka 8:15.
8) Oyang’anira ayenera ayambe ayesedwa ndi kubvomerezedwa asanaikidwe manja – 1 Timoteo
3:10.
9) Anthu ofuna ntchito ya oyang’anira ayenera asankhidwe ndi mpingo – Machitidwe 6:1-6.
B. Komabe pali kusiyana pakati pa ganizo lofunikira, ndi losatsimikizika kapena looneka ngati ndi loona.
1) Poti Ayuda patsiku la Pentekoste (Machitidwe 2) anauzidwa kuti alape nabatizidwe, ndi ganizo
lofunika kuti anthu amenewa anali achikulire kuti anatha kukhulupirira ndi kubatizidwa.
2) Likuoneka ngati ganizo loona koma losatsimikizika loti popeza anthu analipo zikwi zitatu ndiye
kuti mmaiwe ndi m'malo osamba anthu mu mzinda wa Yerusalemu.
3) Likuoneka kuti ndi ganizo loona ndipo lingatheke loti atumwi onse anagwira ntchito yobatiza
anthu zikwi zitatu aja mothandizana.
C. Nthawi zambiri pakhala pali bvuto pofuna kumvana ngati ganizo la anthu pa mfundo ina ndi lofunika
kapena losatsimikizika kapena ndi lotheka. Zitsanzo:
1) Mpingo wa ku Trowa unasonkhana pa tsiku loyamba la Sabata kunyema mkate – Machitidwe
20:7. Atsogoleri antchito yobwezeretsa anali naonso maganizo amenewa oti mipingo yonse,
kulikonse m’Chipangano Chatsopano amanyema lamulungu lirilonse. Komabe ena amafunsa
ngati limeneli liri ganizo lofunikira potengera pa ndime yake yokhayi.
2) Ganizo linanso likutengedwa mu 1 Timoteo 3:2, loti mwamuna mmodzi sangakhale mkulu
pamalo. Koma enanso amatsutsa zimenezi.
Umodzi 57
3) Mkate womwe unkagwiritsidwa ntchito pa Pasika unali wopanda chotupitsira. Yesu
anagwiritsa ntchito mkate wapa Pasika pamene anali kuyambitsa mgonero wa Ambuye. Pakhala ganizo loti mkate wa pamgonero wa Ambuye ueyenera udzikhala wopanda
chotupitsa.
D. Tomasi Campbell, m’chikalata cha dongosolo lake analemba:
Ngakhale zoganizira chabe ndi zochotsedwa ku malemba, ngati zaganiziridwa
mwabwinoko, zingathe kumatchulidwa kuti ziphunzitso za mau opatulika a Mulungu,
koma kodi sizikumangiriridwa mmaganizo a Akhristu kopitirira. Komwe akanayenera
kuunika ndi kulumikiza bwino mgwirizano wake, ndipo mwaumboni natsimikizira kuti
ziri chonchodi; popeza chikhulupiriro chawo chisasamire pa nzeru za anthu, koma mu
mphamvu ndi ulamuliro wa Mulungu. Choncho palibe kuchotsa zinthu kwa mtundu
umenewu kungatengedwe monga choyanjanitsa, koma zimakhala ku zotsatira ndi
kumangirika kwa mpingo.
Iye analankhula zimenezi chifukwa anaona kuti panali kutsamiranso pa maganizo a munthu
potenga maganizo a choonadi cha m’malemba.
4. Kusiyanitsa pakati pa zofunikiradi ndi zongochitika.
Ngakhale chitsanzo cha mpingo woyamba uja chingakhale molingana ndi malamulo a atumwi aja, zichitika zawo zina zitha kungokhala monga zochitika chabe zomwe ziribe gawo lirilonse
ndi chifuniro cha Mulungu mu mpingo wake. Mwachitsanzo, cholinga, kutanthauza ndi magawo ena a mgonero wa Ambuye monga tionera mmalemba akuonetsa chifuniro cha
Mulungu kwa ife lero, koma malo kapena nthawi yochitira mgonerowo (m’chipinda chapamwamba usiku) ndi zinthu zoti zinangochitika basi.
5. Kusiyanitsa zochitika mdziko lathu kapena dera lathu, zokhala kanthawi kochepa ndinso
zachikhalidwe, ndi ziphunzitso zapadziko lonse ndi magwiritsidwe ntchito achikhalire.
A. Malamulo ngakhale zitsanzo zina zinaoneka ngati tanthauzo lake ndi cholinga chake kwa
kanthawi kochepa ndi malo ake. Zitsanzo:
1) Akazi kubveka mitu yawo popemphera – 1 Akorinto 11.
2) Kupsopsonana kopatulika – 1 Akorinto 16:20
3) Kusamba mmapazi – Yohane 13; 1 Timoteo 5:10.
4) Kupewa banja chifukwa cha masutso alinkudza – 1 Akorinto 7:25-31.
Izi siziri zotimanga ife lero ponena zoona, ngakhale kuti malamulowo akutero. Ena
samasiyanitsa ndipo akadagwiritsidwabe ntchito malamulowa lero.
B. Anthu a mgulu lobwezeretsa lija ndinso ena omwe sanali mgululi anatsutsa kuti mfundo ya m’Chipangano Chatsopano yoletsa akazi kutsogolera mmisonkhano yachipembedzo ndi
ntchito za mpingo linali monga mwambo ndi chikhalidwe komanso malinga ndi nthawiyo,
osati ndiyogwira ntchito padziko lonse mpaka kale ayi. Koma Paulo watengera malamulo ake
pa chilengedwe ndi kuchimwqa kwa munthu – 1 Akorinto 14:34-35; 1 Timoteo2:11-15.
C. Payenera kukhala kuganizira mozama bwino kuti tithe kusiyanitsa zofunikira kwambiri, ndi
Umodzi 58
zongochitika chabe ndi zachikhalidwe, komanso ndi zogwira ntchito konsekonse.
6. Kusiyanitsa zoyambirira ndi zopitirira nazo pa chifuniro cha Mulungu.
Malamulo ndi zitsanzo zina zimakhazikika ndi kukhuza kwambiri ku nthawi zoyambirira ndi
zokhazikitsa mpingo, osati ku nthawi zonse. Zitsanzo: “Zizindikiro za mtumwi” – 2 Akorinto 12:12; udindo wa atumwi; Bungwe la ku Yerusalemu – Machitidwe 15.
7. Kusiyanitsa mawu okuluwika ndi oona.
A. Baibulo liri ndi mau ena omwe analembedwa kuti amveke monga momwe aliri mosabvuta
ndipo ena akamveke mokuluwika. Timasokoneza zomwe Baibulo litanthauza pamene titenga
mau olembedwa moona ngati mkuluwiko ndi olembedwa monga mkuluwiko ngati oona.
B. Mafunso ena okhudza chipembedzo omwe amafunsidwa pa nkhani imeneyi ndi aja a za
ulamuliro wa zaka chikwi (mileniamu) wa Khristu (Chibvumbulutso 20) ndinso zogwiritsa
ntchito zikho zambiri pamgonero wa Ambuye.
C. Maganizo othandiza kuti tizindikire mau okuluwika (olembedwa ndi J.R. Duncan):
1) Momwe nkhaniyo ikumvekera.
2) Ngati zonenedwazo zinena zachinthu choti sichingatheke mwachilengedwe.
3) Ngati tanthauzo lenileni la nkhaniyo litsutsana ndi malemba ena.
4) Ngati tanthauzo lake lenileni lidzafuna machitidwe omwe ali olakwika kapena oletsa
zinthu zoona.
5) Ngati tiuzidwa kuti ndi mau ophiphiritsa.
6) Ngati zotsimikizika ndi zokhazikika zilowa m’malo osatsimikizika ndi osakhazikika.
7) Ngati zinenedwa mongoseweretsa.
8) Kuona wekha momwe zinthu ziriri panthawiyo ndi nkhaniyo.
9) Malamulo amaperekedwa mmau omveka bwino.
7. Kodi zoyankhula za Yesu mnthawi za utumiki wake zikutilamula ife mumpingo lero?
A. Anthu ena amati ziphunzitso za Yesu pankhani za kulekana m’banja ndi kukwatiranso ndinso zomwe anayankhula pa chiphunzitso cha paphiri zinali za kwa mbadwo wapansi pa chilamulo
cha Mose omwe unatha panthawi yomwe Yesu anafa, ndipo sizigwiranso ntchito mumpingo lero.
B. Pamene zina za ziphunzitso za Yesu zinkagwirizana ndi momwe Ayuda ankamverera
chilamulo cha Mose (pita ukadzionetsere kwa ansembe; “Alembi ndi Afarisi amakhala
pampando wa Mose; choncho mverani ndikuchita zomwe akuuzani”), zambiri za ziphunztso
zakezi ndi za ufumu/mpingo ndipo ndi zokonzedwera mpingowo. Chiphunzitso cha paphiri
chinena za chiyero cha ufumu – Mateyu 5:20ff. Pankhani ya banja kulekana ndi kukwatiranso,
Yesu akusiyanitsa chiphunzitso chake ndi cha Mose – Mateyu 19:3-9.
Umodzi 59
Mitu yofunika potsiriza:
1. Ambiri akufufuza matanthauzo ena atsopano pakati pa mipingo yonse yomwe iri mgawo
lobwezeretsa lija. Iwo amadzudzula kusagwiritsa bwino ntchito ndinso kusiyana maganizo mugululi pamomwe anamvera ndikutanthauzira machitidwe akale aja (malamulo, zitsanzo,
kuganizira kofunika). “Mamasuliridwe amasiku ano” amafunika kuti ife tisiye kufufuza za zoonadi za nkhaniyo kuchokera kunkhani yomwe siikhudza nkhaniyo ndipo tiganizire
mosamala zankhaniyo, mbiri ya nkhaniyo yalembedwera. Alangizi abwino ndinso omasulira
malemba okhwima akhala akulimbikitsa zimenezi. Mamasuliridwe atsopano amakana zitsanzo
ndi zoganizira kuti zisakhale zamphamvu yolamulira ndipo amangobvomereza malamulo
okhawo olembedwa mosakuluwika ndi mwwachindunji. Izi zakhala chomwechi chifukwa cha
mabvuto omwe takomana nawo pofuna kuzindikira kuti kodi ndi zitsanzo ziti kapena
zoganizira ziti zomwe ziri zomangirira. Koma mabvuto onsewa akatha, anthu adzakhalabe
akuyang’ana pa zotsanzo ndi zoganizira kuti apeze muuni wowaunikira kuti mpingo
ukhulupirire ndi kuchita ziti.
2. Zolimbana zathu zambiri za momwe tingagwirire ntchito ya mpingo zimabwera chifukwa
chokakamira dongosolo kapena machitidwe, zomwe zotsatira zake zimayamba kulamulidwa
ndi moyo wopendekera ku chilamulo. Mpingo woyamba womwe unachita potsatira utsogoleri
ndi malangizo a atumwi sunayenere kukhala chitsanzo chathu, koma timaona dongosolo la kachitidwe mmalo monse momwe Mulungu analibe nawo dongosololo. Timachita izi
chifukwa cha khalidwe lathu lomwelija lopendekera pa malamulo lofuna kukhala odziwitsitsa. Pamene tisiya moyo ndi khalidwe lopendekera ku malamulo ndikuyamba kumvera pansi pa
chisomo, pamenepo tidzatha kulemekeza chitsanzo cha m’Chipangano Chatsopano popanda kupitirira ndi kumasulira moonjezera.
3. Malembo amazindikira zambiri zomwe ndi mfundo zazing’ono zomwe zimatchedwa “mfundo,
kapena nkhani zazing’ono zoti titha kusiyana pa momwe tiziganizira” – Aroma 14,15 – nkhani
zomwe mpata umakhalapo anthu atha mwachilungamo, ndimokhulupirika kulolerana kusiyana
maganizo pakumasulira kwake. Tiyenera kulemekeza chikumbumtima chathu pazomwe ife eni
tichita, koma Baibulo litiphunzitsa kuti tingathe ndipo tiyenera kugwira ntchito pamodzi ndi
iwo omwe maganizo awo ndi athu asiyana kwambiri pa zinthu zina zazing’ono. Koma pali
mfundo za choonadi zina zazikulu za uthenga wabwino zomwe tiyenera kugwirizana kuti
tikhale amodzi (onani ndikuwerenga Aefeso 4:1-6). Mfundo zazikulu zachoonadi zimenezi
zalembedwa momveka bwino m’Baibulo. Choncho pamene tiri ofunikira kulimbikirabe
ntchito yofufuza zomwe Mulungu atilamulira m’malemba, sikuti tidzipeza mayankho onse
kapena kugwirizana pa mfundo zofunikira zazikulu kuti tithe kugwira ntchito pamodzi.
--B. Shelburne
South Texas Leader’ Meeting
September 30, 1989
Kusiyanitsa Malemba ndi Miyambo M’chipembedzo.
Mawu oyamba: Werengani Marko 7:1-13. Ayuda anadzipangira miyambo yaumunthu yambiri naipanga kukhala yamphamvu ndi ulamuliro kotero kuti anaika pambali chilamulo cha Mulungu
chifukwa cha miyambo yaoyo. Kodi nafenso tingachite zimenezi? Mipatuko yambiri mntchito yobwezeretsa ija inabweramo chifukwa cholemekeza kwambiri miyambo ndi kuitenga ngati yofunika
kwambiri kuposa malemba.
Malemba ndi mau a Mulungu. Sitingathe kumasula chomwe iwo amanga mwaqchimvekere. Miyambo
ndi mau a munthu. Imapangidwa ndi nzeru za munthu ndi zikhalidwe za makolo zosiyirana. Tiri ndi
ufulu wosintha miyambo ndi zizolowezizi.
Umodzi 60
1. Kodi miyambo imayamba bwanji? Nanga imachokera kuti? Inayamba kudzera m’njira ziwiri:
A Pamene Mulungu wapereka lamulo lomwe sanafotokoze bwino momwe lamulolo
B ligwirira ntchito, iye watisiyira mwai woti tisankhe njira yabwino yogwirizana ndi nthawi
yathu komanso momwe zinthu ziriri panthawiyo.
1) Izi ziyenera kutero popeza uthenga waperekedwa ku mitundu yosiyanasiyana mzaka
mazana-mazana.
a) Ife timagwiritsa ntchito njira zosiyana siyana zofalitsira uthenga mosiyana ndi
mpingo woyamba uja.
b) Timasonkhana mmalo osiyanasiyana ko
c) Machitidwe ena a kapembedzedwe kathu ndi osiyana kwambiri ndi ampingo
woyamba uja.
2) Pamene malembo safotokozera bwinobwino njira ya machitidwe ake, ife timayang’ana
pa zofunikira za munthawi zathu zino ndi malo athu ndinso poganizira zomwe zingachitikedi kuchokera mmalemba, ndipo kenako timasankha njira yoyenera ndi
yabwino. Zizolowezi ndi zikhalidwe zimenezi, kaya njira zimenezi zoyambika kalezi, ndizo zimapanga miyambo.
3) Miyambo imatha kuyambanso posonkhanitsa nzeru zochokera kwa atsogoleri athu
omwe timawalemekeza ndinso anzeru ena amakedzana.
4) Sinkhani zonse zopezeka mmalemba zimamveka bwino. Mu zomwe sizimveka
bwinozo, mwai ulipo wololera mokhulupirika kusiyana kwa maganizo ndi
kutanthauzira. Kutanthauzira kwa mfundozi ndikosiyirana kuchokera ku mbadwo
umodzi kupita ku mbadwo winawo, ndipo sitimaphunziranso nkhanzo kwa ife tokha.
5) Malembo satchula pachokha mwachimodzichimodzi cha zonse zomwe tikumana nazo
munthawi zathu zalero (monga mankhwala ozunguza bongo). Tiyenera kumaona zoona
zenizeni za malemba pa zinthu zimenezi ndikuzigwiritsa ntchito pa zochitika ndi
zobvuta moyo wathu wa masiku amakono. Aphunzitsi athu ndi atsogoleri athu
amagwiritsa ntchito njira imeneyi poweruza zina ndi zina ndipo nafenso timasiyira ena.
Zonse zosonkhanitsidwa kuchokera ku maweruzo akalewo zimakhala miyambo yathu
kapena zizolowezi zathu ndi ziphunzitso zathu mumpingo. (kumbukirani, kuti
sitikunena za zinthu zolembedwa momveka bwino m’Baibulo, koma za maganizo athupi la munthu lopanda ungwiro.)
6) Izi zingathandize kupeza chifukwa chomwe gulu lathu lagawanika.
a. Chipangano Chatsopano chinalibe cholinga choti chikhale monga bukhu
la dongosolo la malamulo monga chinali Chipangano Chakale (ngakhale tiyenera kulemekeza malamulo omwe chitipatsa)
b. Kwakukulu Chipangano Chatsopano chiri ndi mfundo zazikulu za
choonadi zomwe zingagwiritsidwe ntchito pa bvuto liri lonse mu
chikhalidwe chiri chonse. Ndipo Mulungu ayembekezera kuti ife tikule
monga Khristu mu umunthu wathu kuti tithe mwaumunthu wathu
kuchita zinthu
Umodzi 61
zobvomerezeka – Yeremiya 31:33; Aroma 13:10.
c. Koma thupi lathu lauchimo limakonda malamulo ooneka olembedwa
mofotokozedwa bwino monga a m’Chipangano Chakale aja.
1. Kuti titsimikizire zaungwiro wathu poona momwe tichitira bwino potsatira malamulo ena.
2. Kuti tisamaganizire ndikugwiritsa ntchito malamulo.
3. Kuti tisasinthike mkatimo.
d. Choncho tayesetsa kuika “mosamveka bwinomo” m’Chipangano
Chatsopano pongoganizira, kuchotsera, kuika maganizo athu
ndikumasulira malingana ndi zomwe tikuyembekezera. Timafuna
lamulo lapa chirichonse. Dongosolo lirimo m’Chipangano Chakale
lakayendetsedwe kampingo ndi ntchito zake, koma nthawi zina tatenga
ndikugwiritsa ntchito moyo wopendekera pa dongosolo lodziwika,
ndikufuna dongosolo la malamulo ena oti m’Chipangano Chakale
mulibe ata. Ndipo kuyambira pamene maganizo ndi nzeru zina za munthu zinayamba kugwiritsidwa ntchito kuti zitseke mmipata momwe
simumamveka bwino ndikuti apeze dongosolo lakayendetsedwe ka ntchito zina, nthawi zonse sitinakhala ndi maganizo ofanana mu
mchitidwe umenewu. Choncho tangokhala ogawikana mtimagulu, kagulu kali konse ndikumaganiza kuti ndikokhako komwe kayendetsa
ntchito zampingo mogwirizana ndi dongosolo la malemba.
e. Tikanatha kupewa kugawikanaku ngati tikanazindikira kuti kutsutsana
kwathu kulipo chifukwa cha mbali ya maganizo athu ndikutanthauzira
kwa umunthu wathu, osati chifukwa cha malemba omveka bwino.
Ndiyenera kumvera chikumbumtima changa, koma ndisamangirire
chikumbumtima changacho kwa ena ngati njira yoyesera Chiyanjano
chathu. Makolo athu am’ntchito yobwezeretsa ija anati,”
mchikhulupiriro,k umodzi; mmaganizo, ufulu; mzinthu zonse,
chikondi.”
2. Ndikofunikira kudziwa ndiikumvetsa kuti mmitundu yonse ya miyambo muli maganizo ena a
umunthu.
A. Miyambo ingathe kufaniziridwa ndi mau a Mulungu, koma ndi maganizo a munthu. (Miyambo ina ingathe kukhala ndi maziko ake ochokera ku malemba kuposa ina.)
B. Nkhani zomveka bwino ndi zofunikira za mau a Mulungu sizingaikidwe pambali kapena
kukaikiridwa. Ngati sitilemekeza mphamvu ya mau a Mulungu, ndiye kuti basi, tataya zonse. Tasokonekera.
C. Koma kusiyana maganizo pa miyambo kumafuna kulolerana chifukwa ife pamodzi ndi
amphunzitsi athu tonsefe ndi anthu omwe tingathe kuchimwanso. Choncho ndikofunikira
kwambiri kumadziwa kuti kodi ndi nkhani ziti zomwe ziri zammalembo ndipo ndiziti zomwe
siziri zammalembo koma zamiyambo chabe.
D. Miyambo ndi zizolowezi za chikhalidwe ndi mamvedwe a zinthu angathe kusiyidwa pambali
ndikusinthidwa ngati akusokoneza ndikulepheretsa ntchito ya Mulungu.
Umodzi 62
(Zitsanzo: ganizo loti akazi samakhala pamodzi pophunzira Baibulo mwapadera; kugwiritsa
ntchito Baibulo
lotanthauziridwa kamodzi kokha basi; kusagwirizana ndi nyumba zopembezereramo; maganizo oti mlaliki sangalalike mmalo oposera amodzi pa nthawi imodzi; ganizo loti munthu
mmodzi ndiye adzilalika nthawi zambiri mumpingo;p ndi zina zotere.)
3. Zoona zina zomwe tiyenera kuzizindikira zokhudza kusintha mmiyambo yathu.
A. Tiri ndi miyambo monganso ena amachitira.
B. Tiyenera kumadziwa kusiyana pakati pa miyambo ndi malembo kuti tisalimbane chifukwa cha
miyambo monga momwe tingachitire chifukwa cha malemba. Akhristu ena olemekezeka
akupha mipingo yawo chifukwa chosadziwa za kusiyana kumeneku. Tidzalandira mphoto
chifukwa choima nji! Pa malemba; tidzaweruzidwa chifukwa chogawanitsa kapena kutchinga
mpingo chifukwa cha miyambo ndi zizolowezi.
C. Kawirikawiri kusintha sikukhala kwa phindu ngati kungokhala kapena kuchitika chifukwa
chongofuna kusintha basi (pokhapokha kukhale chifukwa chofuna kutidzutsa ndikutipangitsa
kuti tiganize zomwe tikuchitazo).
D. Ngati njira kapena maganizo omwe tazolowera kuchitira zinthu akulepheretsa ntchito ya
Mulungu, tiyenera kukonzekera ndikukhala ndi chidwi chofuna kusintha. Iripo mizimu yomwe ikapezeka kumwamba pokhapokha ngati titasintha magwiridwe athu antchito kuti ikhale
yamphamvu. Paulo mtumwi anali wokonzekera kusintha chirichonse chomwe sichinali chomangiririka ku mau ngati chinali choti chikapulumutse mizimu yotayika – 1 Akorinto 9:19-
23 – ndipo sakanakondwera ndi mitima yathu yosalola kusunthika koma kuumirira miyambo
ndi zizolowezi yomwe ikulepheretsa kufikira mizimu yotayika yomwe iri kunja.
E. Inde ndikobvuta kwambiri kusiyiratu mwambo wogwirira ntchito kapena kamasuliridwe,
ngakhale kuti kutero kuli kulimbana ndi mau a Mulungu kapena kulepheretsa ntchito ya
Mulungu. Komatu dziwani kuti sipakhala kukula muuzimu kapena kukula kwa mpingo ngati
palibe kusintha kwabwino.
F. Zambiri zomwe tichita mumpingo kuti tiyang’anitsitse tidzaona kuti ndi zizolowezi chabe
kaya miyambo chabe zosati zofotokozeredwa mu malemba. Zitsanzo:
Mapemphero a Lachitatu madzulo.
Misonkhano iwiri yamapemphero Lamulungu. Mapemphero a Lamulungu mmawa pa 10:30
Mgonero wa Lamulungu usiku. Pemphero lalikulu limodzi.
Nyimbo zitatu tisanapemphere kenako nyimbo litatha pemphero. Kusiya vesi yachitatu ya nyimbo.
Bukhu la nyimbo. Otsogolera nyimbo.
Madododo a nyimbo mmabuku a nyimbo.
Mayimbidwe okhala ndi magawo anayi onse a mau.
Kuimba mokoma monga momwe tidziwira.
Chikho chakechake pamgonero.
Madzi a chipatso champesa.
Kudutsitsa chifaniziro cha mgonero mmizere.
Umodzi 63
Kutenga kochepa kwambiri ka mkate ndi chikho.
Pagome. Nyumba zopemphereramo.
Maofesi a nyumba zopemphereramo. Zizindikiro za mpingo.
Dzina loti “Mpingo wa Khristu” monga dzina lokhalo lobvomerezeka ndi lopambana. Nyumba zosonkhanirana.
Mobatizira.
Malaudi sipikala.
Zida za kanema ndi kanema.
MaBaibulo olembedwa ndi alembi osiyanasiyana.
Kagawidwe ka mitu ndi ndime m’Baibulo.
Othandizira ntchito zina.
Ulaliki wotenga mphindi wakumi atatu (30 mins)
Nyimbo zoitana.
Misonkhano yofalitsa uthenga yotenga sabata yatunthu.
Munthu mmodzi yekha wolalikira nthawi zambiri.
Alaliki a achinyamata, misonkhano ya achinyamata kuperekera mbale ya chopereka.
1) Miyambo yambiri yomwe tawerengayi inayamba yakanidwapo pamene inali kungoyambidwa kumene. Ina yaiyo mpaka lero ikuoneka ngati yabwino ndi
yobvomerezeka munthawi zathu zino. Inayo ingafune kuonedwanso ndikusinthidwa apa ndi apo. Mbali yaikulu kwambiri ya dongosolo la momwe
tichitira mumpingo lingathe kusinthidwa koma ndikumapitirirabe kumvera ndikulemekezabe zomwe malemba amaphunzitsa.
Zofotokozera:
• Kukhala mozungulira gome ndikumalandira mgonero monga tichitira
pakudya chakudya.
• Zosakhala ndi woyendetsa ntchito kutsogolo kapena ulaliki wokonzedwa.
• Kuwernga malembo ambiri.
• Alaliki osiyanasiyana pa misonkhano yosiyana.
• Msonkhano kugawidwaq mtimagulu khumi ting’ono ting’ono.
• Msonkhano wotenga maola awiri.
• Mapemphero asanu kapena khumi.
• Aliyense kupita kutsogolo kukalandira mgonero.
• Kumangoimba ndi mau amodzi ofanana osagawa mmau anayi aja ngati kwayala.
• Kuyamba ndi mgonero ulaliki usayambe.
• Akazi kukhala kwaokha mosiyana ndi amuna.
• Kukumana kwa kumidzi.
Izi sikuti ndiye zobvomerezekazo, koma zikusonyeza zomwe zinayenera
kuchitidwa malingandi ndi malemba.
2) Tikanabvutika kwambiri polandira ndikupembedza potengera dongosolo la
mpingo woyamba uja, ngakhale posanena za mphatso zao za Mzimu Woyera:
• Analibe nyumba yawoyawo yopembedzera.
• Oyankhula ambiri pamsonkhano – aliyense yemwe anali ndi choyankhula.
• Aliyense yemwe anali ndi nyimbo yake
Umodzi 64
ankaimba osatinso zotokonzekera.
• Nthawi zambiri ankakweza manja mmwamba popemphera.
• Akazi ankabvala maduku, osangoti monga chipewa chabe.
• Kulibe kukonzekera ngakhale dongosolo lenileni.
• Kupembeza kwawo kumatenga nthawi yaitali kwambiri.
3) Akhristu ampingo woyamba uja nawonso akanabvutika kwambiri ndi miyambo yathu.
• Kutsiriza ikamafika 12 koloko.
• Zinthu zabwino, zamakono monga nyumba etc.
• Akazi osabvala maduku, obvala zobvala zionetsa mikono yawo.
• Amuna ndi akazi kukhala pamodzi (kumaiko ena)
• Nyimbo zoyimbidwa mokoma, ndinso mamvekedwe anayi munyimbo
monga mau onse aakulu, aang’ono, apakati ndi ena okometsera.
• Misonkhano yokhala ndi ndondomeko, yochepetsedwa mwina chifukwa
cha zina (?)
4) Mipingo yathu imene, yasintha zambiri mzaka zapitazi osazindikira kuti tasiya
malemba.
• Kusintha kuchokera ku Baibulo Lolembedwa m’chichewa chakale kupita
ku chichewa chamakono.
• Misonkhano ya achinyamata.
• Magulu ogwira ntchito zina.
• Kuyenderana pakati pa amayi.
• Madongosolo a mautumiki.
• Magulu apadera oyimba.
• Mautumiki a mapemphero apadera.
• Nkhani za mumpingo m’manyuzi.
• Kugwiritsa ntchito vidiyo ndi zithunzi zake.
• Kugwiritsa ntchito ndalama zampingo pogulira chakudya ndi mmisonkhano.
• Matimu a mpira a mpingo.
• Nyumba zochitira masewera olimbitsa thupi ndi zina za anthu abanja
lonse.
• Alaliki achigawo kapena pamalo.
• Misonkhano yokonzedweratu.
• Ubatizo wochitika mmadamu okonza osati ku mtsinje kapena dziwe.
• Kugwiritsa ntchito malaudi sipikala ochokera ku “misonkhano ina” mu
mpingo wa Khristu.
• Kuwawerengera ana nthano ya m’Baibulo nthawi yamapemphero a Lamulungu.
G. Miyambo ingathe kukhala ndi nzeru. Nthawi zina zimaonetsa kuphunzira ndi umulungu wa
atsogoleri anzeru, komabe miyamboyi ndi ya anthu basi.
H. Miyambo kawirikawiri imangothandiza kuti munthu adziwike mtundu wake. Kusintha
miyambo ndi zizolowezi sikulakwira Mulungu, komatu kwa ife kumaoneka ngati kusintha mpingo. Koma kusintha kwambiri kopanda tanthauzo kwa miyambo ndi zizolowezi
Umodzi 65
kungasokoneze mpingo ndikubweretsa kusamvana.
I. Bvutoli pamenepa sikukhala ndi miyambo, koma kuilola kuti ikhale monga mfumu
yotilamulira ndikumabvutika kusamala monga momwe tikanachita ndi mau a Mulungu.
J. Miyambo imasonkhanitsa ndipo imafuna kuti tidziilemekeza. Njira yekhayo yomwe ingatithandize kupewa kulowerera ndi kuyamba kulamuliriridwa ndikufooketsedwa ndi
miyambo ndi zizolowezi zimenezi, ndi younikanso miyambo yathuyo m’mibadwo yonse
pogwiritsa ntchito kuunika kwabwino kwa mau a Mulungu powerenga liwulo ngati kuti
sitinamveponso zamiyambo yathu. Izitu zimafuna kulimba mtima ndikupirira zedi. Miyambo
iyenera kumaunikidwa ndi malemba, osati malemba kumawaunika ndi miyambo.
Mau otsiriza: Tayesani kufufuza ndikuzindikira momwe maganizo anu amangiriridwa ku miyambo.
Tapezani nthawi yoti muganizire mozama zazinthu, ndipo mosadzinyenga nokha muonemo zinthu
zangokhala monga miyambo chabe. Izi zidzakuthandizani ndipo mudzaona kusiyana pamomwe
mudzayambire kubvomera momwe mungalandirire kusintha. Nditha kukhala ndi zinthu zanga zomwe
ziri zokondedwa ndipo ndimazitenga ngati zofunika kwambiri, komanso ndiyenera kulemekeza
ndikuonetsetsa kuti thupi la Ambuye likulandira zonse zofunikira zake ndiponso ndiyenera
kulemekeza zosowa ndi zofunikira poyamba za ena. Tiyenera “kumverana wina ndi mnzake
mkumvera Mulungu” – Aefeso 5:21.
--- B. Shelburne, West Tate Seminar, Brownfield, TX, Apr. 1992.
Mndandanda wa zothandiza zina pa zotsutsana.
Ngati mutapezana ndi wina wokutsutsani muntchito ya Mulungu, nawa Mafunso ena oti mudzifunse
nokha.
1. Kodi ine ndikuonjesera gawo liti ku makanganowa chifukwa cha kufooka kwanga, kupusa
kwanga, kusakhala ndi maganizo abwino kapena machimo?
2. Kodi kusayankha bwino kwanga kwaonjezera bwanji pakulimbanaku? Ndingathe
kudziletsa pamomwe ndichitira wina akandikwiyitsa.
3. Kodi yemwe akunditsutsayu walakwitsa komabw ali wokhulupirika, kapena ndiwochimwa
kwenikweni? Izi zimathandiza mayankhidwe anga.
4. Kodi ndikupemphera motsimikiza chifukwa cha wonditsutsayo ndinso kuti papezeke njira
ya chilungamo ndi yachiyero yothetsera bvutoli? Kodi ndayesapo kusala pamodzi ndi mapemphero? Kodi ndikufunsa nzefu, kudzichepetsa ndichizindikiritso cha zolakwa
zakumbali yanga? Chithandizo cha Mzimu Woyera.
5. Ngati pali kulakwirana, kodi ndapitapo kwa m’bale wangayo kapena mlongoyo momvera bwino malinga ndi dongosolo losanjidwa ndi Yesu mu Mateyu 18:15-20; 5:23-24?
6. Kodi ndapita ndi mtima wodekha (Agalatiya 6:1-2)? Kodi ndakonda mtendere wokwanira
kuti nditha kuchitadi dongosolo lopitalo mmalo modikira kuti koma winayo ndiye
andipeze?
7. Kodi ndayesetsa kusunga chinsinsi choti makanganowo asakhudze anthu ena? Izi
zimateteza umodzi wa mpingo ndi banja.
Umodzi 66
8. Kodi ndikuyesetsa kugonjetsa choipa ndi chabwino? (Aroma 12:21) kapena kodi
ndikubwezera choipa ndi choipa chinzake? Kodi ndalola kuti wotsutsana nayeyo anditsitse mpaka ndifike pakufanana ndi khalidwe lakelo?
9. Kodi ndakumbukira kuti kubvutika chifukwa chikhala ndi moyo wofanana ndi Yesu
ndicho chiphunzitso chachikulu chomwe ndiyenera kupereka?
10. Kodi ndiri ndimantha kuti ndikambirane zobvuta ndi wonditsutsayo? Mutha kukambirana
pa chirichonse, chingakhale chobvuta chotani, ngati muyankhulana munjira yoyenera.
Kodi ndabwera munjira zoti zimupangitsa woyambana nayeyo kudziteteza m’malo
mololera? Kodi ndikuoneka ngati ndifuna kumuputa?
11. Kodi ndafufuza njira zina zocchitira zomwe ndiyenera kuchita, zomwe woyambana nayeyo
angathe kubvomereza? Nthawi zonse njira imapezeka ngati tikondweretsedwa
ndikufufuzako.
12. Kodi ndikuyankhulayankhula za woyambana nayeyo ndi ena mmalo moyankhula kwa iye?
Izi zimangosonkhezera moto wa kulimbanako.
13. Kodi ndikuyesetsa kudandaulira pagawo lomwe wotsutsana nayeyo ndi ine tingagwirizane? Kodi ndikuyesetsa kukonza ubale wathu?
14. Kodi ndakhala ndi nthawi yophunzira momwe Yesu pamodzi ndi ophunzira ake
anamchitira pamene panabuka kusamvana?
15. Kodi ndikuweruza zolinga za mkati a wotsutsana nayeyo pamene sindingathe kuona za mumtima kapena kudziwa zonse zachitika? (Yohane 7:24; Mateyu 7:1-5; Yakobo 2:12,13).
Kodi ndingakondwere ndi muyezo womwewo wachiweruzo utaperekedwa kwa ine?
16. Kodi ndayesa kupempha malangizo ndi uphungu kuchokera kwa achikulire, anzeru ndi
odalilika?
17. Kodi ndakhala nayo nthawi yoganizira ngatidi ndikubvutika chifukwa cha ine mwini
kapena chifukwa cha Mulungu? Kumbukirani kuti ife sitimuona Yesu akubvutika
chifukwa cha iye mwini, popeza anali atadzikhutula nali wofafa ku thupi. Ifenso
tikufunsidwa kuchita chimodzimodzi.
18. Ngati wotsutsana nayeyo salola kusintha, kodi ndiri wokonzeka kutula nkhani yonseyi kwa
Mulungu mwini? 1 Yohane 4:4; 1 Petro 2:23; Masalmo 23:5. Kodi ndiri wokonzeka
kusiyira Mulungu kuti abwezere zonse? Aroma 12:19. Kodi ndiri ndi mzimu wokhululuka, pozindikira kuti nanenso ndilakalaka kukhululukidwa – Mateyu 6:12,14,15.
19. Ngati ndichoka ndikusiya malo kapena chinthu chifukwa chakulimbana ndikutsutsana,
kodi ndayesetsa kuchita mbali yanga yosiya ubale uli wosaonongeka?
Zochokera ku maphunziro okonzedwa ndi a Shelburne otchedwa “Moyo ndi ntchito ya Mlaliki”
Ndondomeko ya Moyo wa Mpingo
Mipingo ina imalowa pansi chifukwa cha chiwerengero cha anthu ndi mabvuto ndi maganizo.
Umodzi 67
1. Kodi tikumuika Khristu ndi mtanda monga potsamira penipeni pa uthenga wathu? 1 Akorinto
2:2.
2. Kodi abusa akuwetadi mwauzimu, kapena angopanga maganizo ongoti bola ziziyenda malinga ndikukonda kwawo? 1 Petro 5:1-4; Yohane 10:1-18; Ahebri 13:17.
3. Kodi alaliki sanasiyitsidwe ntchito yawo yeniyeni yolalika malembo ku mizimu yosowa?
Machitidwe 6:1-6.
4. Kodi alaliki ndi atsogoleri ndi zitsa zokwanira za zomwe alalika? 1 Timoteo 3:1-13; 4:12.
5. Kodi tikukopa anthu kulowa mumpingo ndi mau a Mulungu, kapena ndi ntchito zina zathupi
zosangalatsa thupi ndi zina zadziko? 1 Akorinto 3:10-13.
6. Kodi timawakonda osochera kotero kuti titha kudzichepetsa molingana ndi momwe angalolere
Mulungu kuti tikawafikire, kapena timayembekezera kuti iwo ndiwo ayenera kutsatira zomwe
ife tifuna basi? 1 Akorinto 9:19-23.
7. Kodi timalimbika posamala otembenuka mwatsopano ndi anthu omwe anagwa naukanso,
kapena timangowasiya akumangodzigwera okha? Mateyu 28:19-20; 1 Atesalonika 5:14; Aroma 15:1; Aefeso 4:11-=16; Ahebri 5:11; 6:3.
8. Kodi tikugwiritsa ntchito mphatso ndi maluso a azimayi mokwanira ndi mogwirizana ndi
malemba? Aroma 16:1-3,6,12; Afilipi 4:2,3; 1 Timoteo5:3-16.
9. Kodi tiri ndi chidwi chofuna kuthandiza anthu “kupachika umunthu wao wakale” ndikukhala obadwa mwatsopano ngati ife kuti abatizidwe? Kodi tikuthandiza anthu, kuphatikizapo
atsogoleri kuti athane ndi kudzitukumula ndi kudzikondweretsa okha komwe kumagawanitsa
mipingo ndi mabanja? Aroma 6:1-14; 7:7-25; 8:1-17; Aefeso 4:22-24; Agalatiya 5:19-23.
10. Kodi timalimbikira chiphunzitso cha m’Chipangano Chatsopano pa zakusinthika kwa mkati
monganso momwe tichitira ndi chiphunzitso cha “kutsatira dongosolo labwino?” 2 Timoteo
3:5; Mateyu 18:1-3; 2 Akorinto 3:6.
11. Kodi tikati kumvera timachit mogwirizana ndi uphungu wa Mulungu watunthu kapena
chifuniro cha Mulungu, kapena timangochita pongotsata ziphunzitso zotikondweretsa –
Machitidwe 20:27; Mateyu 23:23,24.
12. Kodi timawakonda otayika koti mpaka tingalolere kusiya miyambo yathu ina ngati
ingatisokoneze ndikulepheretsa kuti tikawafikire? Kodi timasokoneza miyambo ndi zizolowezi za chikhalidwe chathu ndi zofunikira za
malemba? Mateyu 15:1-9.
13. Kodi Akhristu ena onse omwe tisonkhana nawo amasamala kwambiri mizimu ya otayika koposa zowakondweretsa iwo eni ndi zosawakondweretsa? Aroma 15:1-3.
14. Kodi pali maubale oipa mumpingo kapena pakati pa atsogoleri omwe chifukwa
chakudzitukumula sitingathe kuwathetsa, ngakhale akulepheretsa ntchito ya mpingo? Kodi
iripo njira yomwe mukupanga pakali pano yoti muthandize kukonza ndi kuchotsa kuwawirana
mitima komwe kwakhalapo kuyambira kale mumpingomo komwe kukufoketsa mpingo?
Mateyu 18:15; 5:23,24; Afilipi 2:14-16.
Umodzi 68
15. Kodi pali machimo ena omwe angobisidwa mmitima ya Akhristu kapena atsogoleri omwe
akulepheretsa kuti chisomo cha Mulungu chichite nawo mpingo ndikuthandiza? Yoswa 7; 2 Akorinto 6:14-7:1; 2 Timoteo 2:19-22.
16. Kodi atsogoleri akupitirizabe kuphunzira ndikukula kuti athe kutsogolera osati kuti mpingo
uwapitrire? 2 Timoteo 2:15; 2 Petro 3:18; Kodi alipo atsogoleri ena omwe akulephera kugwira ntchito chifukwa cha mantha? Mateyu 25:14-30; Chibvumbulutso 21:8.
17. Kodi kusala pamodzi ndi mapemphero kumakonzekera njira zabwino zopanga maganizo ndi
machitidwe abwino? Machitidwe 13:1-3; 14:23.
18. Kodi tikuphunzitsa mnjira yoti imapherezera mkusinthika kwa miyoyo? Kodi anthu
akuthandizidwa kutuluka muuchimo ndi moyo wachionongeko? Luka 4:18,19; Aroma 12:1,2.
(miyoyo yosinthika imakhala ndichikoka)
19. Kodi utumiki wathu wophunzitsa umalingana bwanji ndi utumiki wa mapemphero owirikiza?
Kodi kapena tikuyeserera kuchita ndi utumiki ulionse popanda unzake? Machitidwe 6:4; 13:3.
Maganizo khumi ndi atatu (13) omwe Thomas Campbell analemba ndi kunena poyera.
Ganizo 1: Kuti mpingo wa Khristu pano pa dziko lapansi mofunikira, mwacholinga komanso
mwalamulo langwirizano ndi umodzi; wokhala ndi iwo onse opezeka ku malo konse omwe chikhulupiriro chawo chimatsamira pa Khristu ndikumumvera mu zonse molingana ndi malemba,
ndikuonetsera zomwezonso pa khalidwe lawo lodziletsa, osati kwa wina aliyenseyo; pakuti siwina aliyenseyo amene angatchulidwe kuti ndi Mkhristu woona ndi wolongosoka.
2. KutiKuti ngakhale Mpingo wa Khristu pa dzikoli ufunikira kukhalabe pakati pa anthu
osiyanasiyana, mosiyana ndi wina, koma sipayenera kukhala kusiyananso ndi magawano
pakati pake. Ayenera kumalandirana wina ndi mnzake monganso momwe Yesu Khristu
wawalandirira ku ulemerero wa Mulungu. Choncho ndicholinga chimenechi onse anayenera
kumayendera lamulo limodzi, kusamalira ndikumayankhula chinthu chimodzi; ndi kukhalanso
olumikizidwa pamodzi mu mtima umodzi, ndinso muchiweruzo chimodzi.
3. Kuti izi zitgheke, pasakhale chirichonse chomwe chikidwe ndikukakamiza Akhristu monga
mfundo zolembedwa zoti Akhristu azizilemekeza monga chikhulupiriro chawo, kapena
chomwe ayener kulamulidwqa nacho mona malamulo a mgonero, koma zokhazo zomwe
zaphunzitsidwa molongosoledwa bwino ndikuikidwa mwa iwo kuchokera mmawu a Mulungu.
Zosaloleranso china chirichonse, kutengedwa ngati lamulo la Mzimu Woyera, mu malamulo
oyendetsera mpingo wawo ndi ntchito zina zapakati pawo, koma zokhazo zomwe
zafotokozedwsa bwino ndi kuperekedwa kwa iwo mwa ulamuliro wa Ambuyathu Yesu Khristu pamodzi ndi Atumwi ake pa Mpingo wa m’Chipangano Chatsopano; kaya pa
kulongosolera kaya pakutsimikizira pa zomwe zinachitika kale.
4. Kuti ngakhale malemba am’Chipangano Chakale ndi Chatsopano ndi ogwirizana mosalekana, pamodzi ndikupanga bvumbulutso limodzi langwiro la chifuniro cha umulungu, lomangirira
ndikupulumutsa mpingo, choncho chifukwa chachimenechi sungagawanitsidwe; koma pa za chomwe chiri cha pacholinga chawo cha panthawi yomweyo, Chipangano Chatsopano chiri
changwiro monga Bukhu la malamulo a chipembedzo, khalidwe labwino, ndi kayendetsedwe
kampingo wa Chipangano Chatsopano, ndinso monga lamulo langwiro lapakagwiridwe
kantchito zina za anthu ake, monganso popeza Chipangano Chakale chinali mapembedzedwe,
kusunga khalidwe labwino, ndiponso kayendetsedwe kabwino ka ntchito za mpingo
waChipangano Chakale ndi ntchito zinanso zosankhikia za anthu ake.
Umodzi 69
5. Kuti ndikulemekeza malamulo ndi zoikika za Ambuye wathu Yesu Khristu, pamene malembo
akhala chete pa za nthawi kapena machitidwe, ngati zoterozo ziripo, palibe ulamuliro wamunthu womwe uli ndi mphamvu yoikapo maganizo ake, ndicholinga chofuna kukwaniritsa
zooneka zoperewerazo podzipangira malamulo ampingo; kapena pasapezeke kuwaikira
Akhristu madongosolo ena munkhani ngati zimenezi, koma iwo ayenera kugwiritsa ntchito malamulo ndi zoikika za Ambuye Yesu monga momwe zingagwirizanire mwachidziwikire ndi
kuyankha cholinga cha mpingo wawo. Munthu alibe mwai waukulu woika ulamulo ndi
zoikika zake mu mpingo, zomwe Ambuyathu Yesu Khristu sanaike. Palibe chirichonse
chomwe chiyenera kulandiridwa mu chikhulupiriro kapena chipembedzo champingo, kapena
kupangidwa mona mfundo yoyanjanitsa pakati pa Akhristu, chomwe sichinakhalapo munthawi
ya Chipangano Chatsopano.
6. Kuti ngakhale zoganizira ndi zochotsedwa ku malemba, ngati ziganiziridwa mwabwino,
zingathe kutengedwa monga chiphunzitso cha malembo oyera a Mulungu, koma pamenepa
ndiye kuti sakumangirika ku chikumbumtima cha Akhristu kopitirira momwe amalandirira
choonadicho, ndikumaona ngati ndimmwne ziyenera kukhalira malinga ndi zomwe
akuwerengazo; popeza chikhulupiriro chawo sichiyenera kuima pa nzeru ya anthu, koma
mumphamvu ndi ulemerero wa Mulungu. Choncho, kuchotsera koteroko kusapangidwe
kukhala monga lamulo loyanjanitsira, koma akhalapo zonse zoyeretsa, kukonza chimangiriro cha mpingo. Choncho apa nchachidziwikire kuti kuchotserako zina za mmalemba kotereku,
ndikuganizira ndikuikirira maganizo ena omaoneka ngati oona sikuyenera kuchitika munkhani zonse zampingo.
7. Kuti ngakhale ziphunzitso za choonadi cha umulungu, ndi maumboni odzitetezera ku
zolakwikazi, akhale oti mwina tingataye nawo moyo, ndipo pamene ali okwanira ndi oyenera zolinga zimenezi, ndiye kuti ziri bwino; komabe, popeza zambiri za zimenezi zichitika
m’maganizo aumunthu, ndiponso zambiri zake zichokera ku zoganizira za munthu, siziyenera
kutengedwa ngati malamulo oyendetsera Chiyanjano cha Akhristu; pokhapokhapo tiganizira
zomwe ziri zotsutsana ndi zoonazo, zakuti palibe yemwe ali ndi ufulu pa zachiyanjano cha
mpingo, koma zokhazo zokhala ndi chiweruzo chokhala ndi maganizo omveka, kapena afikira
pa kudziwitsitsa za ziphunzitso; pamene mpingo unadziwa ndikukhala nazo kuyambira kale
lomwe, ndipo udzakhala nazo, zokhala ndi ana, ang’ono ndi achinyamata pamodzi ndi
abambo.
8. Kuti monga kuli kosafunikira kuti anthu ayenera kudziwa kapena kumvetsa bwino zoonadi za
umulungu zonse zobvumbulutsidwa kuti ziwayeneretse kukhala ndi udindo mumpingo;
pachifukwa chomwechi, asabvutike ndikukhala ndi luso la ntchito mwapadera koposa momwe
angadziwire; koma kuti posiyana ndi zimenezi, mwakuzindikira za moyo wao mwauzimu,
kusochera ndikuonongeka kwa moyo wao mwa chikhalidwe ndi zochita, ndinso za njira ya chipulumutso mwa Yesu Khristu, kuphatikizira pa luso la pa chikhulupiriro chawo ndi
kumvera iye mu zinthu zonse, molingana ndi mau ake, ndizomwe ziri zofunikira kwa iwo kuwayenereza kulandiridwa ku Mpingo wake.
9. Kuti osne amalandira luso limeneli chifukwa cha chisomo, ndipo amachitira umboni zonsezi
kudzera momwe achitira ndi khalidwe lawo ndi zopsetsa mtima zawo, aonane wina ndi mnzake oyeretsedwa amtengo wapatali a Mulungu, akondane wina ndi mnzake ngati abale,
ana am’banja limodzi ndi atate mmodzi, akachisi a mtima umodzi, anthu a mtchupi limodzi,
achisomo chimodzi, ziwalo za chikondi chimodzi cha umulungu, ogulidwa ndi dipo lamtengo
umodzi, ndiponso oyembekezera mwaumodzi kulowa cholowa chimodzi. Choncho omwe
Mulungu wawamanga pamodzi munthu wina asyeserere kuwalekanitsa.
Umodzi 70
Kuti malekano pakati pa Akhristu ndichinthu chipitsitsa, chodzala ndi machimo ena
ambirimbiri. Malekano ndi chinthu chotsutsana ndi Chikhristu, popeza chimaononga umodi wooneka wa thupi laKhristu; ngati kuti iye anagawanika, kuchotsa ndikudula magawo ena
athupi lake. Malekano ndi kutsutsana ndi malemba, monga amaletsedwa ndi ulamuliro wa
Mulungu, kuphwanya lamulo lake. Malekano siumunthu, popeza amautsa Akhristu kuti azidzudzulana, adzizondana kapena kudana, omwe ali omangiriridwa ku lamulo lalikulu,
loposa, lokondana wina ndi mnzake ngati abale, makamaka monga momwe Khristunso
anawakondera. Mwachidule, malekano ndi chipatso cha kusokonekera maganizo ndinso cha
ntchito iriyonse yachoipa.
10. Kuti kunyalanyaza ndikusiyako zina za bvumbulutso la choonadi cha Mulungu, ndinso
kungoonjezera ulamuliro wina wopangitsa kuti maganizo a anthu ndizopeka zina kukhala njira
yoyanjanitsira, poziika mu malamulo, chikhulupiriro, kapena chipembedzo cha mpingo, ziri,
komanso zakhala zodziwika zomwe zayambitsa ndikubweretsa, kuyambitsa zonse
zachinyengo ndinso kugawanikana zomwe sizinachitikeponso mu Mpingo wa Mulungu.
11. Kuti zonse zomwe ndi zotumikira kwambiri ku ungwiro woposa ndi zoyeretsedwa za mpingo
pano pa dziko ziri, choyamba, kuti palibe womwe ukalandiridwe ngati woyanjana nafe, koma
monga wokhala ndi muyezo wa chidziwitso cha malemba chomwe chanenedwa pamwambapa, ngakhale, chachiwiri, kuti uliwonse ukhale pachiyanjano chake kopotirira koposa ngakhale
zoona za luso lake pa momwe achitira ndi zopsetsa mtima ndi khalidwe lake. Chachitatu, kuti oyang’anira ake okhala nazo zoyeneretsa monga mwa malemba, ogwiritsa ntchito mfundo
zokhazo zachikhulupiriro ndi chiyero zobvumbulutsidwa ndikuikidwa mmau a Mulungu osati zina ziri zonsezo zopangidwa ndi munthu. Potsiriza kuti mmagwiridwe ao onse a ntchito zawo
amakhala pafupi ndikusunga zonse zoikika ndi umulungu, chitatha chitsanzo cha mpingo wakalekale, kuonetseredwa m’Chipangano Chatsopano; popanda zoonjezera zina ziri zonse za
maganizo a munthu kapena zongotulukiridwa ndikuikidwa ndi anthu.
12. Potsiriza. Ngati pali zina zochitika malingana ndi nthawi zofunikira kuti zithandizane pochita
ndi zoikikika za umulungu zisapezeke mmasamba a bvumbulutso la Mulungu, koma, zokhazo
zomwe ziri zofunikira pachifukwa chimenechi ziikidwa pansi pa gulu za anthu, popanda
kukometsera kwa mtundu wina uliwonse kuti zioneke ngati gwero lake ndilopatulika, kotero
kuti kusinthika kulikonse komwe kungachitike kapena kusiyana pa masungidwe a zinthu
zimenezi kusabweretse kulimbana kapena kugawanikana mumpingo.
Translated from English by Rhodes Maluwa. © by G.B. Shelburne, III (except for any graphics and scripture quotations). May be reproduced for non-profit, non-publishing instructional purposes provided this entire copyright notice is included and document content is not altered. South Houston Bible
Institute, PO Box 891246, Houston, TX 77289-1246 USA, tel. 281-990-8899, Email [email protected], web site <www.shbi.org>. Scriptures, unless
othewise noted, are taken from theBukhu Loyera, lopangidwa ndi The Bible Society of Malawi, P.O. Box 740, Blantyre, Malawi, copyright @ 1999.